Chichewa

Akwizinga oganiziridwa kuba chimanga

Mudali fumbi m’mudzi mwa Kamzingeni kwa Senior Chief Kwataine m’boma la Ntcheu Lachinayi sabata yatha pamene anthu adagwira anyamata awiri powaganizira kuti akukolola chimanga cha anthu kumeneko.

Udali mmawa pamene bambo wotchedwa Gannet Muluzi wa m’mudzimo adavumbulutsa anyamata awiri ndi kuwakokera kubwalo la mfumu.

Awiriwo adawathira zingwe
Awiriwo adawathira zingwe

Muluzi adauza Msangulutso kuti m’mudzimo komanso midzi yoyandikira alimi akulira pamene chimanga chikubedwa.

“Ndakhala ndikusakasaka ndiye lero ndawapeza ndekha. Amenewa aona zakuda. Tizikhalira kudandaula chifukwa cha anthu akuba? Sitilola,” adatero Muluzi uko gulu la anthu likululutira zomwe iye amalankhula.

Pamene Msangulutso umachoka m’mudzimo, nkuti oganiziridwawo atawathira zingwe kudikira kuti achite nawo.

 

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.