Chichewa

anatchezera

Listen to this article

Akuti tibwererane
Anatchereza,
Ndinali pambanja ndi mwamuna wa ku Nsanje ndipo ndili naye mwana mmodzi. Koma ndikati tiyeni tikaone kwanu amangoti tidzapitabe chikhalireni palibe ndi tsiku ndi limodzi lomwe abale ake anabwerapo pakhomo pathu ndiponso banja lathu ndi losagwirizira chinkhoswe. Kumudzi kwathu mwanuna wangayu amakananso kukaonako. Panopa tinasiyana chifukwa samagona m’nyumba. Mowa samwa komanso fodya sasuta. Ndiye panopa akukakamira kuti tibwererane, apo bii ndimupatse mwana wake, koma ineyo ndikukana. Gogo, ndithandizeni. Nditani pamenepa?

Mwati mudali pabanja, koma banja lanu padalibe chinkhoswe? Ndiye lidaali banja lotani lodziwa awiri nokhanu? Apa mukuchita kudabwa kuti a kwawo kwa mwamuna wanu sadabwerepo pakhomo panu ngakhale tsiku limodzi—akadabwerapo bwanji ngati akukudziwani? Munasiyana koma pano mwati akukakamira kuti mubwererane, pachifukwa chiti?
Mwachidule, ndinene kuti mmphechepeche mwa njovu sapita kawiri. Kubwererana ndi mwamuna wotere kuli ngati galu kubwerera kumasanzi ake—palibe chanzeru. Koma ngati watsimikiza kuti amakukonda ndipo nawenso umamukondabe, ulendo uno muyesetse kuti akwawo ndi akwanu akumane ndi kukambirana kuti pakhale dongosolo lenileni, chinkhoswe kenaka ukwati wovomerezeka ndi mbali zonsezonse. Pokhapo ndiye kuti mutha kumanga banja, osati zachibwana zimene mudachita kupatsana mwana kenaka wina aziti tibwererane apo bii undipatse mwana wanga. Banja si masanje, chonde!
Zikomo,
Natchereza

Akuthawathawa
Anatchereza,
Mwezi wa April 2011 ndinapeza mwamuna ndipo sindinagonane naye kufikira 6 July 2012 pamene tinakaonekera kwa makolo a tonse. Tsiku limneli andiuza kuti tigonane koma ndinawauza kuti tikayezetse kaye HIV koma adakana ponena kuti iwo ndi blood donor choncho ndisawakaikire ndipo zinatheka. Titasiyana tsiku limenelo adandiuza kuti tikadziwe komwe amagwira ntchito ku Zomba. Nditapita andiuza kuti ndisabwererenso tiyambiretu banja koma ndinakana ndipo ndidabwerera. Patapita masiku adabwera ndi amalume awo kudzafunsira mbeta ndipo zinatheka. Pambuyo pake tidayamba banja ndipo posakhalitsa ndidaima. Mwanunayu adandiuza kuti mmamawa azidya phala ndipo nsima izikhala ya mgaiwa. Chodabwitsa chinali choti phala likafika patebulo limasintha mtundu kukhala lobiriwira (green) koma kuwafunsa samandiyankha zomveka. Nditalimbikira anandionetsa mabotolo awiri momwe munali zinthu za ufa za green koma anakana kundiuza ntchito yake, ati sizimandikhudza. Tsiku lina ananditenga kuti tikayezetse magazi koma titafika kumneko anandiyeza ndekha ati iwo adyezetsa kale. Anandipeza ndi kachilombo ka HIV. Kuyambira tsiku lomwelo anandiuza kuti banja latha ndizipita kwathu. Ndinakatula nkhaniyi kwa amalume awo koma palibe chikuchitika. Nditani?
M

Zikomo M,
Sindidziwa kuti kachilombo ka HIV mudatatenga bwanji, koma sindikukaika kuti mwamuna wanuyo ndi amene adakupatsirani kachilomboko ndipo zikuonetseratu kuti amachita izi uku akudziwa kuti ali ndi HIV. Ndatero chifukwa cha zochita zake—akuonekeratu kuti alibe chilungamo m’zochitika zake. Nanga timabotolo ta mankhwala obiriwira amathira m’phalato n’tachiyani? Nanga amakana kukayezetsa chifukwa ninji? Pano inu mwapezeka ndi HIV akuti banja latha, zoona?
Ndithu, ngati iyeyo adali walungalunga, akadatha kuchitapo china chake kuonetsa kuti wakhumudwa kuti inuyo ndi amene mwamupatsira kachilomboko. Pali malamulo m’dziko muno, oti wina akapatsira mnzake kachilombo ka HIV mwadala, ameneyo ali ndi mlandu. Ndithu, pitani nayoni nkhaniyi kwa odziwa malamulo kuti akuthandizeni.
Natchereza

Related Articles

Back to top button
Translate »