Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Adachotsa mimba

Gogo,

Ndili ndi mkazi amene kwathu amafika, inenso kwawo ndimapita. Mwamwayi, ndidamupatsa mimba ndipo tidagwirizana kuti tikonzekere mwana wathuyo. Koma tili mkati moyembekezera, iye adachotsa mimbayo. Ndichite naye chiyani?

KT,

Zomba.

 KT,

Mkazi ameneyo sangakusungeni. Kuchotsa mimba n’kupha komwe. Kodi iyeyo sanakuuzeni kuti n’chifukwa chiyani adachotsa mimbayo? Mwinatu amakaika kuti simukwanitsa kulera mwanayo. Mwina padalibe chitsimikizo chokwanira kuti musungana. Komabe, mulimonse mmene zingakhalire, kuchotsa mimbayo kudali kulakwa. Ngati munthu akupha gazi la magazi anu, pali zambiri zoipa zimene angakuchitireni.

 

Ndazunguzika

Gogo,

Ndili pabanja koma timakhala kosiyana chifukwa cha ntchito. Mwezi ukatha ndimamutumizira ndalama koma ndikangopanda kutumiza amati ndikufuna kusokoneza banja. Tilinso ndi bizinesi imene ili komwe mkazi wangayo amakhala. Ndikakhala kuti ndalama zandisowa ndipo ndikamupempha amati ndalama zatha. Ndichitenji?

LP,

Thyolo.

 LP,

Ngati si nkhani za zibwenzi, mabanja ambiri amatekeseka chifukwa cha nkhani za ndalama. Kayendetsedwe ka chuma pabanja kamafunika kuchitika mogwirizana. Choncho nkofunika kuti mukhale pansi ndi kukambirana momwe ndalama ziziyendera. Mukuyenera kuunikira bwino momwe muzigwiritsira ntchito ndalama zimene mwapeza aliyense payekhapayekha komanso bizinesi yanu.

 

Ali ndi mwana

Odi gogo,

Pali mkazi wina wa mwana kale amene ndili naye m’chikondi. Ndine wokonzeka kumukwatira koma ena akuti ndimusiye chifukwa ali ndi mwana kale. Komanso ena akuti ndimukwatire. Ndichitenji chifukwa chikondi changa paiye nchozama.

MKM,

Nsanje.

MKM,

Pajatu chikondi ndi anthu awiri ndipo ngati awiri akondana, palibe angawalekanitse. Tsatani chokonda cha mtima wanu ndipo muyenera kumukonda mkazi wanuyo ndi mwana wakeyo. Taonapo mabanja ochuluka amene akukhala bwinobwino ngakhale mwamuna kapena mkazi adali ndi mwana wakunjira. Kodi amene akuti musatengane nayewo akupezerani mkazi wina?

 

Ofuna  Banja

Ndine mtsikana wa zaka 21 ndikufuna mwamuna wodzakwatirana naye. 0888972662.

 

Ndine mayi wa mwana mmodzi ndipo ndikufuna mwamuna. 0884620216.

 

Ndili kundende ndipo ndituluka posachedwa. Ofuna atumize uthenga kwa mkulu wa pandende ino pa 088842396.

 

Ndili ndi zaka 32 ndikufuna mkazi wa zaka 25. 0885586333.

 

Ndili ndi zaka 20 ndikufuna shuga mami. 0884055485.

 

Ndili ndi zaka 25 ndikufuna mkazi wa zaka 20 mpaka 24. 0882 670 052.

 

Ndili ndi zaka 22 ndikufuna mkazi wosaposa zaka 20. 0884 972 707.

 

Ndikufuna mtsikana wa chuma amene akusowa chikondi. 0885 243 621.

 

Ndili ndi zaka 22 ndikufuna mkazi. 0882507551.

 

Ndili ndi zaka 23 ndikufuna mkazi. 0884 975 939.

Ine nyamata wa zaka 27 ndikufuna sugar mami wa zaka 34 mpakana 45 akhale wa ndalama andiyimbire pa 0111 642 230

 

Ndili ndi zaka 22 ndikufuna mkazi wopanga naye ubwenzi. Akhale wachifundo, wachikondi chosaona umphawi wodalirika ndi womvetsetsa. 0884 660 274

 

Ndili ndi zaka 25 ndipo ndikufuna mkazi womanga naye banja koma akhale Mkhristu wa zaka za pakati pa 18 ndi 24.

0881 663 069

 

Ndikufuna mkazi wakuti ndikhale naye pachibwenzi mpaka ukwati. Akhale wochokera chigawo cha pakati woti sanakwatiwepo. 0999 873 691

 

Ndili ndi zaka 25 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka 18 mpaka 25. 0888 176 547/ 0994 346 472

 

 

 

 

 

Related Articles

Back to top button