Anatchezera

Sakundilipira
Zikomo gogo,
Ndakhala ndikugwira ntchito kukampani ya alonda ina kwa miyezi 11 popanda masiku opuma. Mwezi ulionse amatidula K500 ati ya yunifolomu. Ndidasiya ntchito mwezi wa December chifukwa amachedwa kulipira. Pakatha miyezi iwiri amatipatsa za mwezi umodzi. Ndalama za mwezi wa December mpaka lero sanandipatse.
HP, Zomba.

HP,
Kampani imeneyo ndithu mukhoza kuitengera kukhoti la makampani. Poyamba amakuberani kukulipiritsani yunifolomu. Izi ndikunena chifukwa yunifolomuyo imakhala ya kuntchito osati yanu. Idali ngati chimodzi mwa zipangizo zanu za ntchito. Kodi angakuduleni malipiro chifukwa mukugwiritsa ntchito chibonga cha kampani? Mukhozanso kukadandaula kuofesi ya zantchito m’boma lanu ndipo akakuthandizani.

Zonse ndine
Gogo wanga,
Ndimagwira ntchito ya m’nyumba koma chilichonse pakhomo ndimachita ndine kuyambira kusamala m’nyumba, kuphika, kusesa panja, kusamala mwana kutsegula pageti, kuchapa ndipo zonse ndimagwira mwana ali kumsana olo akhalepo makolo a mwana sakundilandira mwana wawoyo. Ndithandizeni, Anatchereza, nditani pamenepa?
TM, Mulanje

Zikomo TM,
Inuyo pamene munkafunsira ntchito kwa bwana wanu mudafunsira ntchito yanji? Ndafunsa choncho chifukwa nthawi zonse munthu ukamafunsira ntchito bwana amakufunsa kuti ‘ukufuna ntchito yanji?’ Tsono ngati pali ntchito yoonjezera mumachita kugwirizana malipiro ake. Koma mmene mwayalira nkhani yanu zikuoneka kuti abwana anu ngovuta ndipo alibe chikondi. Kagwiridwe ka ntchito motere ndi ukapolo. Makamaka zandimvetsa chisoni kumva kuti chilichonse mumagwira nokha mwana ali kumsana ngakhale makolo ake alipo. Uku ndiye n’kusowa chikondi ngakhale kwa mwana wawo yemwe. Tsono ngati chili chizungu kuti chilichonse azisiyira watchito, tsiku lina adona m’nyumbamo adzasimba tsoka. Ndaonapo ine abambo ena akukwatira mtsikana wantchito kusiya mkazi wawo ati wantchito akukwaniritsa chilichonse m’nyumbamo. Amayi otere, omwe amasiyira wantchito chilichonse pakhomo iwo ali tambalale kumapenta milomo ndi zikhadaba pamkeka kapena pasofa, asadandaule zikawachitikira zotere. Amuna ambiri amalakalaka atadyako zophika akazi awo, koma haa, zonse amvekere wantchito aphika! Basopo! Samalani nazo zimenezo. Tsono inu a TM, musadandaule kwenikweni kuti ntchito ikukuchulukirani, pitirizani kugwira modzipereka, simudziwa chomwe Mulungu wakukonzerani. Tsiku lina mudzalandira mphotho yanu chifukwa cha kulimbikira ntchito pakhomo.

Ndemanga
Anatchereza,
Ndati ndiikirepo ndemanga pankhani yomwe munalemba chaka chatha ya mzimayi yemwe akuti mwamuna wake amamubisira kuti amamwa ma ARV. Mayiwa athokoze Mulungu kwambiri pakuti apulumuka ku likukumwe la matenda ndipo asachedwenso, apite kukhoti kukamang’ala. Mwamunayo ndo woopsa kwambiri akufunika chilango chachulu
Ine Mzungumbuli,
Lilongwe.

Share This Post