Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Wamboni, ine Msilamu

Zikomo Anatchereza,

Ndinagwa m’chikondi ndi mtsikana wa Mboni za Yehova mpaka ndinamuchimwitsa moti ndikunena pano kuli mwana wamphongo. Makolo ake atamufunsa ananditchula ineyo ndipo atandiitana ndi akwathu ndidavomera mlanduwo. Makolo a mtsikanayu adati ngati ndikufuna kuti zithe bwino ndilowe mpingo wawo kuti asakandisumire kukhoti komanso kuti ndizisamalira mwana wangayo. Ine sindikufuna kulowa mpingowo, koma mtsikanayu akuti akhoza kulola kulowa Chisilamu ngati makolo ake angalole. Kodi apapa ndiye nditani kuti mwanayu ndizimusamalira popanda kulowa mumpingo wawowo? Kodi nditani kuti mkaziyu ndimukwatire?

BJ,

Lilongwe

BJ,

Mwazingwadi, achimwene a BJ. Vuto lili apa ndi loti inuyo simufuna kulolera zofuna za makolo a mkazi munamuchimwitsayo koma mukufuna zanu ziyende basi! Sizikhala choncho mukafuna kulowa moyo wa banja. Kulolerana ndiye gwero la banja. Mkazi munamuchimwitsayo waonetsa kale chikondi chake kwa inu chifukwa akulolera kuti atha kukutsatirani ku Chisilamu bola makolo ake amulole, koma inu chikondi chanu n’choperewerako pang’ono chifukwa mukumenyetsa nkhwanga pamwala kuti simungayerekeze kulowa mpingo wa mkazi wanuyo. Mulungu ndi mmodzi, baba, mipingo ndiye njambirimbiri! Langizo langa apa ndi loti zonse zimatha n’kukambirana. Ngati akuchikazi nawonso sakulolera zoti mwana wawoyo alowe Chisilamu, monga inuyo mmene mwakanira kuti simungalowe mpingo wa Mboni za Yehova, kwatsala njira imodzi—muthabe kulowa m’banja, koma aliyense akhale ndi ufulu wokapemphera koma akufuna. Zikakaniza apo, ndiy kaya. Ndakhala ndikunena nthawi zambiri kuti banja si masewera; pamakhala zambiri zofuna kutsatidwa musanalowane, koma mukadya mfulumiza, mavuto ake amakhala ngati amenewa. Koma, baba, nzoona mungalephere kuthandiza mwana wanu kaamba ka kusiyana mipingo? Mwana adalakwa chiyani? Nzoona makolo a mkazi akukuletsani kuthandiza mwana wanu kaamba koti simunalowe mpingo wawo? Chonde, mwana yekhayo asavutike chifukwa cha nkhani yanu. Muzimuthandiza m’jira iliyonse, makolo a mkazi ndikhulupirira sadzaona cholakwika mwana wanu akamalandira thandizo kuchokera kwa bambo ake omubereka.

 

Amandikakamiza zogonana

Agogo,

Ndine mtsikana wa za 17 ndipo ndili ndi chibwenzi chomwe chimandikakamiza kuti tiyambe kugonana. Nditani?

 

Mwana wanga, musiye ameneyo, sadzakuthandiza! Ndipo wachita bwino kundiuza msanga za nkhawa yako. Anzako ambiri amakopeka ndi zautsiru ngati zimene akukukakamiza bwenzi lakolo ndipo mapeto ake ndi kutengapo mimba kapena matenda opatsirana pogonana. Anyamata kapena abambo ambiri si okonzeka kuvomereza kuti ndiwo akupatsa pathupi kapena matenda ndiye chimakutsalira, tsogolo lako n’kupiratu pamenepo. Fatsa, mwana wanga, sunga khosi ndipo mkanda woyera udzavala! Ukadzisunga udzaona kukoma moyo wako onse utapeza mwamuna weniweni amene adzakukonde ndi mtima wake wonse, osati kamberembere amene akuti muzigonana panopa muli pachibwenzi. Umuuziretu kuti iwe si chidole choseweretsa. Asaa!

 

Ofuna mabanja

 

Ndikufuna mkazi wa zaka 19-23 komanso woopa Mulungu—0881 131 533

 

Ndine mkazi wa zaka 33 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndili ndi kachilombo ka HIV koma ndikumwa mankhwala.

 

Ndikufuna mwamuna wa zaka 35-37. Wondifuna aimbe pa 0882 617 531

Ndine mwamuna wa zaka 35 ndipo ndi ana awiri.

 

Ndikufuna wachikondi woti ndikwatire, akhale Mkhristu wa zaka 25-30 wokhala ku Lilongwe konkuno. Akhale wokonzeka kukayezetsa magazi. Wondifuna andiimbire pa 0882 511 934.

 

Related Articles

Back to top button