Anatchezera

Nditani Anatchereza?

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili ku koleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire m’banja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti inyeyo adzandikwatire. Kodi kumeneku ndi kukonda? Ndithandizeni, agogo, nditani.

Ndi L,

Likuni, Lilongwe

 

Wokondeka L,

Funso lako ndalimva ndipo ndikuti wafunsa bwino zedi. Bwenzi lakolo ndi munthu wachilungamo, koma chilungamo chake chaonjeza. Munthu wotere osamukhulupirira chifukwa ndi kamberembere. Iyeyu wanena chinthu chanzeru kwambiri kuti pakalipano musamagonane chofukwa akuopa kuti akatero atha nawe chilakolako chifukwa wakudziwa. Koma akuti akufuna apeze mkazi wina wapambali kuti azikapumirako poti iye ndi munthu, nanga iwe wakuuza kuti nawe utha kupeza wina woti uzicheza naye pamene mukudikira kuti mudzakwatirane? Akunama ameneyo; akufuna kuti azioneka ngati munthu wokhulupirika pomwe ndi wachimasomaso ndi akazi ena. Tikamati kudzisunga ndi nonse awiri, osati wina aziti mnzangawe udzisunge koma ine ndikayendayenda. Kunjaku kwaopsatu, ndiye wina azipanga dala zachibwana ngati zimene akunenazo, si zoona ayi. Ngati ndi wachilungamo, iyenso ayenera kupirira kuchilakolako cha thupi kufikira tsiku lomwe mudzalowe m’banja. Koma ngati adayamba kale zogonana ndi akazi ena, mchitidwe umenewo sadzausiya. Ndiye, kunena zoona, mwamunayo sali woyenerera kumanga naye banja chifukwa alibe chikondi chenicheni ndi iwe. Amati mbuzi ikalawa mchere sigwirika!

 

Amandikakamiza

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili ndi bwenzi langa wa zaka 19. Iyeyu amandikakamiza kugonana naye. Ine zimenezo sindimafuna koma ndimalola kupanga naye zimenezo chifukwa ndimamukonda kwambiri ndipo kukana ndimaopa kumukhumudwitsa. Ndiyeno ndipange chiyani kuti mchitidwewu uthe? Zikomo.

BL,

Lilongwe

 

Zikomo BL,

Pamsinkhu wakowo wayamba kale zogonana ndi anyamata? Zoona? Ndithu, sukula bwino, mwana iwe. Uli pasukulu kodi? Ayi ndithu, siya mchitidwe umenewo ndipo limbikira sukulu ngati uli pasukulu kuti udzakhale ndi moyo wansangala kutsogolo. Tsono ndikuuze za kuipa kwa zomwe ukuchitazo. Poyamba wati bwenzi lakolo limakukakamiza zogonana, ine ndikuti iweyo ndi amene umafuna! Si wanena wekha kuti umamukonda kwambiri ndipo umaopa kumukhumudwitsa. Zopusa basi! Adakuuza ndani kuti mukakhala pachibwenzi muyenera kugonana poonetsa chikondi chanu? Mathero ake mupatsanapo mimba kapena matenda ndipo zikatero adzangokutaya uko, osakulabadiranso! Ukatenga mimba usanakhwime pamchombo ndi vuto lalikulu limenelo. Mwina pobereka ukhoza kufa, kapena kung’ambika moti udzakhala ndi matenda aja odzionongera—mikodzo ndi chimbudzi kumatuluka nthawi imodzi usakufuna. Samala, mwana wanga, kunja kuno kwaopsa ndi matenda a Edzi. Ndiye chimene ungachite apa ungolimba mtima n’kumuuza bwenzi lakolo kuti sukufunanso zogonana chifukwa ino si nthawi yake. Ukamuuza zimenezo mpamene udzadziwe kwenikweni ngati amakukondadi. Ine ndakuuza, koma zonse zili ndi iwe mwini. Ukapanda kumvera usadzati ena sadakuuze! n

Share This Post