Anatchezera

Ndimufunsirebe?
Ndine mnyamata wa mu Lilongwe ndipo ndidagwa m’chikondi ndi msungwana wina. Ndakhala ndikuponya mawu kwa iye koma iyeyo amayankha moti savomera kapena kundikana. Kodi ndipitirizebe kumufunsira? Ndithndizeni ndazunzika maganizo.
B,
Lilongwe.

Zikomo B,
Ndikuyankha molingana ndi kuti siunandiuze kuti wakhala nthawi yaitali bwanji ukuyesa mwayi wako.
Zikuoneka kuti msungwanayo sanapange chiganizo chokulola kapena kukukana. Nthawi zambiri msungwana akakhala m’malingaliro otero n’chifukwa chakuti akukukayikira. Chikaikochi chikudza chifukwa pali zina zimene adamva za iwe ndiye akadali kulingalira kuti apange chisankho payekha.
Komanso iweyo mwina chidwi chako ukungoonetsa kuti ukumufuna. Tsono akalola, chotsatira chidzakhala chiyani? Mwinatu msungwanayo malingaliro ake ndi akuti akufuna kupeza mwamuna wa banja pamene iwe ukungoonetsa zizindikiro za chibwenzi basi.
Pomaliza ndiyenera kukuuza kuti ngati wayesa kumufunsira koma siukulandira yankho loyenera, bwanji osayamba wakhala mnzake nkumacheza zina ndi zina? Akuyenera kukumvetsetsa kaye kuti umaganiza chiyani, nanga umafuna chiyani asanakulole. Izo ndiye udziwe.
Mbali inayi, ungodziwanso kuti fupa lokakamoza limaswa mphika choncho ngati watha nthawi yaitali ukuyendera, ndi bwino kuyang’ana kwina. Nthawi siyibwerera.

Wokwatira wandipatsa mimba
Zikomo Gogo,
Ndinapanga chibwenzi ndi mwamuna wina amene ankaonetsa Chikondi kwambiri pa ine.
Izi zili choncho, mwamunayo sanandiuze kuti ndiwokwatuira koma nditamva kwa ena ndidamufunsa adayankha kuti akufuna kumusiya ndipo andikwatira ineyo.
Inetu ndili pasukulu ndipo zisanatheke zoti andikwatirezo, wandipatsa mimba pano akuti ndizikhala kwathu ndipo azingondithandiza.
Kodi ndipange bwanji pamenepa.
VD,
Chiradzulu.

VD,
Ndi ambiri asungwana ndi amayi amene ali ndi nkhani zotere. Zagwa zatha, ukuyenera kuyang’ana kutsogolo.
Pali zinthu ziwiri zimene ndingakulangize. Choyamba, udziwe kuti ngati wakupatsa mimba, nkhaniyi ukuyenera kuitengera kukhoti la majisitileti. Malamulo atsopano a ukwati akusonyezeratu kuti wopereka mimba n’kuthawa akuyenera kubweretsedwa pamaso pa oweruza.
Kukhotiko n’komwe akatambasule kuti akuyenera kukuthandiza motani.
Chachiwiri chimene ndinganena n’chakuti usataye mtima kulekeza sukulu panjira chifukwa uli ndi pathupi. Osataya pathupipo monga ena angaganizire. Ukuyenera kukabereka ndipo ukalera ndi kuyamwitsa mwana wakoyo mwakathithi, udzabwerere kusukulu.
Sukulu ndi tsogolo lako lowala ndipo udziwe kuti udzatha kuthandiza bwino mwana wakoyo moti bamboyo adzachita manyazi. Koma osaiwala kutengera nkhaniyi kukhoti.
Andipatse mimba?
Agogo,
Ndinali ndi chibwenzi chimene ndakhala nacho zaka 4 ndipo takhala tikugwirizana za ukwati.
Koma posakhalitsapa anangosintha n’kumanena kuti akufuna andipatse mimba koma adzandikwatira zaka ziwiri zikubwerazi. Kodi pamenepo pali chikondi? Chonde ndithandizeni.
RC,
Mzuzu.

RC,
Apa palibepo chikondi. Akupatse mimba ya chiyani? Adzakukwatira zaka ziwiri zikatha chifukwa chiyani? Zaka 4 zonse zapitazo asanakukwatire akufuna chiyani?
Udabwe nazo. Kodi anatu amayenera kukhala mphatso ya m’banja ngakhale ena angathe kukhala ndi chisankho chokhala ndi ana a mwamuna kapena mkazi amene sanakwatirane naye.
Choti udziwe, amuna ena amangofuna kukupusitsa. Uyu akhoza kukhala mmodzi mwa amuna otere. Nanga mpaka kukuuza kuti akufuna kukupatsa mimba? N’kutheka iyeyo akuuzanso akazi ena atatu chimodzimodzi. Tsono udzatani nonse mukalolera kutenga mimba kuchoka kwa iye?
Khala pansi, sunthapo phanzi asakutaire nthawi.
Kuthokoza
Ndikuthokoza kwa onse amene ananditumizira mauthenga palamya kundifunira mafuno abwino a chaka talowachi. Ndikuti zikomo. Inetu Gogo Natchereza ndilipo chifukwa inunso mulipo, choncho ndimasangalala ndi chikondi chimene mumandionetsera. Mulungu azikudalitsani masiku onse a moyo wanu.  n

Share This Post