anatchezera

Amandimenya

Zikomo gogo,

Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mwamuna wa zaka 25. Tili ndi mwana mmodzi koma vuto ndi loti ndikati ndachoka kupita kwa chemwali anga osamutsanzika amati ndinali kwa amuna ena ndipo amandimenya. Nthawi ina adandimenya mpaka adandigoneka kuchipatala kwa sabata imodzi. Nditafotokozera akuluakulu za nkhaniyi sanandithandize. Kodi chibwenzichi ndithetse kapena ayi?

Ndine LBT

Wokondeka LBT,

Sukufotokoza bwinibwino kuti chibwenzi chanuchi ndi chotani—mukhalira limodzi kunyumba kwa mwamunayo kapena ukukhala ndi makolo ako? Nanga akuluakulu amene udawafotokozera za nkhaniyi ndi ati? Nanga chemwali akowo amakhala kuti poti mwamuna mpakana azikuganizira kuti unali kwa amuna ena? Ndiye wati nthawi ina yake adakumenya mpaka kukagonekedwa kuchipatala kwa sabata yathunthu, chipatala chake chiti cholandira munthu womenyedwa popanda lipoti la polisi? Ngati sindikulakwa, zikuoneka kuti iwe udathawa kwanu ndipo ukukhala ndi mwamunayo ndipo zikuoneka kuti makolo ako kapena achibale adakunyanyala chifukwa cha zomwe udachitazo n’chifukwa chake ngakhale utawafotokozera za kumenyedwa ndi mwamunayo amangoti ‘kaya zako izo, nzimene umafuna’. Ndakhala ndikulangiza achinyamata patsamba lino kuti mukafuna kulowa m’banja palibe amene angakuletseni chifukwa nzimene makolo amafuna kumene kuti ana awo apeze mabanja olongosoka, bola kutsatira miyambo yonse yofunika polowa m’banja. Mukadya mfulumiza kapena osamvera malangizo a makolo, zotsatira zake ndi ngati izi ukuonazi chifukwa simudalandire mwambo wa mmene anthu amakhalira m’banja. Chomwe ndingakulangize panopa nchakuti mwamuna womenya mkazi si mwamuna wokhala naye m’banja, ndi chilombo chimenecho. Nanga muyambe pano kuchitirana nkhanza muli ndi mwana mmodzi nanga kumene mukalambire zidzakhala bwanji?

Sindidziwa komwe amakhala

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 22 ndipo ndili ndi chibwenzi koma komwe amakhala sindidziwako. Takhala pachibwenzi kwa chaka chimodzi ndiye nditani?

CC

Lilongwe

 

Zikomo CC,

Koma nzoona zimenezo munthu n’khukhala pachibwenzi ndi mnzako kwa chaka chathunthu koma osadziwa komwe amakhala? Vuto ndi chiyani? Chibwenzi chotani chimenecho? Mudyetsanapo nyama ya galu pamenepo. Kodi mwamunayo safuna kuti udziwe komwe amakhala kapena iweyo ndamene ulibe chidwi chodziwako? Poti sindidziwa cholinga cha chibwenzi chanu sindinenapo zambiri, koma kunena zoona, ngati cholinga chanu ndi kudzakhala pabanja ndi bwino kuti mudziwane zenizeni—komwe iye amachokera, makolo ake, chomwe akuchita ndi zina zotere. Kupanda kumudziwa bwinobwino, sudzakhumudwa kuti wakwatiwa ndi chimbalangondo? Ndiye chmwe ungachite umufunse kuti akuuze komwe amakhala ndi zomwe amachita ndipo utsimikize zimenezo, kupanda kutero ndiye kuti sukudziwa komwe ukulowera, udzangozindikira uli m’dzenje lakuya! n

Share This Post