Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Mayi anga amandilodza

Anatche,

Zikomo gogo chifukwa cha malangizo amene mumapereka kwa ife awerengi anu. Anga ndi mantha pa zomwe amandichita mayi anga.

Anzawo kwambiri adandiuzapo kuti mayiwo adandiikira mankhwala m’chakudya kuti ndisiyane ndi mkazi wanga. Malinga ndi zochitika pakhomo pathu, sindikudabwa nazo izi.

Ndimapezeka kuti ndikumuchitira nkhanza zosadziwika bwino mkazi wanga ngakhalenso ana athu. Ndipo nthawi zina ndimamuuziratu kuti achoke pakhomopo pa zifukwa za ziii!

Pena ndikakhala bwino, ndimamukonda mkaziyo koma zikangogundika kumakhala ndewu osati masewera. Ankhoswe adasiya kubwera kudzagamula nkhani zathu. Nanenso ndatopa nawo moyowu.

Ndichitenji?

LW,

Blantyre.

LW,

Nkhani yanu ndi yomvetsa chisoni. Zakuti ena amatha kuchitira zoipa zotere ana awo ndimadziwa. Ena amatha kuchitira mankhwala ana awo kuti asaadzakwatire kapena kuti aziwakonda kwambiri.

Ndine mmodzi mwa amene amakhulupirira kuti padziko lapansi pali ochita zabwino ndi ochita zoipa. Mayi anu akhoza kukhala ndi mphamvu yochita zoipa.

Langizo langa kwa inu ndi lakuti, mulimbikire kupemphera kuti chiwanda chili ndi mayi anu chisakukhudzeni. Pofika pokhala ndi ana awiri si masewera ndiye izi zikhoza kungokusokonezani zitukuko za pakhomo panu.

Langizo langa lalikulu ndi lakuti, musayerekeze kupita kwa asing’anga chifukwa kumeneko mukangopusitsidwa chabe. Akhoza kukufunsani mafunso inu kumuonetseratu mukukaikira mayi anu kuti akukulodzani. Nanga akakakuuzani kuti muwakonze?

 

Adandithawa

Gogo wanga,

Ndinali paubwenzi ndi msungwana wina wa ku Nkhata Bay kwa chaka. Mwadzidzidzi, iye anathetsa chibwenzicho pa zifukwa zosadziwika bwino. Koma ndakhala ndikumuthandiza pa maphunziro. Ndidapeza chibwenzi china ndiye akubwera ati tibwererane.

FG,

Machinga.

FG,

Ameneyotu amafuna kukutayani chifukwa anaona mawanga ena. Mwinatu anali ndi chikhulupiriro kuti apeza mwamuna wina, kapena alipo wina amamunamiza. Mwina kumenekonso zakavuta kapena mwamunayo wamutaya.

Musakhale naye ntchito ameneyo, si mwati ichi nchibwenzi? Chibwenzitu ndi njira yodziwira munthu amene ungadzamange naye banja ndiye ngati uyu akukutayani popanda chifukwa chenicheni musanalowe m’banja mutayeni angadzakuvuteni kutsogoloku.

Muyeneranso kuzindikira kuti kunjaku kwaopsa. Ino si nthawi yomangosinthana akazi ngati zovala.

 

Apongozi, alamu ovuta

Anatchereza,

Ndine mnyamata wa zaka 23 ndipo ndili ndi mwana wa mwamuna wa chaka chimodzi. Ndimagwira ntchito ku Lilongwe. Vuto lalikulu ndi apongozi   anga komanso abale a mkaziyo. Iwo amachita zonse zotheka kuti ndisiyane ndi mkazi wanga. Ndichitenji?

BB,

Lilongwe.

BB,

Nkhani yanu ndiyovuta kuyankha chifukwa mwangobenthula pang’ono. Kodi iwowo amati vuto ndi chiyani? Kodi mkazi wanuyo mudatengana naye bwanji? Ukwati wanu ulibe ankoswe? Kodi mukukhala pachitengwa?

Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunatambasule bwino nkhani yanu. Zikomo.

 

Ofuna mabanja

Awerengi, ndisanakupatsireni mndandanda wa ofuna mabanja amene atumiza mauthenga awo sabata ino, ndati ndinenepo nkhani imene yakhala ikundikhudza makamaka patsamba lino.

Ndimalandira mauthenga ambiri a achinyamata amene amanena kuti akufuna mayi wamkulu kuposa iwo. Ambiri mwa achinyamatawa amati akufuna mayi wakuti ali ndi chuma kale.

Monga gogo, izi zimandikhudza. Mauthengawa ndikamaika sikuti zimandisangalatsa koma chifukwa monga gogo ndimalemekeza ufulu wa wina aliyense kupeza wachikondi wake. Uthenga umene sitiika ndi umene ndaona kuti ukukhudza ana.

Tsono langizo langa kwa anyamata amene amafuna mkazi wamkulu, wachuma kale ndi lakuti, uwu ndi ulesi waukulu. Nchifukwa chiyani mukufuna kupeza yophaipha? Chuma simungachipeze kupyolera m’kukwatira wa chuma kale. Ichi nchimasomaso. Dekhani komanso dzilimbikireni nokha. Mukadzakhala pabwino, simudzavutika kupeza kazi wa kukonda kwanu.

Nanga mpaka mukwatirane ndi munthu wa msinkhu wa mayi anu?

 

Ndine mnyamata wa zaka 35 ndipo ndili ndi ana awiri. Ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 20 ndi 40 koma akhale wopemphera. 0885629370. n

 

 

Related Articles

Back to top button