‘Bingu azitsanzika’

Katswiri pa ndale yemwe ndi mphunzitsi wa phunziro la ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Joseph Chunga wati machokedwe a mtsogoleri wa dziko lino, Bingu wa Mutharika posauza anthu ake kungapereke mafunso ambiri kwa Amalawi.

Chunga amalankhula izi m’sabatayi pomwe kudadziwika kuti Mutharika adali m’dziko la Nigeria komwe adaonedwa akulandiridwa ndi mtsogoleri wa dzikolo, Goodluck Jonathan.

Mutharika adachoka m’dziko muno Lachiwiri koma aneneri aboma adakana kuti Mutharika sadachoke ndipo ali m’dziko muno.

Lachitatu, Mutharika adaoneka m’dzikolo zomwe zimasemphana ndi zomwe aneneri abomawa adauza atolankhani kuti Mutharika alipo.

Koma Chunga akuti izi zingapereke mafunso m’mitu mwa anthu chifukwa anthu amafuna kudziwa kuti bambo wawo wapita kuti.

“Mutha kuona kuti aka sikoyamba, komabe m’malamulo adziko lino mulibe lamulo lomwe limanena bwinobwino momwe ziyenera kukhalira.

“Komabe, ana amafuna kudziwa komwe bambo alowera,” watero Chunga.

Share This Post