Chichewa

ANATCHEZERA

Listen to this article

Adatidyera ndalama

Zikomo gogo,

Timakumana banki ya m’mudzi pakhomo la mayi wina yemwenso adakakamira kuti azisunga ndalamazo. Iye adatenga ndalamazo ndi kuchitira chinkhoswe. Litakwana tsiku logawana adati amukawa achitaka ndipo adati tisonkhe. Titasonkha adati sizidakwane, tikuyenera kusonkhanso ndalama zina chifukwa imaperewera K170 000. Titani?

BCA,

Karonga.

BCA,

Kaneneni kupolisi basi. Uku n’kuba mopusitsa. Palibenso china chimene mungachite. Ndipo mudalakwa kusonkhanso ndalamazo.

 

Amagwiranagwirana

Zikomo gogo,

Ndili pachibwenzi ndi mkazi wina amene amakhala ku Blantyre pomwe ine ndili ku Balaka. Nthawi zina bwenzi langalo amapita kwa mnzanga komwe amagwiranagwirana. Zikatero mnzangayo amandiuza zonse zinachitika. Kodi mnzangayo akundikonda?

BK,

Balaka.

BK,

Funso lisakhale lakuti kodi mnzanuyo akukukondani, koma kuti kodi mkazi wanuyo akukukondani? Ayi ndithu, ndipo mukadakhala ena mukadangomusiya. Mukhoza kutuma anthu ena afufuze ngati mnzanuyo amachita izi ndi bwenzi lanulo. Chifukwatu akhoza kukhala kuti akungofuna kuti musiyane. Apatu mukamati amagwiranagwirana mukutanthauzanji? Zingatheke izo? Ndikuonatu ngati amenewo amapitirira mpaka kuchita zachiwerewere. Samalani, phukusi la moyo sakusungira ndi mnzako.

 

Ndikufuna ana anga

Ndili ndi zaka 20 ndipo banja ndi mkazi wanga lidatha tili ndi ana awiri. Anawo ali kwa agogo akuchikazi koma ndikati ndikawatenge amandikaniza. Komanso kodi banja likatha ana apita kumpingo wa mayi awo kapena bambo awo?

SF,

Dowa.

SF,

Nchifukwa chake ambiri amalimbikitsa kuti ndi bwino kukwatira munthu wolingana naye zikhulupiriro: ana sachita kusankha kuti apite mpingo wa bambo kapena mayi awo. Nanga inu banja lanu mudamangitsa bwanji? Pomwe limatha mgwirizano udali woti ana apite kuti? Nanga chisamaliro cha kholo linalo chizikhala motani? Dziwani kuti ngakhale banja lithe, makolo a anawo ndi omwewo basi, choncho ndi ufulu wanu kuwasamalira mwanjira iliyonse. Kaneneni nkhaniyi kwa ankhoswe anu ngakhalenso kupolisi yoyang’anira za m’banja.

 

Tibwererane?

Anatchereza,

Ndidali ndi chibwenzi pamene ndinkakhala ku Mzuzu. Koma nditasamukira ku Lilongwe ndidamva kuti amayenda ndi mphunzitsi wina. Nditamufunsa amayankha zosalongosoka ndipo adathetsa chibwenzi. Koma pano akuimba foni ati ndimukhululukire. Tsono nditani poti ndidapeza wina?

R,

Lilongwe.

 

R,

Ndimanena kawirikawiri kuti kukhala kutali nthawi zina kumachititsa chikondi kuzilala. Poti mwati mudapeza wina, pitirizani ndi ameneyo chifukwa simukudziwa chifukwa chimene akufuna kuti mubwererane. Nkutheka kuti pano ndi mphunzitsiyo zasokonekera. Mtsogolo mwabwino, kumbuyonso kwabwino.

 

Ndamuonongera zambiri

Zikomo gogo,

Ndidakhala pachibwenzi ndi mkazi wina kuyambira 2010 mpaka 2013. Adathetsa chibwenzi mu 2014 pomwe ankandinamizira kuti ndili ndi mkazi wina. Pano amandiimbira kupempha zosiyanasiyana ndipo ndimamugulira koma ndikamuuza kuti tikumane amati watangwanika. Nditani, ndamuonongera zambiri.

JS,

Lumbadzi.

JS,

Pomugulira zinthuzo mumati mukutani? Apatu sindingakuikireni kumbuyo chifukwa mukudziwa chimene mukuchita. Ndingonena kuti onani momwe ndayankhira R pamwambapa.

 

Ofuna mabanja

Ndili ndi zaka 36 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndikufuna mwamuna wa zaka za pakati pa 40 ndi 45 womanga naye banja. 0995249329

 

Ndimakhala ku Thyolo ndipo ndikufuna mkazi wa digiri wa zaka 18 mpaka 25. 0884081949

 

Ndili ndi zaka 25 ndikufuna sugar mummy. 0882535844

 

Ndili ndi zaka 43 ndikufuna mkazi wa zaka 25 mpaka 35 wapantchito ndipo akhale wokonzeka kukhala ku Zomba. 0996492161

Related Articles

Back to top button