Chichewa

Anatchezera

Ndimamukonda
Agogo,
Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine n’kumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani?
Ine Amfumu,
Zingwangwa

Amfumu,
Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu ndi chiyani jwenikweni. Poyamba mwanena kuti mkaziyo munasiyana naye zaka ziwiri zapitazo, munasiyana chifukwa chiyani? Mwati pano mkaziyo akuti mubwererane ndipo inu nomwe mukuti ‘kunena zoona ndimamukonda’. Komanso inu nomwenso mukuti pano munalimba mtima, mukutanthauzanji? Mwatinso mkaziyo ali ndi mwana wa mwezi umodzi, n’chachidziwikire kuti mwanayo si wanu-poti mwanena nokha kuti chibwenzi chanu chidatha zaka ziwiri zapitazo. Apatu, kunena zoona Amfumu, mayankho muli nawo ndinu. Ngati mkaziyo mukuti mumamukonda, chovuta n’chiyani kuti mubwererane? Koma mukuti mwalimba mtima, kulimba mtima kotani? N’chifukwa chake ndikuti zonse zili ndi inu kuti mubwererane kapena ayi poti zifukwa zake zomwe mudalekanirana mukuzidziwa ndinu. Mwakula mwatha, Amfumu.

Akufunabe wakale?
Agogo,
Ndili ndi mkazi yemwe ndabereka naye ana atatu koma nthawi zambiri wakhala akumafunabe chibwenzi chake chakale chomwe chidamusiya. Ndakhala ndikupeza ma SMS olemba I LOVE U MPAKA KALE pafoni. Ndikamufunsa amathamangira kupepesa. Kodi andithandiza ameneyu? Ndinganene kuti ndidapezadi mkazi kapena ndiyang’ane wina? Chonde ndithandizeni.
Ine Che Mwenye

Che Mwenye,
Pa Chichewa pali mawu oti madzi saiwala khwawa. Mawuwa akutikumbutsa kuti pali anthu ena amene akakhala pachibwenzi, ngakhale chibwenzicho chitatha akakumana amakumbutsa chikale; amathanso kumachitirana nsanje, chonsecho chibwenzi adathetsa pakati pawo. Mchitidwe kapena khalidwe lotere silofunika anthu mukakhala m’banja chifukwa tanthauzo lake n’loti wina akuzembera mnzake wabanja pokhala ndi chibwenzi kapena zibwenzi zamseri. Wina akangozindikira kuti mnzangayu akundiyenda njomba, ukwati nthawi zambiri sulimba.
Tsono apa kunena mwachindunji, mkazi wanuyo alibe chilungamo chifukwa sangamalembe kapena kulandira ma SMS achikondi kwa wina inu mulipo. Malamulo a m’banja amakana zimenezi, chifukwatu munthu wotere sunga mukhulupirire. Banja lagona pachikondi ndi chikhulupiriro kwa wina ndi mnzake.
Komanso inu, abambo, muli ndi vuto. Akazi anu akachokapo basi muli pafoni gwi! kuyang’ana kuti waimba ndani kapena kumayang’ana ma SMS. Si bwino kumatero chifukwa zimaonetseratu kuti m’banja mwanu simukhulupirirana.Chomwe mungachite apa ndi kukhala pansi ndi akazi anu kuwafotokozera bwino lomwe za kuipa komagonekerana khosi ndi bwenzi lawo lakale pomwe tsopano ali ndi inu. Ngati akupiririzabe mchitidwe wotere, muli ndi zifukwa zokwanira zothetsera banja chifukwa mkazi sakhala ndi mitala. Pajatu amati mapanga awiri avumbwitsa.

Related Articles

One Comment

  1. Chifukwa chani nkazi sangakhale ndi mitala ngati mamuna? Ndiyankhe apa iwe “Anachezera”. Asa!

Back to top button