Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Akundifunanso

Anatchereza,

Telemu yotsiriza ya Fomu 3 ndidapalana ubwenzi ndi mtsikana wina pasukulu yathu ku Mulanje. Koma tikuyandikira kulemba mayeso a Fomu 4, bwenzi langalo lidanditumizira uthenga palamya kundiuza kuti chibwenzi chatha chifukwa sindine ‘mwamuna’.

Iye adaonjezera kuti pomwe ankandilola n’kuti ali ndi chibwenzi china. Izitu zidandiwawa kwambiri chifukwa tinkalonjezana kuti tidzakwatirana.

Chondivuta n’choti atangomva kuti ndayamba ntchito adayambanso kundiimbira foni n’kumandiuzakuti chikondi chake pa ine sichidathe. Ndichite chiyani pamenepa?

DF,

Mulanje.

DF,

Nthawi zonse ndimalangiza amene ali m’sukulu kuti ayenera kupewa mchitidwe wokhala ndi zibwenzi. Izi ndimanena makamaka chifukwa zimasokoneza maphunziro. Taonani apa mukuti mtima wanu udasweka mutayandikira kulemba mayeso a Fomu 4 mkaziyo atathetsa chibwenzi.

Sindikukaika konse kuti izi zidakhudza momwe mudakhonzera mayeso a Fomu 4. Simukadakhonza kuposa momwe mudachitira mutakhumudwa ndi kuthetsa kwa chibwenzi kumene mudakumana nako.

Tsono funso lanu mukuti muchitenji? Langizo langa ndi loti, musataye nthawi ndi mtsikanayo chifukwa waonetseratu kuti ndi wamadyeramphoto komanso ali ndi mtima wa chimasomaso. Adakuuzani kuti adakulolani ngakhale adali ndi chibwenzi china panthawiyo. Tsono, muli ndi chitsimikizo chotani kuti mukadzakwatirana naye sakapezanso mwamuna wina wamseri?

Taonani adati inu si mwamuna pomwe amathetsa chibwenzi. Tsopano akukusakani chifukwa mwapeza ntchito. Kodi mutakwatirana naye, ntchitoyo n’kutha ameneyo sadzakuthawani? Samalani naye mkazi wa chimasomaso!

Zikomo Gogo,

Ndidapanga chibwenzi ndi mkazi wina yemwe ali ndi mwana mmodzi. Chithereni ukwati wake woyamba, patha chaka ndi miyezi ingapo. Mgwirizano wathu ndi woti tidzamange banja.

Koma tsiku lina ndikuchokera kuntchito ndidangolowa m’nyumba osagogoda ndipo ndidamupeza akulankhula pafoni. Adadzidzimuka n’kudula foniyo koma nditamulanda ndidaona kuti amalankhula ndi mwamuna wake woyambayo.

Ndidamuuziratu kuti chibwenzi chatha ndipo azipita kwawo. Adagwada n’kulira kunena kuti ndimukhululukire sadzayambiranso. Iye adati mwamunayo amaimba kufuna kudziwa njira yopita kwa mayi anga kuti akaone mwana.

Ndichitenji, mundiyankhe pafoni pomwepa.

G,

Lilongwe

Zikomo a G,

Poyamba, ndikukumbutseni kuti ndi zovuta kuti aliyense amene wandifunsa ndi zimuyankhanso pafoni. Izi zili choncho chifukwa ndimalandira mafunso ambiri choncho kuti aliyense ndizimuyankha pafoni sizingatheke. Palinso ena amafulasha, tsono ine kuti ndiziimbira aliyense amene akufulasha, ndiwo ndigula?

Tsono kubwera ku funso lanu, poyamba ndikudabwa kuti mukukhala bwanji ndi mkazi amene simunalongosole zaukwati? Kodi mutapatsana mimba, sipakhala mavuto ena?

Izi zili choncho, mudziwe kuti mkaziyo akunama kuti amapereka njira ya komwe mayi akukhala kwa mwamuna wake wakale. Tiziti nthawi yonse adali limodzi, mpaka mwana mwamunayo samadziwa pakhomo pa mayi a mkazi wake?

Akadakhala kuti amakambirana za njira bwanji adadula foniyo? Samalani.

Ofuna mabanja

Ndikufuna mkazi koma akhale wa zaka 17.

Pepani sindiika nambala yanu chifukwa mwati mukufuna mkazi wa zaka 17. Ameneyo si mkazi koma mtsikana ndipo malamulo a dziko lino akuletsa kuti ana osakwana zaka 18 asamakwatiwe.

Ndine mwamuna wa zaka 28 ndipo ndili pantchito ku Lilongwe. Ndikufuna mkazi wopanga naye ubwenzi mpaka banja. 0888873265/0995036970

Ndili ndi zaka 34 ndipo ndikufuna mkazi wokonda kupemphera. Akhale wa zaka za pakati pa 24 ndi 34. 0885662144

Ndili ndi zaka 26 ndipo ndikufuna mkazi womanga naye banja kuno ku Lilongwe. 0881527637

Ndili ndi zaka 31 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka 29 kapena 30. 0881391631

Related Articles

Back to top button