Anatchezera

Anatchereza

Ndikumanyozedwa

Anatchereza,

Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Ine ndili pabanja ndipo pano tikutha miyezi 7 ndipo timakondana kwambiri. Koma panopa ndikunyozedwa ndi mkazi yemwe mwamuna wangayu adamukwatira poyamba ineyo kulibe. Kodi pamenepa nditani?

Edna,

Blantyre

Zikomo mayi Edna,

Choyamba ndikumbutseni kuti chikondi ndi anthu awiri, wachitatu ndi kapasule. Ndikhulupirira mudayamba mwamvapo mawu amenewa. Ndiye apa mwanena nokha kuti inu ndi amuna anu mumakondana kwambiri, ine ndingoti umo ndiye ziyenera kukhalira chifukwa maziko a banja langwiro ndi chikondi, chikondi chake chozama. Pamene pali chikondi palibe mantha, koma dziwani kuti nthawi zonse padzakhala ena ena ansanje omwe sakondwera anthu akamakhala mwachikondi m’banja. N’kutheka kuti mkazi wakale wa mwamuna wanu akuchita nsanje ndi inu malinga ndi mmene mukukhalira m’banja mwanu n’chifukwa chake akuyesayesa kuti akusokonezeni. Ndi kavuwevuwe ameneyo, musamamulabadire. Sindidziwa kuti mkazi mukunenayo banja ndi mwamuma wanu lidatha bwanji, ndiye nkhani yoti mukumanyozedwa ndi mkaziyo muwauze amuna anu. Ngati sakuchitapo china chilichose chokuthandizani, muli ndi ufulu kuitengera nkhaniyi kubwalo la milandu kuti chilungamo chioneke chifukwa pokunyozani akukuphwanyirani ufulu wanu.

 

Ndidalirebe?

Agogo,

Ndine mnyamata wa zaka 23 ndipo ndimagwira ntchito ku Mangochi. Asananditumize kuno ndidakumana ndi mtsikana wina wake dzina lake Zione B, wa zaka 20 ndipo panthawi imene ndinkamufunsira iyeyu adali ndi chiphaso choyendera kunja (passport). Mu June mnzake wina adamuuza kuti wamupezera ntchito ku Joni koma panthawiyo adamuyankha kuti sangapite n’kundisiya ine pandekha. Mu August achimwene ake adandiitana kunyumba kwawo ku Lilongwe kukakambirana zokhudza ukwati wathu choncho tidagwirizana za mwezi wa December kuti tidzapange chinkhoswe. Chokhumudwitsa nchakuti mkaziyu adapita ku Joni pa 7 November ndipo adandiimbira foni kamodzi kokha mmene adangofika kumeneko ndipo mpaka pano sakuimbanso. Ndikamuimbira panambalayo sikupezekanso. Mmene zililimu kumbali ya chikondi chathu zikuta- nthauzanji?Ndidalirebe kapena ayi?

  1. M’min,

Mangochi

Zikomo F. M’min,

Mosafuna kuchulutsa gaga m’diwa, wachikondi wakoyo alibe chikondi ndi iwe ndipo ndakaika ngatidi adapita ku Joniko kukagwira ntchito ndipo ndikuganiza kuti kudali kuphiphiritsa chabe mmene amati mnzake wamupezera ntchito. Mmene ndikuonera ine ali kubanja ameneyo! N’chifukwa chake adangoimba foni kamodzi kukuuza kuti wafika ku Jonjiko ndipo kenaka adasintha nambala kuti olo uimbe musamalankhulanenso. Ndiye langizo langa ndi loti usataye naye nthawi ameneyo, wapita basi. Yang’ana wina amene angakupatse chikondi chenicheni, osati wachiphamaso. Atsikana ambiri makono ano chilungamo chikumachepa, kaya n’chifukwa chiyani? N’chifukwa chake maukwati a masiku sakulimba chifukwa chosowa chilungamo. Ambiri akumakhala ndi zibwenzi zoposa ziwiri zamseri, aliyense n’kumamulonjeza kuti akwatirana naye. Zokhumudwitsa kwabasi.

 

Akundikaniza

Ndine mayi wa zaka 30, ndili pabanja ndipo ndili ndi ana 5. Ndimalakalaka nditabwerera kusukulu koma abambo akunyumba amakana. Ndipange bwanji?

 

Nzomvetsa chisoni kuti abambo akukukanizani kubwerera kusukulu. Ndi amayi ochepa kwambiri omwe amaganiza ngati inu, kuika maphunziro patsogolo. Ndikhulupirira bamboo aliyense akhoza kukhala ndi chidwi ndiponso wonyadira kuti mkazi wake akulimbikira sukulu chifukwa maphunziro ndiye chitukukocho. Ndakunyadirani kwambiri. Koma mwina pali zifukwa zake zimene amuna anu akukukanizirani kuti mubwerere kusukulu, mwina n’kutheka kuti ana ena ndi aang’onoang’ono moti adzasowa chisamaliro chanu mukapita kusukulu. Poti simunalongosole bwinobwino kuti sukulu yake ndi yotani mpovuta kuti ndikuthanzizeni kwenikweni, koma ngati zonse zili bwinobwino m’banja lanu, pitirizani kukambirana za ubwino wa sukulu pofuna kutukula banja lanu. Ndaonapo ine amayi akuluakulu apantchito, monga aphunzitsi, akupita kusukulu pofuna kuonjera maphunziro. Akakhoza amatha kukwezedwa pantchito ndipo potero amathandiza amuna awo pankhani ya chuma m’banja. Sukulu sinamatu paja. Mwina chilipo chimene akukukayikirani amuna anuwo kuti mukabwerera kusukulu sizikhala bwino. Ndikhulupirira si choncho.  

 

OFUNA MABANJA

Ndikufuna mkazi woti ndimange naye banja, wa zaka 18-25, akhale wapantchito. Amene angasangalatsidwe aimbe pa 0882 234 843. Zachibwana ayi, ndili siliyasi.

 

Ndine wa zaka 32.Ndikufuna mwamuna wa zaka 35-45. Wofuna aimbe pa 0881 042 774.

Ndine mnyamata wa zaka 25 ndikufuna mkazi wa zaka 18 mpaka 26 wofuna banja. Aimbe pa 0995 154 501

 

Sindili pantchito koma ndikufuna mkazi wa zaka 25-35. Wosangalatsidwa aimbe pa 0992 395 279.

Ine ndi wa zaka 32 ndikufuna mwamuna wabanja koma akhale wa siliyasi. Akhale wa zaka za pakati pa 35 ndi 40, woopa Mulungu. Tandiimbirani pa 0888 437 123.

Share This Post