Chichewa

Asaka ofukula manda ndi kutengamo ziwalo

Listen to this article

 

Apolisi ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe ati akufunafuna anthu aupandu omwe adafukula manda ndi kudula ziwalo za mtembo wa mtsikana yemwe adamwalira masiku angapo apitawo m’mudzi mwa Mgona, m’dera la T/A Chitukula m’boma la Lilongwe.

Akuti awa ndi malodza: Wisiki
Akuti awa ndi malodza: Wisiki

Pofotokoza nkhaniyi, mneneri wa polisi ya Kanengo, Esther Mkwanda, adati iwo adalandira lamya yonena kuti anthu ena achipongwe, omwe zolinga zawo sizikudziwika bwino, adafukula manda ndi kudula ziwalo zingapo za mtembo wa Maria Roja, wa zaka 18, yemwe adamuika m’mandamo.

“Chimene chidachitika n’chakuti ifeyo tidangolandira foni mmamawa yonena kuti anthu apeza manda ofukulidwa kwa Mgona. Ife tidathamangirako ndipo tidapeza kuti mandawo ndi ofukulidwadi ndipo kuti thupi lili m’dzenje momwemo koma atalichotsa m’bokosi lomwe adachita chophwanya,” adafotokoza Mkwanda pouza Msangulutso.

Adapitiriza kunena kuti adapeza kuti achipongwewo adachotsa maso, lilime, milomo, chala chamkombaphala chakumanzere, komanso ziwalo zobisika.

Iye adati adachita kukhomanso bokosilo mothandizana ndi anthu a m’mudzimo ndipo adaikanso thupilo m’mandamo.

Mkwanda adati ngakhale apolisi sadagwirebe wina aliyense pankhaniyi, iwo ayesetsa kuti omwe adachita khalidwe lachilendoli agwidwe kuti akayankhe mlandu kukhothi.

Mayi Janet Wisiki, yemwe ndi mayi ake aang’ono a malemuyo, adati zomwe zidachitikazo ndi malodza enieni.

“Ine ndikuluphera kugona poganizira kuti kodi chandiona ine ndi chiyani? Kapena nditi chikunditsata ine ndi chiyani pamalodza oterewa? Kunena zoona, anthu amenewa andilaula ine. Ngakhale makolo anga zoterezi sadazionepo,” adatero Wisiki, akusisima.

Mayiyu, yemwe ali ndi zaka 40, kwawo kwenikweni ndi m’mudzi mwa Jeriko, m’dera la T/A Pemba, m’boma la Dedza. Akuti adabwera ndi kukhazikika kwa Mgonako zaka 30 zapitazo. Iye ati chomvetsa chisoni chinanso n’chakuti Maria, yemwe adali mwana wa mchemwali wake wamkulu, wamwalira ali wachisodzera.

Malinga ndi Wisiki, Maria adamwalira atadwala malungo.

Related Articles

Back to top button