Anatchezera

Sakuthandiza

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse admwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji?

JS

Mulanje

 

Pepa JS,

Apa zikuonekeratu kuti ngakhale ukuti ‘amuna anga’ anthunu simunali pabanja ngakhale mumagonana mpakana kuberekerana mwana. Chimene chimachitika nthawi zambiri n’chakuti atsikana akangogwa m’chikondi ndipo mwamuna akangowauza kuti awakwatira, basi amaganiza kuti mwamuna ndi yemweyo basi ndipo amayamba zogonana naye ati pofuna kulimbikitsa chikondi kuti asamakaike za chikondi chawo, kumene kuli kulakwa kwakukulu. Atsikana ambiri aononga tsogolo lawo chifukwa cha mchitidwe wotere chifukwa anyamata kapena amuna ambiri ndi akamberembere, ongofuna kudzisangalatsa osalabadira za tsogolo la mnzawo. Akangomva kuti mtsikhana watenga pathupi basi, chibwenzi chimathera pomwepo. Zikatero mtsikana zako zada. Koma dziko lino lili ndi malamulo okhudza maukwati ndipo ngati wina wakuchimwitsa, ali ndi udindo woti akusamale komanso mwana. Ndiye apa usazengereze-pita ukadule chisamani kukhoti basi kuti chilungamo chioneke. Mwina amuna ena amene amakonda kuchimwitsa ana a eni akhoza kutengerapo phunziro!

 

Akundikakamira

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pang’ono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi itatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni.

MT

Zomba

 

Zikomo MT,

Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima m’maganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu…? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi n’kusiya munthu wachikondi weniweni.

 

Ndimudikirebe?

Gogo wanga,

Ndithandizeni. Ine ndinapeza bwenzi chaka cha 2010 ndipo adapita ku Joni chaka chomwecho. Foni amaimba, inenso ndimaimba koma amangoti ndibwera pompanopompano koma kuli zii! Amandiuza zolimbitsa mtima ndipo ndili pano ndakana amuna ambiri mpakana ena kufika pomandinena kuti ndine chikwangwani. Agogo, ndizidikirabe?

AK,

Lilongwe

 

Zikomo AK,

Koma ndiye wapirira! Chibwenzi choyamba 2010 kenako munthu ulendo wa ku Joni chaka chomwecho mpaka pano? Ayi, ndithu, adzakugwiritsa fuwa lamoto ameneyo ukapanda kusamala naye. Zaka zachuluka ndipo adakhala kuti watsimikiza zomanga banja ndi iwe bwenzi china chake chitaoneka kuti alidi ndi cholinga choti awirinu mukhale thupi limodzi. Mwina n’kutheka mwamunayo wapeza kale mkazi ku Joniko ndipo adakwatira koma chachikulu uyambe wapeza umboni weniweni usadaganize chochita. Umuuze kuti wadikira nthawi yaitali ndipo choona chenicheni sukuchiona ndipo umupatse nthawi kuti ngati sachita zotheka kufikira tsiku lakutilakuti basi aiwale za iwe chifukwa wanamizidwa kokwanira. n

Share This Post