Chichewa

Agumula chiliza nkutengamo alubino

 

Adaikidwa m’manda pa 27 May m’chaka cha 2000. Koma zodabwitsa zachitika pa 17 October 2015 pamene anthu olusa agumula chiliza ndi kuthawa ndi mafupa.

Izi ndizo zachitika m’manda ena kwa Mkanda, T/A Kalolo m’boma la Lilongwe komwe anthu ena afukula maliro a alubino amene adaikidwa m’manda zaka 15 zapitazo.

Malinga ndi T/A Kalolo, mandawo adagonekapo John Mphoka yemwe adabadwa mu 1952 ndipo adamwalira pa 25 May 2000 ndi kuikidwa pa 27.

Malinga ndi Kalolo, malemuwo adali amtundu wa chi alubino, zomwe zikupereka maganizo kwa mfumuyi kuti alipo m’dera lawo amene akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

 

“Nanga inu munthu tidamuika zaka 15 zapitazo, ndiye ngati ndi alendo iwowo adziwa bwanji kuti pamenepa tidakwirirapo munthu wa chi alubino? Alipo konkuno amene akukhudzidwa ndi izi komabe tikufufuza,” Kalolo adatero Lachitatu.

Kalolo adati adazindikira kuti malemuwo abedwa Lolemba pamene m’mudzimo mudagwa thambo lakuda. Iye adati pamene adzukulu amati akakumbe nyumba yoti malemuwo akagone, ndi pamene adaona malodzawo.

“Pamene timafuna kukumbapo padayandikana ndi pomwe tidagoneka malemuwo. Ndiye mwambo wokumba udasokonekera kaye pamene tidathamangira kukadziwitsa apolisi,” adatero.

Pamalopo akuti padangotsala bulangete lokha koma bokosi lidali litawola kale. Apolisi atadzafukula akuti adapeza mafupa 22 ang’onoang’ono koma mafupa ena onse adatengedwa ndi achiwembuwo.

Mneneri wapolisi mumzinda wa Lilongwe Kingsley Dandaula adati nkhaniyo ndi yoona koma akuyenera alandire lipoti kuchokera kwa apolisi awo kuderalo.

“Tamvadi za nkhaniyi koma tikudikirabe apolisi kuderalo kuti atipatse zomwe apeza komanso kuti tidziwe momwe nkhaniyi ikuyendera,” adatero Dandaula.

Tili pa nkhani yonga iyi, chisoni chidagwira anthu am’mudzi mwa Nyundo kwa T/A Mwansambo m’boma la Nkhotakota pamene anthu ena adafukula mafupa pamene amalima m’munda.

Malinga ndi mneneri wapolisi ya Nkhotakota, Williams Kaponda, izi zidachitika mu esiteti ya Basal pamene anthu amalima m’mundamo pa 18 October.

“Anthuwo adali akugwira ntchito yolima m’mundamo, koma adadzidzimuka pamene adatema fupa. Podabwa, iwo adakauza bwana wawo amene adadzatidziwitsa,” adatero Kaponda.

Kaponda adati pamodzi ndi achipatala, adathamangira kumundako komwe adakapeza mafupawo ndipo zidatsimikizika kuti adali amunthu amene akumuganizira kuti adamwalira m’chaka cha pakati pa 2013 ndi 2014.

Koma mayi wina komweko akuti wazindikira zovala za malemuwo kuti adali amuna ake amene adasowa.

Related Articles

Back to top button