Nkhani

Akufuna T/A Chekucheku achoke

Anthu okwiya Lolemba ndi Lachiwiri m’sabatayi adasonkhana paofesi ya DC wa boma la Neno komwe amapempha bwanamkubwayo kuti achotse T/A Chekucheku avulidwe ufumu wandodowu ati chifukwa wanyanya ziphuphu.

Mmodzi mwa anthuwa, Steve Donda, wa m’mudzi mwa Donda kwa T/A Chekucheku, akuti mfumuyi ikulanda minda ya anthu, ikumadyetsera ng’ombe zake m’minda mwa anthu komanso ikulonga mafumu posatsata ndondomeko ya ufumu wa Chingoni.

Koma mfumuyi yati zomwe akunena nzabodza ndipo iye satula pansi ufumu.

“Kusiya ufumu ndiye kuti ndamwalira, apo ayi sizitheka,” idatero mfumuyi.

Iyo idaonjeza: “Ndikukonza zowatengera anthuwa kukhoti. Pali milandu yambiri.”

Donda adati sasiya kupempha boma kuti lichotse mfumuyi. “Panopa tayamba kusonkhana kwa DC, sitikubwerera mmbuyo mpaka mfumuyi itachotsedwa,” adatero iye.

DC wa bomalo, Memory Kaleso Monpeiro, watsimikiza kuti ofesi yake yalandira madandaulowa ndipo wati Lolemba kudavuta moti sadagwire ntchito.

“Adatchinga ofesi yathu moti sitidagwire ntchito.Lero [Lachiwiri] bolani, angofika anthu oposera 100 pomwe dzulo [Lachiwiri] kudafika anthu oposa 200,” adatero Monpeiro.

Iye adati watumiza madandaulo a anthuwo ku ofesi ya pulezidenti poti ndiye ali ndi mphamvu zonse.

Related Articles

Back to top button