Chichewa

Ankadziwana ndi mayi anga’

 

Kale makolo amachita kusankhira ana awo munthu wokwatirana naye, koma pano zinthu zidasintha ngakhale kuti makolowo akhoza kungokhala muni wowalitsa kuti ana aonane n’kukondana.

Anthu ambiri apezapo mabanja chifukwa chakuti makolo awo kapena abale awo ena amachezera limodzi ndipo kudzera mukucheza kwawoko ana awo adaonana ndi kukondana mpaka lero ndi banja.

Lucky ndi Sheira patsiku la chinkhowe
Lucky ndi Sheira patsiku la chinkhowe

Njira ngati iyi ndimo lidayambira banja la Lucky Madaika wochokera kwa Chipyali m’boma la Balaka ndi Sheira Kachitseko wa kwa Bubua, T/A Makwangwala ku Ntcheu.

Awiriwa kuti akumane n’chifukwa chakuti Lucky ankapitapita kunyumba kwa Shiera malingana ndi bizinesi yake ya zamakompyuta kukaonana ndi mayi a Sheira ngati kasitomala wake.

Ukutu akuti kudali kumayambiriro a chaka cha 2015 ndipo atapita kangapo kunyumbako, adalephera kuugwira mtima mpaka adapempha nambala ya lamya kuti aziimbirana n’kumacheza koma kenako chibwenzi chidayambika.

“Tidakhala pachibwenzi kwa miyezi ingapo kenako tidaganiza zopanga chinkhoswe ndipo zonse zoyenera monga kukaonekera kumakolo ndi zina zitachitika, chinkhoswecho chidachitikadi ku Area 47 mumzinda wa Lilongwe,” adatero Sheira.

Iye adati m’miyezi 7 ikudzayi awiriwa adzakhala akuvekana mphete, makamaka pa 9 July, 2016 mumzinda womwewu wa Lilongwe.

Lucky adati aiwiriwa amakhulupirira kuti powalenga, Mulungu adakonza kuti adzakhala limodzi poona chikondi chomwe amapatsana komanso akuti pali zambiri zomwe onse amakonda kapena kudana nazo.

Iye adati akufuna banja lake lidzakhale lachitsanzo pamaso pa anthu kuyambira kumudzi kwawo, m’tauni momwe akukhala ndi kumpingo komwe amapemphera ndipo akuti tsiku ndi tsiku amapemphera kuti Mulungu adzawatsogolere kukwanitsa maloto awowa. n

 

 

Related Articles

Back to top button