Nkhani

Abusa chepetsani tsankho

Ngakhale ambiri amati padziko lapansi palibe chilungamo, anthufe timayembekeza kuti kumpingo kokha tikapezako kachilungamo popeza uku ndi kumene ambiri timaphunzirako za ungwiro wa Mulungu.

Komatu ngakhale mipingo imakhala patsogolo kuphunzitsa za kufanana kwa anthu pamaso pa Mulungu, m’mipingo momwemo mumachitikanso tsankho lodabwitsa.

Tikaonetsetsa, tsankholi limabadwa kuchokera ku ndalama, kotero kuti opeza bwino, omwe kawirikawiri amapereka mochulukirapo kumpingo, amapatsidwa chidwi chambiri kulekana ndi akampopangolo.

Kagawidwe ka maudindo m’mipingo yambiri kamaona m’thumba la munthu, pamine si onse ochita bwino omwe ali ndi nzeru zoyendetsera mpingo.

Ena mwa iwo amakhalanso ndi zofooka zoti zikhonza kubwenzeretsa mpingo m’mbuyo.

Masiku a uneneri ano, abusa monse aliri kunenera zabwino kwa olemera, pomwe osauka ena zaka zikupita sadamvepo mawu a uneneri.

Ndikudziwa uneneri umachoka kwa Mulungu koma kodi Mulungu angamangoona zopsinja za ochita bwino kuiwala ana ake ena osaukawa? Zimakhala bwanji pamenepa?

Akachimwa wochita bwino mumpingo, kudzudzula kwake kumavutirapo pomwe akapunthabuye saati aimitsidwa liti mumpingo akalakwitsa.

Akagonekedwa m’chipatala olemera, abusa amachita ngati agone kunsi kwa bedi kupemphelera wodwalayo, koma akadwala osauka abusa salabadira n’komwe.

Pakagwa zovuta pakhomo pa wochita bwino, kathamangidwe ka abusa kamasiyana ndithu ndi m’mene achitira zikamuonekera mphawi.

Ngakhale chidwi chimene anthu amalandira kumpingo chimasiyana. Abusa ambiri amaonetsa chidwi kwa anthu omwe atsika galimoto.

Ndiponi pamakhala anthu ena omwe amayenda mtunda wautali sabata ndi sabata kusaka Yehova. Amakhala opsinjika ndi umphawi ndi mavuto ena koma chifukwa akuoneka otuwa, sapatsidwa chidwi ndi abusa kapena utsogoleri wampingo.

Anthu akapsinjika ndi zothodwa zosiyanasiyana amaona ngati kothawira ndi kumpingo, koma ngati mipingo ikulamuliridwa ndi ndalama, anthu athawira kuti?

Komatu pokhapokha ntchito za abusa zisonyenze chilungamo ndi chikondi cha Mulungu, kulalikira kwawo kukhonza kukhala pachabe chifukwatu anthu amaona machitidwe a mtsogoleri.

Email: rtheu@yahoo.com

Related Articles

Back to top button