Nkhani

‘Kukonza misewu kukuyenda’

Listen to this article

Pali chiyembekezo kuti ntchito za mtengatenga za m’dziko muno zingapite patsogolo chifukwa ntchito zikuluzikulu za chitutuko cha misewu zoposa zisanu zimalizika chaka chino chisanathe.

Poyankhula ndi Tamvani sabata yatha, mneneri wa bungwe loyang’anira za misewu m’dziko muno la National Roads Authority (NRA), Portia Kajanga, anavomereza kuti ntchito zomanga misewu’yi zakhalitsa kuposa mmene adayembekezera.

“Misewu yatsopano monga Karonga-Chitipa, Ekwendeni-Ezondweni ku chigawo cha kumpoto; Mchinji-Kawere, komanso kukonzanso kwa msewu wa Lilongwe-Nsipe ngakhalenso Msulira-Nkhotakota m’chigawo chapakati zitha pofika mwezi wa Disembala chaka chino.

“Izi zikuphatikizanso mlatho wa South Rukuru ku Rumphi. Msewu wa Mchinji-Kawere okha umene ukuyembekeza kutha mu Julaye,” anatero Kajanga

Komabe mneneriyu adati pa zilinganizo zonsezi, ndi ntchito yomanga mlatho wa South Rukuru yokha imene imalizike munthawi yoikika kuyambira pa chiyambi.

Iye adati misewu iwiri yatsopano ya Thyolo-Thekerani-Muona komanso wa Limbe-Zomba ikuyembekezeka kuyambika chaka chino.

“Tikadakhala titamaliza miseuyi koma vuto la kusowa kwa mafuta m’dziko muno ndi limene lachedwetsa ntchitozi. inagumula mwina ndi mwina,” adatero Kajanga.

Related Articles

Back to top button
Translate »