Anatchereza

Wokondedwa Anatchereza,
Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Thandizeni.
Ndili ndi mkazi yemwe ndakhala naye kwa nthawi ndithu. Iye adapezeka wodwala ndipo mthunzi wake utatsala miyezi iwiri kuti akhale ndi mwana, makolo ake adamuitanitsa. Pozindikira kuti izi zimachitika, ndidaloleza kuti apite.
Ndipo sindidafowoke kumuthandiza nthawi yonseyo mpaka kuchira. Koma atachira, achibalewo adati ndichoke kumene ndikukhala ndipite kwawoko.
Sindidagwirizane nazo ndipo ndidakana. Mwanayo atabadwa, adati ndisapite kukamutenga koma ndipite komweko tizikakhala. Sindidagwirizane nazo ndipo ndidaneneratu kuti sindingapiteko.
Lero patha miyezi 13, ndipo makolowo akunena kuti ndipite kumudziko ndikamutenge mwanayo. Ndichitenji?
SL,
Balaka
SL,
Zikomo chifukwa chondikhulupirira. Choyamba mukuyenera kuzindikira kuti pena anthu amakhala ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana. Ndikulangizani molingana ndi kuti simunatiuze ngati mkazi wanu ndi inu muli a mitundu yofanana.
Ngati muli a mtundu umodzi, mukudziwa chimene ndikunena. Komanso mukuyenera kudziwa chimene makolowo akuchitira izi.
Nchifukwa chake ndinganene kuti ngati muli a mtundu umodzi, mwina mukhoza kudziwa kuti panali china chimene amafuna achite naye mwanayo, ndiye amakumangani. Koma chifukwa sizinatheke, nchifukwa akukuuzani mupite.
Koma zonsezo ndi inu ndi mkazi wanu. Kodi maganizo ake ali pati? Akudziwa, akuuzani.
Sindikhulupirira zaufiti, koma izitu ziliko.
Tsono pa ganizo lakuti mukamutenge mwanayo kapena ayi, ndikuuzani motere: mwanayo mukamutenge, chifukwa ndi wanu. Koma mupite kukamutenga patapita nthawi mpaka kutamvetsetsa chimene chikuchitika. Pitirizani kumuthandiza kuti musamuphere ufulu.
Cholinga choti pathe nthawi kaye nchakuti, muone momwe zikukhalira. Panopa, tumizani zofunika.
Anatchereza.

Kodi akazi amafuna chiyani?
Zikomo Anatchereza,
Ine ndi mnyamata wa zaka 24 ndipo ndikusaka msungwana wakuti ndimange naye banja. Komatu zikundivuta.
Vuto lalikulu ndilakuti sindikudziwa kuti akaziwa amafuna chiyani kwenikweni.
Izitu ndikunena chifukwa cha zomwe ndakhala ndikuziona. Panopa ndafunsira akazi okwana atatu koma chomwe ndikuchiona nchakuti ngakhale akundikana, pakatha masiku angapo, amandiimbira, kapena kuchita zina, kundikopa kuti chibwenzi chiyambepo.
Nchifukwa chiyani akuchita izi? Ndikufuna kukwatira, koma sindikudziwa kuti kwenikweni amafuna chiyani? Thandizeni gogo.
CGS,
Karonga
CGS,
Zikomo chifukwa cha uthenga wanu.
Mkazi asanalole mwamuna ukwati, amadikira kaye ngatidi mwamunayo watsimikiza.
Akatero, amaona kaye ngati mwamunayo angamuthandize. Apa amaunikiranso ngati angayanjane magazi polingalira mtundu, chipembedzo, maphunziro  ndi zina zotero.
Malingaliro otero angabweee patatha nthawi tsono nchifukwa chake kuyambira kale amanena kuti ndikuyankha mawa.
Iyi imakhala nthawi yoti akufufuzeni ngati simukudziwana bwino.
Kodi inuyo mbiri yanu njotani? Mwinatu akaziwo sakukudziwani ndiye akafufuza akupeza kuti mulibe banga, nchifukwa chake akubwerera kuti mukwatirane nawo.
Malangizo anga ndi akuyi, musanafunsire, muzimulola mkaziyo akudziweni. Muzimupatsa nthawi yokwanira ndi kumulola kuti akudziweni bwinobwino.
Kupanda kutero, palibe chotheka.
Anatchereza.

Share This Post