Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Anzanga sakundifunsira

Ndine mtsikana wa zaka 20, vuto ndili nalo ndi loti sindikufunsiridwa ndi anyamata amsinkhu wanga koma okwatira okhaokha. Kodi agogo nditani pamenepa? Kapena ndingosiya kulola anthuwa ndi kumangokhala ‘single’?

EDS,

Lilongwe

 

Zikomo EDS,

Kuti uzifunsiridwa ndi anthu amene ali kale pabanja vuto lako ndi chiyani? Funsoli udzifunse wekha ndipo yankho ulipeza. Kodi umakonda kucheza ndi anthu otani-achinyamata anzako kapena akuluakulu oti si amsinkhu wako? Chifukwatu ngati umacheza ndi achinyamata anzako sipangalephere wina kukhala nawe ndi chidwi. Chimodzimodzi ngati umakonda kucheza ndi amuna oti ndi okwatira iwe n’kumawagonekera khosi, chowalepheretsa kukufunsira n’chiyani? Mwina anyamata sakukufunsira chifukwa akudziwa mbiri yako yoti umakonda ma ‘sugar daddy’. Ndiye madzi asanachite katondo, usiye kuwalola ndipo uyambe kucheza ndi achinyamata anzako. Mwana mng’onong’onowe chofuna kupasulira mabanja a eni n’chiyani?

 

Tachokera kutali

Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndakhala pachibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka 4. Poyamba pa chibwenzi chathu timakondana kwambiri koma panopa zinthu zinasintha ndipo ndikuganiza kuti mwina adapeza chibwenzi china ngakhale amakana ndikamamufunsa. Izi zili choncho ndimakanika kuti ndikhalenso pachibwenzi ndi munthu wina chifukwa ndimaganiza kaye komwe tachokera. Nditani naye mnyamata ameneyu, ndikhale nayebe kapena ndingosiyana naye? Chonde ndithandizeni.

LK,

Ntcheu

 

Mwana wanga LK,

Amati fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika. Chikondi sakakamiza. Monga wanena, udayamba kukhala ndi chibwenzi uli ndi zaka 16, cholinga cha chibwenzi chanucho chidali chiyani? Mumafuna kudzakwatirana pambuyo pake kapena adali masanje chabe? Mmene ndikuonera chidali chibwana ndipo pano mnzakoyo watha nawe chidwi, ndipo sakukufunanso. Ndiye madzi asadafike m’khosi musiye, uone zina. Udakali mwana wamng’ono, moti utaika mtima pasukulu sulakwitsa ayi. Ameneyo asakutayitse nthawi, ganiza za tsogolo lako.

 

Mwana si wanga?

Miyezi iwiri yapitayiyo ndidapititsa mkazi wanga kumudzi kaamba ka mwano ndi cholinga choti akatilangize kwa ankhoswe. Mwana wathu atabadwa mayi anga adali asanamuone chifukwa adabadwira m’tauni muno, koma nditapita kumilandu mayi anga adandiuza kuti mwanayo si wanga. Akuti maonekedwe a mwanayo ndi ine sitikufanana ndipo adanditsimikizira kuti pakapita nthawi bambo a mwanayo adzadziwika. Nditani pamenepa?

CR

 

Wokondeka CR,

Nkhani yanu ndi yovuta chifukwa ilibe umboni weniweni, komabe poti mwandifunsa ndiyesetsa kupereka maganizo anga kuti mwina mungapeze yankho pa funso lanu. Choyamba, amvulazakale adati pati bii pali munga kapena kuti moto sufuka popanda moto. Akazi anu mwano akuchitawo wachokera pati? Cholinga chawo ndi chiyani? Inuyo ngati mutu wa banja, simudakhale nawo pansi kuti muwafunse chomwe akuchitira mwano? Chilipo chimwene chikuwapangitsa akazi anuwo kuyamba mwano m’banja, mwina akufuna mchokero, chifukwatu mkazi wofuna banja amalemekeza mwamuna wake. Chinanso, amati galu wamkota sakandira pachabe. Chilipo chomwe mayi anu aona pofika mpakana kunena kuti mwanayo si wanu. Mayi aliyense amanyadira kukhala ndi chidzukulu, koma apa adabwapo kanthu n’chifukwa chake akuti ‘achimwene, mwanayu si wanu’. Koma ali ndi umboni wanji weniweni, poti m’mimba ndi m’chipala? Mwanayo mwina adatengera nkhope ya abale akuchikazi, mwina malume ake kapena agogo ake. Zimathekatu izi m’banja chifukwa zimatengera mphamvu ya magazi a mwamuna kapena mkazi. N’chifukwa chake kunja kuno kuli DNA kuti ngati pali kukayikirana mutha kukayezetsa kuchipatala kuti muone ngati pali ubale pakati pa mwana ndi makolo onse awiri. Koma kuyezetsa DNA si pano, kumalira ndalama osati zamasewera! Ndiye apa ine chimene ndinganene n’choti kuona maso a nkhono n’kudekha, ngati pali chinyengo tsiku lina zoona zake zidzakhala pambalambanda, ndithu zidzaoneka zokha. Komanso ngati inu mulibe chikaiko chilichonse ndi akazi anu ndipo muli ndi chitsimikizo choti sadakudyetseni njomba, palibe chifukwa choti muyambe kukaika panopo. Dziwani kuti mamveramvera adachotsetsa zolo paukwati! M’banjatu mumakhala zambiri, koma kuti lilimbe pafunika chikondi chozama pakati pa awirinu, komanso kupirirana ndi kukhululukirana wina akalakwa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »