Anatchezera

Akufuna mwana

Zikomo Gogo,

Banja ndi mwamuna wanga lidatha mu 2011. Ndidapeza mwamuna wina yemwe timamvana ndipo tidakayezetsa komwe adatipeza kuti tilibe kachilombo koyambitsa Edzi.Vuto ndi lakuti bwenzi langalo limakonda zogonana komanso limandiletsa kuchita za kulera. Wina adandiuza kuti bwenzi langalo lili ndi mkazi koma nditamufunsa adakana. Tsiku lina ndidaimba foni 5 koloko mbandakucha ndipo ndidamva kulira kwa mwana wa khanda. Nditamufunsa adakana ndipo adati ndi wa khomo loyandikana nalo. Ndizimukondabe?

R,

Chiradzulu

 

Wokondeka R,

Mwakumana ndi chilombo cha bodza. Wakunamizani kuti akufuna mwana chonsecho pansi pamtima akudziwa kuti akakupatsani mwana adzakuthawani nkupitiriza kukhala ndi mkazi wake. Wakunamizaninso kuti mwana amalira ndi woyandikana nawo nyumba. Ngati zili zoona, bwanji adadula foni? Asakutayitseni nthawi ameneyo.

 

Ndimamupitirira

Wawa gogo,

Ndili ndi zaka 17 ndi[po pali mnyamata wina wa zaka 20 yemwe akundifuna. Ndimamukonda koma vuto ndi lakuti iyeyo ndi wamfupi kuposa ine. Ndimachita manyazi ndikamayenda naye. Ndimulole?

C

 

Zikomo C,

Sindikuonapo vuto loti musamulolele! Kutalika kukhale nkhani? Chikondi chimachoka mumtima ndipo sichiyenera kuona ngati wina ndi wamtali kapena wamfupi, woonda kapena wonenepa, woona kapena wosaona ndi zina zotero. Chabwino nchiyani kuti mudzapeze mnyamata wamtali ngati inu kapena kukuposani koma alibe chikondi kapena kukhala ndi mwamuna ameneyu yemwe amakukondani nanunso kumukonda. Muloleni ameneyo basi.

 

Amakonda ndalama

Anatchereza,

Ndakhala paubwenzi ndi msungwana wina koma vuto lake akuoneka wokonda ndalama. Tikangokumana, amandipempha ndalama. Timalankhulana nthawi zambiri pafoni koma mwezi ukangotha amati tikumane. Kodi ichi ndi chikondi?

M,

Lilongwe.

 

Wokondeka M,

Ameneyo sakuthandizani. Mkazi woika ndalama patsogolo si wa bwino. Taonani akuonetsa mawanga ake muli pa chibwenzi nanga mukadzakwatirana zidzatha bwanji? Mudzaona kuti pakati pa mwezi mavuto okha okha m’banja. Koma ukangotha mwezi si kusekerera ku chitsakano kwake. Mpeweni.

 

Mtendere palibe

Kuyambira pomwe tidalowa m’banja, sitinathe mwezi tili pamtendere. Iye amati ine si mwamuna amene iye ankakhumba. Iyetu ndi wobadwanso mwa tsopano ndipo akati agwe ndi pemphero, mukhoza kupona kuti ayi mayi amapemphera uyu. Iye amati zivute zitani tidzasiyana basi. Kodi ndidikire adzandisiye, kapena ndilowere kwanga? Inetu ndimamukonda!

M,

Blantyre.

 

Ndili ndi mwana

Gogo,

Bwenzi langa ali ndi mwana mmodzi. Ndimamukonda ndipo ndimafuna kudzamukwatira koma ena akuti ndisatero. Timakondana, nditani?

MKM,

Nsanje.

 

Odi MKM,

Kukhala ndi mwana si chiletso. Ndaonapo mabanja akulimba winayo ali ndi mwana wakunjira. Musamvere zonena za enazo, tsatani mwamuna amene mtima wanu wakonda.

 

 Akuletsa kuona ana

Gogo wanga,

Banja ndi mkazi wanga lidatha zaka zinayi zapitazo koma akundiletsa kuti anawo abwere kwathu ndidzawaone komanso kuti ndikawaone amandiletsa. Ndichitenji ndikufuna kuona ana anga.

WK,

Salima.

 

Zikomo WK,

Banja likatha, ndi ufulu wa ana kuonedwa ndi kuthandizidwa ndi makolo onse awiri ngati ali moyo. Kodi inuyo banja lanu lidatha motani? Pakutha pa banja pamayenera kuikidwa ndondomeko yakuti kodi ana azikhala ndi ndani? Nanga mwamuna kapena mkazi azithandiza bwanji anawo. Koma vuto limatha kukhalapo ngati mkazi wanuyo adakwatiwanso. Mwina amamuletsa ndi mwamuna wakeyo poopa kuti mwina mukhoza kuyambanso kugwirizana kupyolera mwa anawo. Koma izo si zoletsa kuti mukaone ana anu. Ngati muli ndi a nkhoswe kapena abale, pitani kwa a nkhoswe kapena abale a mkaziyo mukafotokoze kuti mukufuna kuona ana anu. n

 

Share This Post