Anatchezera

Ndimukhulupirirebe?
Agogo,
Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina wake ndipo ndakhala naye mwezi umodzi. Vuto ndi loti iye ali ndi mimba ya miyezi iwiri. Kwathu sakudziwa. Ndiye nditani, agogo?
Malizani,
Blantyre
A Malizani,
Funso lako ndi lovuta kukuyankha chifukwa sukufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti bwenzi lako wakhala nalo mwezi umodzi koma akupezeka kuti ali ndi pathupi pamiyezi iwiri. Ndiye ukuti utani pamenepa?
Ndikuyankha pokufunsa kaye mafunso awa: Kodi iwe ndi dokotala kuti udziwe kuti mimba ya bwenzi lakolo ndi yamiyezi iwiri? Kodi udadziwa bwanji kuti ali ndi pathupi? Adachita kukuuza ndi iyeyo kapena udachita kumva kwa ena? Nanga pathupipo ndi pa yani? Kodi iweyo, Malizani, udayamba wakhala malo amodzi ndi mtsikanayo?
Ndafunsa dala mafunso amenwa chifukwa mayankho ukuwadziwa ndiwe. Ngati zili zoona kuti chibwenzi chanu chatha mwezi umodzi koma mtsikanayo akupekeza kuti ndi wodwala kale, miyezi iwiri, monga ukunenera, ndiye kuti adachimwitsana ndi wina wake, osati iwe. Tsono zili ndi iwe kuvomereza kuti mimba ili apo, ngakhale si yako, umukondabe ndipo mwana akadzabadwa udzamulera ndi kumusamalira. Koma n’kutheka? Iwe ndinu Yosefe kuti uvomereze kuti udzatero popanda vuto lililonse?
Ganiza mofatsa ndipo chilungamo choti uchite chioneka chokha. Inde, n’kutheka kuti bwenzi lakolo ndi lachilungamo ndipo lidakuuza za pathupipo. Ndi ochepa amene angatero. Ndiye zili ndi iwe kupitiriza chibwenzi chanu kapena kuchithetsa mwamtendere.
Ndazama m’chikondi
Agogo,
Ndimadziwa kuti kukhala pachibwenzi uli pasukulu ndi zolakwika, koma nanga ine nditani? Ine ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili m’chikondi ndi mnyamata wina yemwe timakondana kwambiri ndipo timathandizana nkhani za sukulu, za kutchalitchi ndi zina zotero ndipo tinalonjezana kuti sitidzagonana mpaka titakwatirana. Koma vuto ndi loti kwathu amandikaniza kupanga chibwenzi ati zimalakwitsa sukulu ndipo utha kutenga mimba. Ndimayesetsa kuti ndithetse chibwenzichi koma ndimakanika chifukwa ndimamukonda kwambiri, ndiye nditani ine?
Amene akukuuza zoti kukhala ndi chibwenzi uli pasukulu sakulakwa, mwanawe. Uwamvere! Poyamba zimayamba choncho, malonjezo, kuthandizana, izi ndi izi, kenaka mutu umaima ndipo pamene uzidzati ‘hii! ndapanga chiyani?’ zako zitada.
Ndithu, mwana iwe, nthawi yokhala ndi chibwenzi siinakwane chifukwa udakali wamng’ono ndipo uli iwe apo ndi pamsinkhu wovuta zedi. Samala, ungadzanong’oneze bondo. Zinazi ndi bwino kuzipewa.
Panopo ukuona ngati mnzakoyo akukukonda m’choona pamene ali ndi kampeni kumphasa. Amayamba kukulowa pang’onopang’ono ngati thekenya kenaka udzangozindikira zinthu zalakwika, wakuchimwitsa! Limbikira sukulu kaye, zachibwenzi pambuyo. Sukulu ndi zibwenzi siziyenderana.
Imva izi, mwana iwe, mawu a akulu amakoma akagonera.
Ofuna Mabanja
Ndikufuna mkazi wa zaka pakati pa 18 ndi 21. Ndine mphunzitsi. Amene angasangalatsidwe aimbe pa 0881 939 676. Zachibwana ayi, koma zasiliyasi.
Ndine mwamuna wa zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi wokongola woti ndimkwatire. Mkaziyo akhale wosachepera zaka pakati pa 21 ndi 24, woti adalemba kale mayeso ake a MSCE komanso wopanda mwana. Ngati ali pantchito zitha kukhalanso bwino kwambiri. Omwe angandifune andiyimbire pa 0884 322 798.
Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndikufuna mwamuna womanga naye banja. Akhale wa zaka zosapitirira 27. Wotsimikiza aimbe pa 0885 552 045.
Ndili ndi zaka 28 ndipo ndili ndi ana awiri. Ndikufuna mwamuna woti ndimange naye banja koma akhale woti adayezetsapo magazi ndipo adapezeka ndi kachilombo ka HIV. Wasiliyasi aimbe pa 0881496 409.

Share This Post