Chill

‘Ankaperekeza mchemwali wake’

Listen to this article

 

Mulungu wamva pemphero ndi pembedzero la Paul Kamanga, yemwe ndi mtolankhani, komanso wowerenga nyuzi pa MBCTv—mnyamatayu wadalitsika ndi kachiphadzuwa kothwanima bwino.

Njoleyitu ndi Temwanani Chavula, wa m’mudzi mwa Mwahenga kwa Mfumu Mwahenga m’boma la Rumphi ndipo akugwira ntchito ku Medmate Pharmacy. Iyeyu ndi womaliza kubadwa m’banja la ana anayi.

Tsopano ndi thupi limodzi: Paul ndi  Temwanani
Tsopano ndi thupi limodzi: Paul ndi Temwanani

Paul, wa m’mudzi mwa Lufu Nkunika, kwa T/A Chindi m’boma la Mzimba, akuti mwayi udamugwera pamene adathira diso namwaliyu mu 2010 akuperekeza mchemwali wake.

Diso lidakakamira panjoleyi, ndipo mwadzidzidzi adazindikira kuti ikukhalanso ku Nyambadwe mumzinda wa Blantyre, komwe Paul ankakhala.

Ngakhale amati mlenje weniweni sasaka m’khonde, Paul adatchera ukonde kuti asodze namwaliyu ndipo zidathekadi.

“Amaperekeza mchemwali wake yemwe ankakhala ku Zingwangwa [mumzindawu] ndipo tidapatsana moni n’kufunsana komwe aliyense amakhaka,” adatero Paul. Chiyambi cha chibwenzi pakati pa awiriwa chidali chidali chotero koma mwana wa mwamuna adali ndi nkhani ina.

Kupita kwa masiku, mbuto akuti idafumbula ndipo awiriwa adayamba kuyenderana komanso kutherana nkhani mpaka Paul kupeza mwayi wokamba zakukhosi.

Mawuwo achititsa kuti lero tiyambe kukamba kuti awiriwa tsopano ndi thupi limodzi chifukwa mwambo wa ukwati wachitika dzulo kuholo ya St Michael and All Angels mumzinda wa Blantrye.

Related Articles

Back to top button