Chichewa

Anatchezera

Ndazunguzika

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani?

RM,

Mzuzu

Zikomo mwana wanga RM,

Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezo chilili m’thupi mwawo, ambiri amaopera kutalitali—safuna kudziwa n’komwe ngati ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka ndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka?

Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana mosadziteteza ndi munthu amene ali ndi kachilomboko. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize n’choti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira.

 

Amadikira ndimuimbire

Anatchereza,

Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni.

TG

Mtakataka

 

Zikomo TG,

Kunena zoona mwana iwe wafulumiza kukhala ndi chibwenzi. Za sukulu uli nazo pafupi iwe? Ndakaika. Iwe, mwana wa zaka 15, chibwenzi n’chachiyani, mwanawe? Ayi ndithu, ukayamba zibwenzi pamsinkhu wakowo sizidzakuthera bwino kutsogolo ndipo udzanong’oneza bondo. Mwana wamng’ono ngati iwe sayenera kukhala ndi zibwenzi koma kuika mtima pamaphunziro chifukwa sukulu ndi yofunika kwambiri. Sunandiuze kuti bwenzi lakolo lili ndi zaka zingati, koma ngati ndi munthu wamkulu ndikhulupirira wazindikira kuti si bwino kukhala pachibwenzi ndi mwana wamng’ono ngati iwe, n’chifukwa chake sakulabadira zokuimbira. Ndiye ngati umamva, chonde musiye ndipo uike mtima pasukulu! Ukapanda kumva langizo langa, kaya zako izo! Usadzati sindinakuuze. n

Related Articles

Back to top button