Anatchezera

Chikondi amatero?

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili kukoleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire m’banja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti inyeyo adzandikwatire. Kodi kumeneku ndi kukonda? Ndithandizeni, agogo, nditani.

Ndine L,

Lilongwe

 

Wokondeka L,

Bwenzi lakolo ndi munthu wachilungamo, inde, koma chilungamo chake chaonjeza. Munthu wotere osamukhulupirira chifukwa ndi kamberembere. Iyeyu wanena chinthu chanzeru kwambiri kuti pakalipano musamagonane chofukwa akuopa kuti akatero atha nawe chilakolako chifukwa wakudziwa. Koma akuti akufuna apeze mkazi wina wapambali kuti azikapumirako poti iye ndi munthu, nanga iwe wakuuza kuti nawe utha kupeza wina woti uzicheza naye pamene mukudikira kuti mudzakwatirane? Akunama ameneyo; akufuna kuti azioneka ngati munthu wokhulupirika pomwe ndi wachimasomaso ndi akazi ena. Tikamati kudzisunga ndi nonse awiri, osati wina aziti mnzangawe udzisunge koma ine ndikayendayenda. Kunjaku kwaopsatu, ndiye wina azipanga dala zachibwana ngati zimene akunenazo, si zoona ayi. Ngati ndi wachilungamo, iyenso ayenera kupirira kuchilakolako cha thupi kufikira tsiku lomwe mudzalowe m’banja. Koma ngati adayamba kale zogonana ndi akazi ena, mchitidwe umenewo sadzausiya. Ndiye, kunena zoona, mwamunayo sali woyenerera kumanga naye banja chifukwa alibe chikondi chenicheni ndi iwe. Amati mbuzi ikalawa mchere sigwirika!

 

Safuna zoyezetsa

Anatchereza,

Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe m’banja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati “ine zimenezo ndiye ayi”. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati ndikudzikaikira ndipite ndikayezetse, osati iyeyo. Akuopa chiyani?

MJ

Lilongwe

 

Odi MJ,

Akuopadi chiyani ameneyo? Pati bii, pali munga, ife akale timatero. Chilipo chimene akuopa chifukwa akanakhala kuti ali bwinobwino, si bwenzi akuchita kukanira patalitali kuti ‘ine toto, pita wekha’. Kudziwa mmene munthu ulili usanalowe m’banja ndi chinthu chabwino kwambiri, makamaka masiku ano pamene kuli mliri wa kachilombo ka HIV/Aids. Mundimvetse bwinobwino pamenepa: si kuti munthu akapezeka ndi HIV ndiye kuti sayenera kukwatira kapena kukwatiwa, ayi. Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala pabanja, koma zimakhala bwino kudziwa mmene m’thupi mwako mulili pofuna kukonza tsogolo la banja lanu. Ngati wina apezeka ndi kachilombo kapena matenda ena kumphasa mumadziwa chochita pofuna kudziteteza kuti nonse mukhale moyo wathanzi. Komanso ngati mukufuna mwana m’banja mwanu madotolo amadziwa njira zokuthandizirani kuti mwana wanu asatenge nawo kachilomboko. Chachikulu ndi chikondi pakati panu-pali chikondi palibe mantha. Mufotokozereni wokondedwa wanuyo zimenezi kuti amvetsetse, koma ngati akumenyetsa nkhwangwa pamwala, musiyeni ameneyo, muyang’ane wina amene angakumvetsetseni pankhani yoyezetsa magazi.

 

Nsalu ya lekaleka

Anatchereza,

Ine ndi mwamuna wanga takhala pabanja zaka ziwiri ndipo nthawi yonseyi takhala tikugwiritsa ntchito njira zolera chifukwa mwamuna wanga amati nthawi yoti tikhale ndi mwana sinakwane-titoleretolere kaye kuti tisadzavutike tikadzakhala ndi mphatso ya mwana m’nyumba mwathu. Kunena zoona zimene amati titoleretolere kaye sindikuziona, komanso anthu kunjaku ndiye akumatiseka ndi kumatinyogodola kuti sitibereka. Ine ndiye ndatopa nazo zimenezi.

KB

Mzimba

 

KB,

Nkhani yanu ndi yovuta kuimvetsa, komabe ndikuthandizani. Choyamba, kodi pamene mumagwirizana zomanga ukwati wanu, mudayamba mwakhala pansi n’kukambirana za mapulani anu pa nkhani yokhala ndi ana kapena izi munagwirizana mutalowana kale? Ndikufunsa chifukwa ukwati ndi anthu awiri. Ine ndikuona ngati mwamuna wanu chilipo chimene sakufuna kuti mudziwe ndipo akunamizira kuti nonse mukulera. Zaka ziwiri mukutolera za mwana? Mukutolera chiyani? Mwanena kale kuti palibe chimene mukuona kuti mwatolerapo mpakana pano. Mumufunse ameneyo kuti nthawi yakwana tsopano kuti mulandire mphatso yomwe mwakhala mukuiyembekeza ija. Mumuuze kuti simupanganso zolera koma zenizeni, mumve chimene ayankhe. Ngati pali vuto lomwe akuchita nalo manyazi kukuuzani, mumuuze kuti asaope chifukwa inu ndi thupi limodzi-mavuto ake ndi anu omwe. Kuli asing’anga odziwa kusula kunja kuno! Akakanika, kuchipatala amathandizanso! Ndani safuna mwana?

 

Sakundilankhula

Zikomo Anatchereza,

Ndili pabanja ndi mkazi wina ndipo timakondana kwambiri. Koma akwawo sagwirizana nawo ndipo ngakhale akumane panjira salankhulana. Ngakhale ine ndikawalankhulitsa sandiyankha. Ndichitenji chifukwa ndikuopera mawa atadwala kapena kumwalira kumene. Thandizeni.

MN,

Mzuzu

 

Zikomo MN

Pamayenera kukhala mgwirizano wa mbali zonse. Ngati mgwirizanowu palibe, banja siliyenda bwino. Izitu nthawi zambiri zimachitika chifukwa awiri okondana adangotengana popanda akuchimuna ndi akuchikazi kugwirizana ndi ukwatiwo. Choncho mpovuta kuti tikulangizeni chifukwa chomwe chidatsitsa dzaye sichikudziwika. Mwinatu mkazi wanuyo ndiye akudziwa bwino pomwe padakhota nyani mchira ndipo ndiye angathandize kuti chiyanjano chikhalepo ndi abale akewo. Monga mwaneneratu apa china chitachitika ndiye kuti mudzasowa mtengo wogwira. Choncho langizo langa likhala lakuti mungomusiya mkaziyo kapena muyendetse dongosolo lonse bwino. n

Share This Post