Chichewa

‘Amayi oyembekezera akulipira k10 000’

Listen to this article

Kusamvana kwabuka pachipatala cha chaching’ono cha Chikangawa m’boma la Mzimba pamene amayi oyembekezera akulipiritsidwa K10 000 pokabereka.

Amayiwo omwe auza Msangulutso ati ndi odabwa kuti mwana akangobadwa, achipatala akumalamula kholo lake kuti lilipire K10 000.

Amayi oyembekezera akulipira K10 000 ku Chikangawa

“Kulibe komwe tingathawire, chipatala chathu ndi chimwechi, sitikudziwa ngati boma lakhazikitsa malamulo woti tiyambe kulipira m’zipatala tikakabereka. Kudabwitsa kwake sakumatipatsa malisiti tikabereka,” adatero mayi wina amene adakana kutchulidwa.

Koma mkulu woona za umoyo m’boma la Mzimba, Lumbani Munthali adavomera kuti amayi akumalipira koma izi zikuchitika kutsatira malamulo amene anthu ozungulira chipatalacho adagwirizana.

Iye adati anthuwo adagwirizana kuti mayi aliyense amene sapita kuchidikiriro (kukadikirira pamene masiku ake obereka ayandikira) azipereka K10 000.

“Cholinga chathu ndichoti amayi azipita msanga kuchipatala osati kudikira matenda ayambe chifukwa ena amapezeka kuti aberekera panjira kapena kunyumba. Ndalamayo imagwira ntchito zosiyanasiyana pachipatalapo,” adatero.

Munthali adatsimikizanso kuti anthuwo sapatsidwa malisiti potsimikiza kuti apereka ndalamayo zomwe zingabweretse mavuto polondoloza ngati ndalamazo zikugwiradi ntchito yoyenera.

“Ndalama iliyonse imafunika umboni monga lisiti kuti yalipilidwadi, apa tivomereze kuti zimalakwika ndipo ndawauza kuti athane ndi vutolo,” adalongosola Munthali.

Iye adati amayi amene amalipira ndalamayo ndi amene apita mochedwa kuchidikiriro, amene aberekera m’njira kapena amene aberekera kunyumba.

“Amene amakadikirira kuchipatala salipira kanthu akabereka,” adatero Munthali.

Komabe ngakhale mfumu yaikulu Kampingo Sibande ikuti malamulowo akuwadziwa, iyo idati sikudziwa kalikonse ngati anthuwo akuyenera kulipira.

“Ife chindapusa chomwe tidavomereza ndi chokhudza kukwatiwitsa mwana osati izizi,” adatero Sibande.

Iye adati malamulowo pamene amakhazikitsidwa amafuna alimbikitse kuti amayi azipita kuchipatala pamene masiku awo ayandikira.

Izi zikukhumudwitsa amayi oyembekezera. Malinga ndi mayi wina amene wangobereka kumene mwana wa mwamuna pachipatalapo, K10 000 ndi ndalama yambiri yomwe sangayipeze.

“Ngati adali malamulo, ndiye mwina bwezi atatidziwitsa kuti tiyambe kutsala ndondomeko yake. Apapa akutiranga koma osadziwa tchimo lathu. Komanso masiku anowa ndi munthu utiyo wa kumudzi angatulutse K10 000?” adafunsa mayiyo.

Mfumu James Lupeska ya m’deralo idati ngati mayi salipira ndiye kuti pena amabwenzedwa ndikulemberedwa kalata yopita ku chipatala cha boma pa Mzimba kapena chipatala chachikulu cha Mzuzu Central.

“Tidayamba kalekale kulipiraku ndipo amati ndi ndalama zopangira chitukuko pa chipatalapo monga kumanga zimbudzi,” adatero Lupeska. n

Related Articles

Back to top button