Nkhani

‘Apezereni obwera chochita, asadzabwererenso ku Joni’

 

Pamene Amalawi ena othawa kuinga anthu a maiko ena kumene kwagundika ku South Africa ati ndi zokhoma zimene aziona sabwereranso ku Joniko, mafumu ena apempha boma kuti lipereke mwayi wa ntchito kwa Amalawi kuti izi zitheke.

Sabata zapitazi, anthu a ku South Africa akhala akuthotha anthu a maiko ena chifukwa ati akuwalanda ntchito, akazi komanso mwayi wochita bizinesi. Ziwawazo zachititsa akunja ena kulandidwa katundu, kuvulazidwa ndi kuphedwa kumene.xeno-6

Potsatira chipwirikiticho, inkosi ya Makhosi M’mbelwa ya ku Mzimba ndi Senior Chief Chimwala ya m’boma la Mangochi apempha boma kuti lipereke mpamba kwa anthuwa woyambira bisinesi kapena ntchito za manja. Mzimba ndi Mangochi ndi ena mwa maboma amene amatumiza Amalawi ambiri ku Joni.

Mafumuwo ati kuchepa kwa malipiro pa ntchito, kusowa kwa ntchito, kukwera mtengo kwa chiongola dzanja anthu akakongola ndalama ku banki, ndi zina mwa zifukwa zomwe adathawira m’dziko muno ndi kukwawira ku South Africa komwe ndalama si nkhani.

Mfumu Chimwala yomwe ana ake atatu ali ku Joni yati boma lionetsetse kuti lapereka mwayi wa ntchito kuti achinyamatawa azigwira kusiyana ndi kukhamukira ku South Africa.

“Achinyamata akhale ndi mwayi wambiri wopeza ntchito komanso maganyu. Boma likakonza izi, mavutowa akhala mbiri yakale. Sindikutanthauza kuti sadzapitanso koma chiwerengero chake chingachepe kusiyana ndi momwe zilili pano,” idatero mfumuyo.

Naye M’mbelwa, yemwe ndi mfumu yaikulu ya Angoni a ku Mzimba, akuti anthuwa sanganeneretu kuti sadzabwerera m’dzikolo.

“Koditu anthuwa amapita kukasaka buledi, ndiye ngati tikufuna kuti asadzapitenso, ndi bwino pakhale malipiro okwera m’makampanimu komanso pakhale mwayi wa ntchito,” adatero iye.

Mkulu wa bungwe la zachuma la Economic Association of Malawi (Ecama) Henry Kachaje akuti Amalawi sadzaleka kupita m’maiko otukuka kukasaka ndalama ngati Malawi sakonza nkhani za chuma.

“Achinyamata sadzasiya kupita m’maiko ena otukuka kukasaka mwayi, pokhapokha Malawi atatukuka pachuma. Nkovuta kusunga wachinyamata m’dziko muno popanda ntchito,” adatero Kachaje.

Iye adati Malawi akuyenera kuchilimika kuti athe kupereka mwayi wa ntchito kwa achinyamata. “Tikuyenera kuthandiza kwambiri maunduna amene angapereke mwayi wa ntchito wambiri monga unduna wa zokopa alendo. Tsoka lakenso palibe chikuchitika chofuna kutukula undunawu,” adatero Kachaje.

Lolemba nduna ya zofalitsa nkhani Kondwani Nankhumwa, Amalawi awiri adaphedwa pa ziwawazo ndipo 3 200 akhudzidwa ndipo ali pamndandanda wobwerera kuno kumudzi. Anthuwa adayamba kufika m’dziko muno Lolemba usiku ndipo akusungidwa ku Blantyre ndi Lilongwe poyembekeza kuti atumizidwe m’makwawo.

Anthu onse amene tidacheza nawo adakana kwa mtuu wa galu kuti sangabwererenso. Mmodzi mwa anthu obwererawa, Yusuf Amidu wa m’boma la Mangochi, akuti amagwira ntchito yowotcherera zinthu kwa munthu wina m’dzikolo. Amidu akuti amalandira K16 000 pa sabata, kusonyeza kuti pa mwezi amapeza K64 000.

Ntchito ngati iyi m’dziko muno ili ndi malipiro osaposera K25 000 pa mwezi malinga ndi Amidu. Iye adati ndalamayo siyingathandize munthu amene ali pabanja.

“Zingathandize boma litaunikira kuti izi zayang’anidwa bwino. Zitatero, palibe ngakhale mmodzi pagululi angabwererenso ku South Africa. Kuli mavuto, timangopitira kuthawa zokhoma kuno,” adatero Amidu amene watha zaka zitatu m’dzikolo.

Zokhoma zimene Amalawi ena akumana nazo si ndizo. Mwachitsanzo, Alick Wyson wa m’boma la Mangochi adaomberedwa pachifukwa. Iye akuti adachitidwa chipongwecho ndi anthu a m’dzikolo pa 24 December chaka chatha.

“Ngakhale Amalawi ambiri akumva za zipolowezo panopa, zidayamba kumapeto a chaka chatha pomwe nanenso ndidaona zokhoma,” adatero iye.

Zione Khombeya amene ali ndi pathupi pa miyezi 7 akuti adathamangitsidwa m’nyumba mwake madzulo pamene amati aziphika chakudya.

Gulu la anthu limene limasaka obwera akuti lidayamba kuthethetsa anthu amene si mbadwa za dzikolo ndipo iye limodzi ndi mwamuna wake adathawa ndi kukabisala. Adavulazidwa mwendo pothawapo.

Evelyn Thumba wa m’boma la Thyolo adamuvulazanso mwendo pamene amathawa. Pamene amatsika pa Kamuzu Stadium, miyendo yake idali yotupa ndipo adafikira m’manja mwa achipatala.

Aka sikoyamba kuti zipolowe zotere zibuke ku South Africa. Mu June 2008, dziko la South Africa lidachitiranso mtopola alendo a m’maiko ena amene akukhala m’dzikolo ndipo anthu 60 adaphedwa pamene anthu oposa 600 adavulazidwa.

Dziko la Malawi lidakatengako mzika zake zoposa 1 000 kaamba ka ziwawazo koma zipolowezo zitazizira, khamu la anthu lidabwereranso m’dzikomo.

Koma Nankhumwa akuti padakali pano boma laponya maso ake populumutsa mzika zomwe zikuvutika ku South Africa ndipo zina zonse zibwera pambuyo.

Nankhumwa akuti boma lili ndi ndondomeko zambiri zomwe lakonza zofuna kuthandizira anthuwa.

“Maso athu ali powapulumutsa kaye ndipo zina zonse zitsatira. Sikuti tangokhala,” adatero iye.

Kutsatira chipwirikiticho, dziko la Malawi lidayamba kututa nzika zake kuyambira Lolemba pamene anthu 390 adatengedwa pa mabasi 6 amene adafikira pabwalo la  Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.

Nankhumwa adati pakufunika mabasi ena 15 kuti akatenge anthu ena amene atsalira m’dzikomo pamene chiwerengero cha Amalawi amene akhudzidwa chidakwera kufika pa 3 200. n

Related Articles

Back to top button