Nkhani

APM wakwanitsa masiku 100 lero

Akatswiri owona mmene nkhani zandale, chuma ndi zina zikuyendera m’dziko muno komanso anthu wamba ati masiku 100 amene mtsogoleri wa dziko lino Pulezidenti Peter Mutharika wakhala ali pampando wolamulira dziko aonetsa kuti mtsogoleriyu ndi wamasomphenya ngakhale Amalawi ambiri, maka akumidzi, adakalibe munsinga za umphamwi.

Ndemangazi zikudza pounguza ulamuliro wa Mutharika m’masiku 100 amene wakwanitsa ali pampandowu.

Pa 30 May chaka chino, bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (Mec) lidalengeza kuti Mutharika ndiye adapambana pachisankho cha pa 20 May. Iye adalumbiritsidwa tsiku lotsatiralo, zomwe zikusonyeza kuti lero pa 6 September watha masiku 100 akulamulira dziko lino.

Pamasikuwa zingapo zachitika monga kuweyeseka kwa chitetezo m’dziko muno pamene umbanda wafika posauzana.

Chitsanzo mwezi wokha wa June ndi July chaka chino kudaphedwa anthu oposa 51 ndi achifwamba oba ndi zida zoopsa kuphatikizapo mfuti. Komanso kwachuluka kuba ndalama m’malo opempherera, m’mashopu, m’makampani komanso m’nyumba za anthu. Posakhalitsapa mfumu ina kwa Madziabango m’boma la Blantyre idaphedwa ndi mbava.

Zina zomwe zachitika ndi nkhani za ulamuliro wabwino, zandale, umoyo wa Amalawi komanso zachuma cha dziko lino zomwe akatswiriwa akuti chisonyezo chilipo kuti zinthu zisintha, koma apemphabe boma kuti likonze momwe mwatsalira.

Mphunzitsi wa ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Blessings Chinsinga, akuti zabwino zomwe Mutharika wachita pamasikuwa n’zochuluka ngakhale zolakwika zizidalephere.

“M’masiku 100 taona [Mutharika akuchititsa] misonkhano yandale iwiri yokha basi; wayenda maulendo akunja ochepa; taona wachiwiri wake akugwira ntchito ndi ogwira ntchito m’boma, zomwe zikuthandiza kuti zachinyengo zichepe. Tili ndi ubwino wochulukirapo womwe taona panthawiyi,” adatero Chinsinga polankhula ndi Tamvanim’sabatayi, koma adatinso ulamulirowu pena waponda Amalawi pachilonda.

“Adalonjeza kuti kabineti ichepa, inde idachepadi koma taonani alangizi mmene achulukiramo. Uku n’kungofuna kumwaza misonkho ya anthu mosasamala. Onaninso momwe ogwira ntchito m’boma akuwachotsera, zomwe zikusiyana ndi zomwe adalonjeza panthawi ya kampeni. Izitu sizikusiyana ndi ulamulo wapita uja,” adatero mkuluyu.

Chinsinga adati akadakhala mayeso, Mutharika akadadya 6 pa 10.

Koma mkulu wa bungwe la ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), John Kapito, adati masiku 100 ngochepa kuweruza boma la Mutharika kumbali ya kagulidwe ka zinthu komabe wati bomali layesetsa pakasamalidwe ka misonkho ya Amalawi.

“Nduna n’zochepa komanso mtsogoleri sakuyenda monga zidalili poyamba. Tayamba bwino, komabe tikudikira kuti tione mfundo zomwe aponya m’ndondomeko ya zachuma ngati ipindulire anthu,” adatero Kapito, napereka [very good] 9 pa 10 kwa mtsogoleriyu pazomwe wachita m’masikuwa.

Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen), Martha Kwataine, adati pamasiku 100 sipadaoneke kusintha kwenikweni kumbali ya zaumoyo chifukwa cha mavuto amene bomali lidawapeza.

Iye adati bomali laonetsa chidwi kuti likufuna kusintha nkhani za umoyo.

“Bomali lapeza mavuto ambiri, makamaka pankhani ya zachuma, ndiye kudali kovuta kuti mbali ya umoyo ikonzedwe. Komabe taona akulankhula ndi amabungwe kuti ndi ndalama zingati zikufunika kuti nkhani za umoyo ziyambe kuyenda bwino.

