anatchezera

Akundidabwitsa

Anatchereza,

Ndili pa chibwenzi ndi mwamuna wina. Chomwe chimandidabwitsa n’choti nthawi zonse ndikamuimbira foni usiku samayankha.

Ndikamufunsa amati idali kotchajitsa. Gogo ndikuona ngati mwamunayu akundiyenda njomba ali ndi mkazi wina ndipo akuopa kuti akayankha amudziwa kuti ali ndi chibwenzi.

Ndithandizeni,

PK,

Ndirande,

Blantyre.

PK,

Ndikadakuthandizani mokwanira ndikadziwa kuti chibwenzi chanu chidayamba bwanji. Nanga mwakhala zaka zinga muli pa chibwenzi?

Nanga mwamunayo ali ndi wa zaka zingati? Amakhala kuti? Ndindani? Nanga amachita chiyani?

Ndalankhula izi kaamba koti ndikuona ngati simukumudziwa bwino.

Nthawi zambiri atsikana ambiri safufuza mokwanira asanamulole mwamuna makamaka munthuyo akakhala wachikulire.

Zotsatira zake amakagwa m’chikondi ndi mwamuna wa mwini wake zomwe zimaika pachiopsezo miyoyo ndi tsogolo lawo.

Ndikupempheni kuti mumufufuze bwino mwamunayu ndi kupeza zoona zake musadachite chilichonse.

Chitani izi mwachangu kuopa kudzanong’oneza bondo mtsogolo.

Natchereza

Ndithandizeni

Gogo Natchereza

Ndidakumana ndi mtsikana wina yemwe nditamuona mtima wanga udakhutira kuti ndi mkazi amene ndimafuna atakhala mayi wa ana anga.

Takhala tikuimbirana foni, komanso kuyenderana kwa zaka ziwiri.

Koma chodabwitsa n’choti ndikamufunsira amakana.

Ndikamufunsa chifukwa chomwe wakanira safotokoza.

Gogo, ndithandizeni. Mtsikanayu ndimamukonda, ndiwokongola, waulemu, wochezeka, komanso wodzilemekeza.

JKJ

Mchinji

JKJ

Chikondi chimapilira, chimaleza, komanso sichipsa mtima.

Mpatseni nthawi mtsikanayu mwina mtsogolo muno zidzayenda.

Ndikadakonda mudafufuza mbiri yake. Atsikana ena amaopa kukwatiwa kapena kukhala pa chibwenzi chifukwa cha zomwe adakumana nazo kapena anzawo ndi abale awo adakumana nazo.

Kambiranani mwina atha kumatsuka n’kukuuzani chomwe chimamuchititsa.

Natchereza

Ofuna banja

Ndikufuna mkazi womanga naye banja. Akhale wa zaka za pakati pa 30 ndi 39, wopemphera, koma yemwe adapezeka ndi kachilombo ka HIV. 0883164130/ 0995268735

PPX

Ndikufuna mkazi

Ndithandizeni ndikufuna mkazi. Ndine mnyamata wa zaka 34 ndipo ndimachita bizinesi. Mkaziyo ayimbe foni iyi 0991 711 433.

AKP

Share This Post