Nkhani

‘Kusowa kwa mpikisano n’kwachabe’

Listen to this article

Pali mantha kuti zipani za m’dziko muno zingayoyoke ngati makatani ngati mipando yonona yachipani monga wa pulezidenti ndi wachiwiri wake ipitirire kukhala yongotola popanda wopikisana naye ku misonkhano yaikulu ya zipani.

Izi zaunikidwa ndi otsogolera zitukuko kumidzi ena ndi katswiri pandale potsatira zochitika kumsonkhano waukulu wa chipani cha People’s Party (PP) komwe mpando wa pulezidenti ndi wachiwiri wake kuchigawo cha kumpoto padalibe kupikisana.

Kusapezeka opikisana m’mipandoyo kudapereka danga kuti mwini chipanichi, yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adutse popanda omugwedeza.

Naye wachiwiri kwa Banda, Khumbo Kachali adadutsa moyera.

M’boma lomwe langopita kumene la DPP, mwini chipanicho komanso yemwe adaali pulezidenti, Bingu wa Mutharika samachititsa msonkhano waukuluwu n’komwe, m’malo mwake iye amangoloza anthu m’maudindo a m’chipanicho.

Chitsanzo, Mutharika adaloza Hetherwick Ntaba kukhala mneneri wachipani.

Mtsogoleri wakale yemwenso adali pulezidenti m’chipani cha UDF, Bakili Muluzi atangotula udindo kwa Friday Jumbe kudali kukokanakokana mpaka pano pomwe chipanichi chagawikana.

Zitadziwika kuti kukhala msonkhano waukulu kuchipani cha PP, anthu ena monga mkulu wina wa bizinesi, Caesar Fatch, adabwera poyera kuti adzapikisana ndi Banda.

Koma poyandikira chisankhocho, Fatch adalengeza kuti wazisiya, ati adzayeseranso kutsogoloku.

Malinga ndi operekera ndemangawa, izi ndizo zikuchititsa kuti zipani za m’dziko muno zizisokonekera pomwe pulezidenti wachipanicho wachoka paudindo chifukwa ofuna mpandowo amakhala akukokana, ena n’kumathiothoka m’chipani.

Katswiri wa pa zandale, Blessings Chinsinga wati zipanizi zitamakhala ndi msonkhanowu n’kupezekanso olimbirana nawo m’maudindo onse, achipani si bwezi mavuto omwe adachitika ku UDF ndi DPP atachitika.

“Izi si zachilendo m’dziko; ngakhale m’maiko akunja mavutowa alipo. Koma mathero a zonse, chipani chimatha chifukwa anthu amayamba kukokana pomwe pulezidentiyo wachoka pampando.

“Ndibwino mipandoyi idziphangiridwa chifukwa pomwe pulezidenti wachoka, amene adayamba kupikisana naye ndiwo amakhala patsogolo,” adatero Chinsinga.

Makiyi Matukuta, mkulu wa bungwe la Malawi Carer ku Mayani m’boma la Dedza, wati anthu kumeneko adali odabwa kumva kuti Banda wadutsa pampando wa pulezidenti popanda opikisana naye.

“Padzikhala kupikisana; anthu amakhala ndi chidwi kumva zomwe opikisanawo akonza. Zateremu ndiye kuti ufune usafune mtsogoleri wanu amakhala yemwe wadutsayo.

“Izi zimapha chidwi cha anthu ena omwe amafuna adzasankhe mtsogoleri yemwe amukonda,” adatero Matukuta.

Related Articles

Back to top button
Translate »