“Bola asamangolankhula koma kuchita malinga ndi mawu awo. Sitikufuna kungowapaka mafuta pakamwa Amalawi. Komanso taona boma likugwira bwino ntchito ndi mabungwe omwe si aboma. Izi n’zofunika kusiyana ndi zija zimachitika poyamba zija kuti amabungwe kumatengetsana ndi boma,” adafotokoza Kwataine.

Iye wati pazomwe Mutharika wachita m’masikuwa angamupatse 6.5 pa 10.

Prof. Ben Kalua wa ku Chancellor College akuti Mutharika wawonetsa mawanga kuti dziko lino likupita kumtendere polichotsa kumoto komwe lidali muulamuliro wapita.

“Tikuchokera kumoto ndipo talunjika kwabwino. Mutha kuona kuti misonkho siyowawitsa ngati ija timaiona ija, zinthu sizikukwera monga zinkachitira. Tikulowera kwabwino,” adatero Kalua, koma adati si kuti zonse zili myaa.

Iye adati nkhani ya zipangizo zotsika mtengo ndi imodzi mapologalamu amene boma liyenera kuganizirapo bwino pandondomeko yothetsa umphawi poti siyopindulira Amalawi onse.

“Nkhaniyi ndi yovuta, sungati zinthu zisintha ndi kupereka zipangizo zotsika mtengo. Timati tithana ndi zipangizo zaulimi zotsika mtengo, koma apa tikumva za simenti ndi malata…Apatu tikungobweretsa mavuto enanso kwa anthu chifukwa mapeto ake zingobweretsa chisokonezo chifukwa si aliyense amene apindule ndi ndondomekoyi,” adatero Kalua.

Koma Lackson Nkhoma wa m’mudzi mwa Dzinjiriza kwa T/A Mpando m’boma la Ntcheu akuti zinthu sizikuyenda kumbali ya bizinesi chilowereni Mutharika.

“Ndimagulitsa zakumwa, koma boma latikwezera msonkho wa pachaka kuchoka pa K4 500 kufika pa K7 500. Ndiye apa pali kusintha kwabwino? Anthuwa ndi amodzi, palibe chachilendo tingachione,” adatero Nkhoma.

Naye Basitiyana Chizinga wa m’boma la Mulanje koma akukhala mumzinda wa Blantyre akugwirizana ndi Nkhoma ponena kuti moyo wa Amalawi sudayambe kusintha, mavuto ati akupitirira.

“Ine ndimagulitsa mayunitsi, ndidali ndi chiyembekezo kuti kulowa kwa a Mutharika zinthu zisintha monga zidalili ndi abale awo aja [Bingu wa Mutharika] koma ayi ndithu. Pano atikwezera msonkho wogulitsira mayunitsi pachaka kuchoka pa K4 000 kufika pa K7 000. Chabwino palibe,” adadandaula Chizinga.

Masiku 100 akhala owawitsa kwa Amalawi maka pankhani ya chitetezo pamene kuphana ndi kuba kwakhala kwachisawawa.

M’sabatayi Mutharika adati akuwadziwa amene aweyesa boma lake pankhani zachitetezo, kotero wapereka mphamvu zonse m’manja mwa nduna ya zachitetezo kuti ithane ndi aliyense amene akubweretsa chisokonezochi.

Iye adanenetsa kuti akuwadziwa amene akutekesa chitetezochi ndipo adati athana nawo.

Mutharika, polankhula atangolumbiritsidwa kukahala mtsogoleri wa dziko lino, adati anthu ogwira ntchito m’boma asade nkhawa chifukwa boma lake silithotha aliyense.

Koma izi ndi zosiyana ndi zomwe wachita pamasiku 100 chifukwa wachotsa kale mkulu wa asirikali General Odillo, wachiwiri wake Major General John Msonthi, wachiwiri kwa wamkulu wa polisi Nelson Bophani, mkulu wa bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra) Charles Nsaliwa, mongotchulapo ochepa.

Chopweteka n’chakuti ngakhale akamunawa achotsedwa ntchito, akhala akulandira malipiro kuboma omwe azichokera kumisonkho ya anthu mpaka mu 2019 malinga n’kuti awachotsa makontirakiti awo asanathe.

Related Articles

Back to top button