Chichewa

Agwidwa ‘ukapolo’ ku Ntchisi

Listen to this article

 

Madzi achita katondo kwa T/A Malenga m’boma la Ntchisi komwe Gulupu Malenga, Peku Wakuda ndi Munkana aletsa anthu a m’mudzi mwa Peku Woyera kukhala nawo pa zochitika zilizonse m’derali kuphatikizapo maliro, ukwati komanso kupita kumsika wawo waukulu potsatira mkangano wa malo.

Nkhaniyi ikuti mfumu yaing’ono Peku Woyera idawina mlandu wa malo womwe udaweruzidwa ndi magulupu atatuwa.

Malinga ndi Peku Woyera, magulupuwa ataona kuti zake zayera pamlanduwu, adanenetsa kuti amkhaulitsa.

Akuti asayende: Peku Woyera
Akuti asayende: Peku Woyera

“Chilango chake anthuwa adagwirizana kuti ine ndi anthu a m’mudzi mwanga tisiye kukhala nawo pazochitika mpaka kutiletsa kupita kukagula zinthu kumsika wathu waukulu ati kaamba koti ndidawina mlanduwo,” idatero mfumuyo, yomwe dzina lake la pamsonkho ndi Tisiyenji Daniyele.

Mfumuyo idati anthuwa adaletsedwanso kukhala nawo pamisonkhano ya chitukuko.

“Ngakhale ana awaletsa kutenga nawo mbali pazamasewero, pomwe amayi awathamangitsa kumabanki a m’mudzi ndi makalabu a ulimi. Moti ndikulankhula pano mayi wina adamulanda katundu wosiyanasiyana pakhomo yemwe adagula patauni yathu yaing’ono,” Peku Woyera adatero.

Iye adati pano anthuwa akudalira msika waukulu wa Ng’ombe womwe uli pamtunda wa pafupifupi makilomita asanu.

Peku Woyera adati ngakhale nkhaniyi idatengeredwa kubwalo la milandu komwe adalamulidwa kuti azisonkhana nawo ndi anzawo, magulupuwo akanitsitsa kuchotsa chiletsocho.

“Ndife akapolo m’mudzi mwathu momwe,” adatero Peku Woyera.

Polankhulapo, gulupu Malenga adavomereza za nkhaniyi ndipo adati chidatsitsa dzaye kuti magulupu atatuwo apereke chiletso chokhwimachi ndi mwano womwe Peku Woyera adachita ponyozera zisamani zomwe amalandira.

Malenga adati mwachikhalidwe chawo, zilango monga izi zimaperekedwa kwa anthu amwano ndi cholinga choti aphunzire mwambo.

Iye adati mudzi wonse walandira chilangochi chifukwa udakhudzidwa pamkangano wa malowo.

“Ife tikufuna kuti mfumuyi ndi anthu ake azibwera kubwalo akalandira chisamani, koma akapitiriza mwano sitingachitire mwina koma kuwalanga powasala,” Malenga adatero.

Koma Clement Zindondo, mmodzi wa akuluakulu a bungwe lomwe si laboma lomwe likutengapo gawo pa achinyamata ndi chitukuko la Ntchisi Organisation for Youth and Development (NOYD), adati anthuwa akusowekera thandizo kaamba koti magulupawa awaphwanyira ufulu wawo wosonkhana ndi anzawo.

“Ife tikudabwa kuti bwanji magulupuwa sakulemekeza chigamulo cha bwalo la milandu? Apatu sakusamala za malamulo oyendetsera dziko lino ndipo ndikhulupirira kuti akhoti achitapo kanthu nkaniyi ikawapezanso,” Zindondo adatero.

Chilangochi nchotchuka zedi m’boma la Ntchisi ndipo mafumu ambiri atengeredwako kubwalo la milandu la majisitireti la Ntchisi chifukwa chophwanyira anthu ufulu wosonkhana ndi anzawo.n

Related Articles

Back to top button