ANATCHEZERA

Adandichotsa ntchito

Zikomo Gogo

Ndakhala ndikugwira ntchito kwa bwana wina mumzinda wa Blantyre kwa zaka 4. Masiku apitawa ndidaapempha holide ya masiku 10 ndipo bwanawo adavomera. Koma ndili kopuma, bwanawo adandiimbira foni kuti andichotsa ntchito ndipo palibe ndalama zimene angandipatse. Ndichitenji chifukwa ku ofesi yolemba anthu ntchito ngakhalenso kukhoti ya makampani koma sindinathandizidwe? Mutu waima.

BMW,

Blantyre.

BMW,

Ili likhale phunziro kwa tonse kuti pamene tikuyamba ntchito, tiyenera kuunikirana bwino lomwe zomwe ziyenera kuchitika pamene ntchito ikutha. Malamulo a zolemba anthu ntchito akuneneratu kuti ngati bwana akuchotsa wantchito wake, ayenera kumuuza kuti amuchotsa pakutha pa masiku 15. Awa ndi antchito amene amalandira malipiro otsika kwambiri.

Chimodzimodzi, munthu siungangodzuka lero n’kunena kuti bwana ndasiya ntchito. Uko ndi kuphwanya malamulo.

Tsono mwati adakuchotsani muli kutchuti. Tchuti ndi gawo la ntchito yanu ndipo sikuti bwana akukuchitirani chifundo. Ndi gawo limodzi la ntchito.

Munthu ngati ukusiya ntchito, ndipo uli ndi masiku amene mumayenera kupita kuntchito, masikuwo mumawerengera ndipo mukhonza kusiya ntchito pompompo.

Chofunika kwambiri ndi kukambirana ndi amene akukulembani ntchito musanayambe ndipo ngati n’kotheka musayinirane. N’kutheka apa kuti ku labour office kapena khoti ya makampani simungaphule kanthu chifukwa palibe umboni wa zomwe mudagwirizana.

Apachibale akundifuna

Anatchereza,

Pali anyamata awiri a pachibale amene akuoneka kuti amandifuna. Mmodzi mwa anyamatawo ndidamudziwa kalekale ndipo wakhala akundifundira koma ndimamukana.

Ndidadziwana ndi winayo chifukwa cha mbale wakeyo ndipo nsye akunditumizira mauthenga a chikondi, ati akundifuna. Ndichitenji, chifukwatu awiriwo akundisowetsa mtendere.

M.E.

Mponela

ME,

Ngati anyamatawo simukuwafunadi ndi bwino kuwauziratu, mmalo mowapatsa banga kuti aziganiza kuti mwayi ukadalipo.

Mwinatu inuyo simutsindika kukana kwanuko. Komanso nkutheka kuti anyamatawo ndi nkhakamira. Mwinanso ali pampikisano kuti aone angakutengeni ndani.

Muli monsemo, mphamvu zili m’manja mwanu, kulola kapena kukana.

Ana owapeza avuta

Zikomo Anatchereza,

Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye m’banja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga.

Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7.

Ndapirira mokwanira, ndithandizeni.

WL,

Lilongwe.

WL,

Musanachite chilichonse pabanja mumayenera kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu.

Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo.

Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja.

Khalani pansi nkumanga mfundo imodzi. Ndi ana ndi abale ati amene ayenera kuchoka pakhomopo ndipo ndi angati amene ayenera kuchoka?

Mukuyembekezera mwana wanu, kusonyeza kuti udindo wanu ukukula. n

WOFUNA BANJA

Ndili ndi zaka 26 ndipo ndikufuna sugar mummy wa ku Lilongwe. 0882673184

Share This Post