Abwatika bwalo, Polisi ku mangochi

Fisi adakana msatsi. Mayi yemwe adauza abale kuti mwamuna wake amafuna kugulitsa mwana wawo wa chialubino wasintha Chichewa.

Vanessa Manyowa wauza bwalo la milandu ku Mangochi kuti zomwe adanenazo zidali zopeka chifukwa panthawiyo n’kuti atayambana ndi mwamuna wake pa nkhani za kumunda.

Kadadzera: N’zokhumudwitsa

Mayiyo adabereka mwanayo wa chialubino asadakwatiwe ndi mwamuna wake watsopanoyu. Padakali pano mwanayo ali ndi zaka 14.

Nkhaniyo idachitika mwezi watha pamene Manyowa adauza achimwene ake kuti mwamuna wake, Nick Adams, wa zaka 38 amafuna kugulitsa mwanayo.

Achimwenewo adatengera nkhaniyo ku polisi ya Mangochi moti Adams adamangidwa ndi mlandu woganiziridwa kugulitsa mwana wa chialubino.

Lachinayi sabata yatha nkhaniyo adaitengera ku khoti la m’bomalo komwe Manyowa adasintha Chichewa.

Manyowa adauza bwalolo kuti adapeka nkhaniyo atayambana ndi mwamuna wakeyo chifukwa adamukaniza kutengapo gawo lake la chimanga ndi mtedza womwe akolola.

“Ndazindikira kuti ndidalakwitsa kwambiri. Mwamuna wanga sadanenepo zoti akufuna kugulitsa mwana wathu,” Manyowa adauza bwalo.

Izitu zidachititsa Manyowa ndi achimwene ake apemphe bwalolo kuti mlanduwo utsekedwe.

Woweruza mlanduwo, Joshua Nkhono adadzudzula Manyowa popekera mwamuna wake nkhani.

Nkhono adati nkhani zokhudza anthu achialubino n’zovuta choncho mayiyo adalakwitsa.

Apa woweruzayo adathetsa mlanduwo, koma adanenetsa kuti bwalo lilanga aliyense wopeka nkhani zokhudza anthu achialubino.

Nawo apolisi ati ndiwokhumudwa kaamba koti Manyowa adawapusitsa.

Mneneri wa apolisi m’dziko muno James Kadadzera adati zomwe wachita Manyowa n’zobwezeretsa zinthu mmbuyo.

Kadadzera adati palibe chomwe apolisi angachite chifukwa mlandu watha.

Polankhulapo mtsogoleri wa bungwe la anthu oyimira anzawo pa milandu la Malawi Law Society (MLS) Burton Mhango adati Manyowa ali ndi ufulu wotseketsa mlandu.

Iye adati zimatengera kukula kwa mlanduwo, komanso umboni womwe ulipo.

“Pankhaniyi zikuonetsa kuti wodandaula yemwenso akadakhala mboni yaikulu ndi yemwe adafuna kuti mlanduwo utsekedwe, choncho ngakhale apolisi akadafuna kuti upitirire sizikadaphula kanthu chifukwa pakadakhala popanda mboni. Mlandu wopanda mboni umavuta,” adatero Mhango.

Koma Mhango adati zomwe wachita Manyowa zaika pachiopsezo moyo wa mwana wake chifukwa anthu akudziwa komwe akupezeka ndipo ena oyipa moyo akhoza kumuchita chipongwe.

Choncho Mhango adapempha aboma kuti apereke chitetezo chokwanira kwa mwanayo kuti ambanda asalowererepo.

Nkhaniyo yachitika mwana wina wa khungu la chialubino atasowa m’boma la Dedza ndipo bambo wake womupeza adauza bwalo la milandu ku Lilongwe kuti ndiwo adamugulitsa mwanayo. n

Share This Post