Chichewa

Akupha makwacha ndi zipatso

 

Chaima Banda, mlimi wa zipatso kwa Manondo, T/A Nkukula ku Lilongwe, akusimba lokoma ndi ulimi wake womwe wakhala akuchita kwa zaka 10 tsopano ndipo akuti kudzera muulimiwu iye wamanga nyumba yamakono, wagula galimoto ndi kuphunzitsa ana ake msukulu zapamwamba.

Chaima, yemwe adayamba ulimiwu ngati bizinesi ya nazale za mitengo ya zipatso zosiyanasiyana akuti tsopano ali ndi makasitomala ambiri omwe amadzagula zipatso ndi mbande za mitengo kumunda wake.

Adatswirika pa ulimi wa zipatso: Banda
Adatswirika pa ulimi wa zipatso: Banda

Mlimiyu adali ngati mlimi wina aliyense wongoyeserera koma kenako adakachita maphunziro a ulimi wa bizinesi ndi momwe angalimire zipatso kuti azipindula pantchito yomwe amagwira chaka chathunthu.

“Poyamba ndinkachita ulimi monga momwe amachitira alimi anzanga ndipo zinthu sizimasintha kwenikweni mpaka pomwe ndidakachita maphunziro a ulimi wa zipatso ngati bizinesi ya mbande ndi zipatso zenizenizo,” adatero Banda.

Iye adati zipatso zomwe amalima zimakhala zochita kukwatitsa ndipo mtengo wake umakhala wabwino kuyerekeza ndi zipatso zamakolo zomwe alimi ambiri amadalira komanso zimakhala ndi nyengo yake.

Kwa chaka chathunthu Banda amakhala akusamalira mbande zokwatitsakwatitsa ndipo ikafika nyengo yadzinja akuti amapha makwacha ambiri pogulitsa mbandezo kumabungwe ndi anthu ena ofuna kubzala mitengo paokha.

“Mwachitsanzo, mbande imodzi ya mtengo wa mango ndimagulitsa pamtengo wa K500 pomwe mapapaya ndi maolanje kapena malalanje ndi magwafa ndimachita K350. Chaka chino ndili ndi mbande 5 000 za mango, 3 000 mapapaya ndipo 2 000 magwafa zomwe ndayamba kale kugulitsa.

“Mabungwe ndiwo amandigula kwambiri moti ena amandipatsiratu chiwerengero cha mitengo ndi mitundu yake yomwe adzafune. Apa zikutanthauza kuti ndimayamba kulima ndi kudziwa kale msika ndi ndalama zomwe ndikuyembekezera,” adatero Banda.

Kudzera mu bizinesi ya ulimi wa zipatso womwewu, Banda adagula makina opopera madzi omwe amachitira mthirira nyengo yadzuwa.

Kupatula phindu lapakhomo, mlimiyu akuti kuchokera mu bizinesi ya ulimi wa zipatso amapeza zipangizo zaulimi wina monga chimanga ndi mbewu zina zomwe poyamba amazipeza akatenga ngongole kumabungwe ndipo phindu lake samaliona bwinobwino. n

Related Articles

Back to top button