Anatchezera

Ndikufuna sukulu
Zikomo Anatchereza,
Ndine msungwana wa zaka 19. Sindidakwatiwepo, ngakhale sukulu ndidaisiyira Fomu 1 zaka zutatu zapitazo.
Sukuluyo ndidasiya chifukwa chosowa ndalama chifukwa makolo anga adasiyana ndipo sangathe kundithandiza.
Padakali pano ndikugwira ntchito m’nyumba ya munthu. Izi ndidapanga chifukwa anthu amandiuza kuti ndikwatiwe koma ine sindimafuna zimenezo. Ndimafuna kudzakwatiwa ntakonza tsogolo lowala.
Chikundivuta ndi nkhani imene ndili nayo patsogolo langa. Nditani kuyi tsogolo langa likhale lowala.
MN, Thyolo.

MN,
Ndathokoza polemba uthenga wanh wogwira mtima. Ndihamike chifukwa cha luntha lanu pofuna maphunziro. Si asungwana ambiri amene ali paumphawi amene amaganiza momwe mukuchitiramu.
Si zoona kuyi kulowa m’banja ndiye kuthana ndi mavuto. Mwinanso kumakhala kuonjezera mavutowo chifukwa kumakhala kosavuta mwamuna kuzunza mkazi amene akumuona kuyi alibenso kolowera.
Popeza mwanena kuyi mukugwira ntchito, langizo langa likhoza kukhala lakuyi, simungagwiritseko gawo lina la ndalama zimene mukulandira polipira sukulu?
Mutabwerera kusukulu, ngakhale mukugwira ntchito, zikhoza kuthandiza. Alipotu ambiri amene leto lino akuvhita bwino koma sukulu adaphunzira akugwira pakhomo la munthu.
Chofunika nkuwagoyokozera bwino abwana kapena adona anu kuti sukulu siyikulepheretsani kugwira bwino ntvhito pakhomo lawo. Zabwjno zonse.

Nsanje yakula
Anatchereza,
Poyamba ndithokoze chifukwa cha kwanu kutithandiza pamavuyo amene timakumana nawo.
Ndili ndi chibwenzi chimene chakhala chikunena kuti chidzandikwatira mu 2017. Koma akangomva kankhani kakang’ono, amakhumudwa ndipo amathetsa chibwenzi.
Izi zakhala zikuchitika kanayi konse. Nkhani yalero ndi ya pa Facebook, pomwe mnyamata wina wandiyamikira momwe ndikuonekera lachithunzi china.
Bwenzi langayo akuchita nsanje kuganiza kuti ndijuyenda ndi mnyamatayo koma ayi.
Chonsechotu ndidamupatsa password yanga kuti aziona ngakhale mauthenga anga obisika. Zikundisowetsa mtendere nditani.
GK, Mulanje.

GK,
Mwamunayo wamukonda, mpaka kumupatsa password! Chikondi chiyenera khbwezeredwa. Kodi iyeyo adakipatsa password yake?
Ena amati nsanje ndi maziko a chikondi koma nsanje ina inyanya. Nsanje ina I asonyeza kuti wochita nsanjeyo ndi kamberembere chifukwa amaganiza kuti zimene amachita ndiye kuti enanso akateto zili choncho.
Mwachitsanzo, mwina iye naye amauza asungwana ena kuti zithunzi zawo zikumusangalatsa nchokinga  chakuyi awakope tsono akuona ngati mnyamata aliyense akakuuza chimodzimodzi ndiye kuti nayenso akufuna kukukopa. Pomwe si zili choncho.
Tsono ichi ndi chibwenzi. Mukadzakwatirana, nsanje yotere idzafika pati? Muzidzapita kuchigayo inu? Kuntchito sadzachitira nsanje abwana anu ameneyu? n

Share This Post