Chichewa

Akhutira ndi mitsutso ya atsogoleri andale

Listen to this article

Akatswiri andale akhutira ndi mitsutso ya atsogoleri omwe akudzaima nawo pa zisankho zapatatu zomwe zichitike m’dziko muno pa May 21 chaka chino.

Akatswiriwa ati mitsutsoyi ndi yofunika kwambiri pa ndale za demokalase kaamba koti imapereka mwayi kwa atsogoleri wotambasula mfundo zawo za chitukuko.

Mary Chilima, ndi phungu wa kummwera kwa boma la Mzimba, Agness Nyalonje, kucheza ku mtsutso wa atsogoleri ku Lilongwe

Iwo adati chokondweretsa n’choti anthu akupatsidwa mwayi wofunsa pamene sakumvetsetsa.

Mmodzi mwa akatswiriwa, Rafiq Hajat, adati mmbuyomu atsogoleri samakhala ndi mwayi wotambasula mfundo zawo kwa anthu omwe akufuna kuti adzawavotere.

“Ndikadakondwa mfundo zomwe atsogoleriwa akutulutsa zikadalembedwa ndi kusayinira kuti mtsogolo asadzakane akadzafunsidwa,” adatero Hajat.

Iye adapempha omwe akuyendetsa mitsutsoyo kuti azipereka nthawi yokwanira yoti anthu azifunsa atsogoleriwo.

Ngakhale anthu ambiri amasankha atsogoleri potengera zipani komanso zigawo zomwe amachokera, kadaulo wa ndale wa ku Chancellor College, Mustafa Hussein, adasindika kufunika kwa mitsutso.

 “Anthu ena amasankha atsogoleri potengera mfundo zomwe akutulutsa. Pachifukwa ichi, tiyeni tipititse patsogolo mitsutso ya atsogoleri,” adatero Hussein.

Koma kadauloyu adapempha omwe akuchititsa mitsutsoyo kuti samakondere mtsogoleri wina aliyense.

Ngakhale akatswiriwa akuti mitsutsi ikupindula, mfumu Mkumpha ya m’boma la Likoma ikuti palibe chaphindu chomwe ikuonapo.

“Atsogoleriwa akungotinamiza, akadzalowa m’boma sadzapanga zomwe akuuza anthu lero.

“Ndikadakhala ndi nambala zawo ndikadawaimbira n’kuwauza kuti asatimate phula m’maso,” adatero Mkumpha.

Godfrey Masawo akugwirizana ndi maganizo a mfumuyi.

Pothirirapo ndemanga patsamba la mchezo la Facebook la kampani yosindikiza nyuzipepala ya Nation Publications Limited (NPL), Masawo adati: “Zinazi ndi mkambakamwa chabe atsogoleriwa sadzakwanitsa.”

Koma alembi a zipani za ndale akuti ndi wokhutira ndi momwe mitsutsoyi ikuyendera.

Mlembi wa UTM, Patricia Kaliati, ndi wa Malawi Congress Party (MCP), Eisenhower Mkaka, adati zipani zawo zikudzigulitsa mokwanira kudzera m’mitsutsoyo.

“Tithokoze mabungwe omwe akonza mitsutsoyi chifukwa yatithandiza kuti tizigulitse kwa anthu ambiri. Ndikudziwa kuti mitsutsoyi iwonjezera mavoti omwe tipeze,” adatero Kaliati.

Komanso kafukufuku akuonetsa kuti anthu ambiri akutsatira mitsutsoyo pa masamba a michezo monga Facebook, Twitter ndi WhatsApp.

Mwachitsanzo, anthu 6 700 ndiwo amatsatira mtsutso wa atsogoleri a zipani za ndale womwe udachitika pa March 29 ku Bingu International Conference Centre (Bicc) mu mzinda wa Lilongwe. Pamene anthu okwana 2 200 adaonera mtsutso wa otsatira kwa atsogoleri a zipani womwe udachitika pa March 26 mu mzinda wa Mzuzu.

Related Articles

Back to top button
Translate »