Anatchezera

Ndazunguzika

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ine ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani?

RM,

Mzuzu

 

Zikomo RM,

Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezi chilili m’thupi mwawo, ambiri amaopera kutalitali-safuna kudziwa n’komwe ngali ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka nndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka? Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana ndi munthu amene ali nako mosadziteteza. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize nchoti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira.

 

Amadikira ndimuimbire

Anatchereza,

Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni.

TG

Mtakataka

 

Zikomo TG,

Kunena zoona mwana iwe wafulumiza kukhala ndi chibwenzi. Za sukulu uli nazo pafupi iwe? Ndakaika. Iwe, mwana wa zaka 15, chibwenzi n’chachiyani, mwanawe? Ayi ndithu, ukayamba zibwenzi pamsinkhu wakowo sizidzakuthera bwino kutsogolo ndipo udzanong’oneza bondo. Mwana wamng’ono ngati iwe sayenera kukhala ndi zibwenzi koma kuika mtima pamaphunziro chifukwa sukulu ndi yofunika kwambiri. Sunandiuze kuti bwenzi lakolo lili ndi zaka zingati, koma ngati ndi munthu wamkulu ndikhulupirira wazindikira kuti si bwino kukhala pachibwenzi ndi mwana wamng’ono ngati iwe, n’chifukwa chake sakulabadira zokuimbira. Ndiye ngati umamva, chonde musiye ndipo uike mtima pasukulu! Ukapanda kumva langizo langa, kaya zako izo! Usadzati sindinakuuze.

 

Ndi mvundulamadzi

Gogo wanga,

Ine ndili ndi bwenzi langa lapamtima ndipo timakondanadi. Koma ndilinso ndi mnzanga yemwe kumbali amakumana ndi bwenzi langalo kumanena mabodza mpaka adamasukirana nkuyamba kumaimbirana foni ine osadziwa, ndinachita kumva kwa munthu wina atandiuza. Nditamufunsa bwenzi langalo adayankha kuti adachita kumuimbira ndi mnzangayo. Ndiye nditamuuza kuti ndikamufunsa, adati ndisatero chifukwa azichita naye manyazi ndiye ndinangozisiya. Koma akuti mnzangayo khalidwe lake ndi lotero chifukwa mnzanga winanso anadandaulapo nkhani zonga zomwezi za iye kuti amakonda kuthetsa mabanja a eni motero. Ena andilangizapo kuti ndisamachezenso naye. Inu mukuti bwanji pamenepa? Tinafuna kupanga chinkhowe koma chinalephereka ndipo sandiimbiranso foni kawirikawiri monga mwakale ndipo ndikamufunsa amangoti ‘kaya’ kapena ‘ndabalalika’. Nditani pamenepa?

D,

Machinjiri, Blantyre

 

Zikomo D,

Ndamva chisoni ndi nkhani yanu chifukwa mwasweka nayo mtima. Koma ndikufuna kukulimbitsani kuti, monga mwamuna, muyenera kupanga chilinganizo choti chikuthandizeni pamoyo wanu kuti kutsogolo kuti mudzakhale moyo wansangala. Mwina zachitikazi ndi mwayi wanu wolingalira kuti kodi akamati ‘bwenzi’ kapena ‘mnzanga’ ayenera kukhala munthu wotani? Mmene mwayalira nkhani yanu, zikuonekeratu kuti bwenzi lanulo ndi munthu wopanda chilungamo chifukwa ngati amaimbirana foni n’kumacheza ndi mnzanuyo, kaya nkhani zamtundu wanji, adayenera kukudziwitsani kuti mnzanuyo adamuimbira ndipo amati zakutizakuti. Sadachite bwino kukubisirani kuti amacheza ndi mnzanuyo pafoni. Nanga nkhani zake zachinsinsi zidali zotani zoti inu asakuuzeni? Komanso mnzanuyo waonetsa kuti ndi mthirakuwiri, kavuwevuwe, mvundulamadzi wotheratu. n

Share This Post