Anatchezera

Amandikakamirabe

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pang’ono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi iatatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni.

 

Zikomo mtsikana,

Ndikuthokoze kwambiri chifukwa cha maganizo ako abwino. Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima m’maganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu…? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi n’kusiya munthu wachikondi weniweni.

Gogo wanga,

Ndithandizeni. Ine ndinapeza bwenzi chaka cha 2010 ndipo adapita ku Joni chaka chomwecho. Foni amaimba, inenso ndimaimba koma amangoti ndibwera pompanopompano koma kuli zii! Amandiuza zolimbitsa mtima ndipo ndili pano ndakana amuna ambiri mpakana ena kufika pomandinena kuti ndine chikwangwani. Agogo, ndizidikirabe?

AK,

Lilongwe.

 

Zikomo AK,

Koma ndiye wapirira! Chibwenzi choyamba 2010 kenako munthu ulendo wa ku Joni chaka chomwecho mpaka pano? Ayi, ndithu, adzakugwiritsa fuwa lamoto ameneyo ukapanda kusamala naye. Zaka zachuluka ndipo adakhala kuti watsimikiza zomanga banja ndi iwe bwenzi china chake chitaoneka kuti alidi ndi cholinga choti awirinu mukhale thupi limodzi. Mwina n’kutheka mwamunayo wapeza kale mkazi ku Joniko ndipo adakwatira koma chachikulu uyambe wapeza umboni weniweni usadaganize chochita. Umuuze kuti wadikira nthawi yaitali ndipo choona chenicheni sukuchiona ndipo umupatse nthawi kuti ngati sachita zotheka kufikira tsiku lakutilakuti basi aiwale za iwe chifukwa wanamizidwa kokwanira. n

Share This Post