Chichewa

Asemphana maganizo Pa ulimi wa ‘chamba’

Listen to this article

 

Alimi ambiri m’dziko muno ati ndi okonzeka kuyamba kulima ‘chamba’ chosazunguza ubongo mmalo mwa fodya bola boma liwaunikire zomwe ayenera kuchita, koma ena akukaikirabe ngati ulimiwu ungawatulutse muchithaphwi cha umphawi momwe akusambira.

Izi zikudza pamene Nyumba ya Malamulo yavomereza bilu yopereka mphamvu kuboma kuti livomereze ulimi wa chamba chachilendochi monga njira imodzi yopititsira patsogolo chuma cha dziko lino kulowa mmalo mwa fodya.

Phungu woima payekha wa dera la kumpoto m’boma la Ntchisi, Boniface Kadzamira, masiku apitawo adapempha Nyumba ya Malamulo kuti ipereke mphamvu kuboma kuti livomereze ulimi komanso kugwiritsa ntchito mtundu wina wa chamba wotchedwa industrial hemp.

Kadzamira adatsindika kuti mtundu wa chamba chomwe iye akufuna Amalawi azilima ndi ndi wosiyana kwambiri ndi mtundu wina wa chamba chozunguza ubongo chomwenso ena amapenga nacho akachisuta.

Chamba akunenacho si ngati ichi chomwe chimazunguza ubongo!
Chamba akunenacho si ngati ichi chomwe chimazunguza ubongo!

Iye adati chamba chomwe akunena chakhala chikulimidwa ndi kugwiritsidwa m’maiko ambirimbiri kuyambira chaka cha 1770, ndipo maiko omwe akulima mbewuyi adatukuka kwambiri kudzera m’phindu lomwe amapeza kuchokera ku malonda a mbewuyi.

“Ine ndine munthu wosangalala komanso wokhutira kwambiri ndi momwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo adaikambirana nkhaniyi. Chamba chili ndi phindu lalikulu kwabasi.

“Dziko la Malawi nalonso liyenera kuyamba kulima ndi kugwiritsa ntchito mbewuyi kuti tiyambe kupeza nawo phindu lomwe anzathu akupeza maiko enawo,” adatero Kadzamira.

Ndipo pocheza ndi Msangulutso Lachiwiri, Gunde Njobvu wa m’mudzi mwa Moloka m’dera la mfumu Kayembe ku Dowa, adati iye ndi wokonzeka kukhala m’modzi mwa alimi oyambirira kulima mbewuyi.

Njobvu adati wakhala akulima fodya wa bale zaka zambiri, koma palibe chomwe wapindula.

“Choncho, sindikuona vuto kuyesako ulimi wa chamba. Mwinanso chamba n’kukhala mdalitso wanga ndipo sindikudziwa kuti ndingachite bwanji kuti ndikhale nawo m’gulu la alimi oyambirira,” adatero mkuluyu.

Kambiza Mwale, mlimi wa zaka 60 wochokera m’dera la mfumu Kasalika m’boma lomweli, adati nkhaniyi adailandira, koma ali ndi mantha kaamba koti omwe akukolezera ulimiwu nkhaniyi sadatulukire nayo poyera kuuza alimi za kusiyana kwa mbewuyi ndi chamba chosuta.

Iye adati ali ndi nkhawa poopa kudzagwa nazo m’mavuto kaamba kosatsatira malamulo.

Mwale adati iye satengapo kaye gawo paulimi umenewu kufikira boma litawaunikira bwino kusiyana kwake kwa mbewu ya chamba choletsedwa ndi mbewu ya chamba chomwe chimagwiritsidwa ntchito popanga zinthu.

Towera Jere, wa m’mudzi wa Mzukuzuku Jere m’boma la Mzimba, naye adati sadapangebe chiganizo ngati n’kofunika kuti iye atengepo gawo pa ulimi wa chamba.

Jere adati mantha ake ali poti zikamayamba, boma ndi mabungwe amagwiritsa njira ndi mawu onyengelera pofuna kukopa anthu pamene pansi pa mtima akufuna kuwagwiritsa ntchito anthu osauka podzilemeretsa.

“Alimi m’dziko muno agwiritsidwa ntchito ngati makasu a anamadya bwino kwa nthawi yaitali kwabasi. Pomwe ulimi wa fodya unkayamba, anthu timauzidwa kuti masomphenya athu akwaniritsidwa tikalimbikira kulima, koma ndi angati omwe akusimba lokoma lero kaamba ka phindu lochokera muulimi wa fodya?” adafunsa mayiyu.

Mmodzi mwa achinyamata omwe amakhala pa Luchenza m’boma la Mulanje, Violet Banda, adati iye sakuona choletsa kulima chamba chosazunguza ubongo.

 

K

oma iye adapempha boma kuti liunikire Amalawi ngati kagulitsidwe ka mbewuyi kadzasiyane ndi momwe zilili ndi fodya wa bale ndi mitundu ina.

“Ndikunena ichi kaamba koti ndikutha kuona alimi atapatsidwanso chiyembekezo chabodza kuti miyoyo yawo idzasintha kudzera muulimi wa chamba. Ayenera kutiuza kuti kodi adzagule chamba ndani, ndipo akusiyana bwanji ndi omwe akugula bale kuokushoni lero?” adatero mtsikanayu.

Mkulu wa bungwe la Community Initiative for People Empowerment (Cipe) Trintas Manda adati alibe chiyembekezo kuti dziko la Malawi lidzatukuka kaamba kolima chamba.

Manda, yemwe bungwe lake limagwira ntchito zake ku Mzimba ndi Kasungu, adatsindika kuti pokhapokha boma la Malawi litathetsa chiyengo chomwe chikuchitika pamsika wa fodya, dziko lino lidzapitirirabe kulirira kuutsi zokolola zili zake.

Woyendetsa ntchito za bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) m’boma la Nsanje Kondwani Malunga adati iye akugwirizana ndi zoti pakhale ndondomeko yapadera yodziwitsira anthu za kusiyana kwa chamba choletsedwa ndi chomwe dziko lino likufuna lichivomereze.

“Anthu ayenera kuphunzitsidwa mokwanira kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chamba choletsedwa ndi chomwe boma likufuna kuchivomereza. Apo ayi, tidzaona mavuto ambiri kuposa phindu lomwe dziko lino likuyembekezera kupeza kudzera muulimi umenewu,” adatero Malunga.

Aphungu angapo ati akugwirizana ndi ganizo loyambitsa ulimi wa chamba m’dziko muno.

Koma ena, monga Lucius Banda, yemwe ndi phungu wa dera la kumpoto m’boma la Balaka, wati monga “munthu sangasiyanitse mowa wamasese ndi thobwa, padzakhala povuta kuti anthu asiyanitse mtundu wa chamba chosuta ndi chogwiritsa ntchito kupanga zinthu”.

“Choncho, pamene tivomereza biluyi, n’kofunikira kuti tiikenso ndondomeko zapadera zomwe zingatsogolere mabwalo a milandu pozenga mlandu omwe angafune kupezerapo mwayi lamuloli,” adatero Banda.

Ndipo mkulu wa bungwe la Drug Fight Malawi (DFM) Nelson Baziwelo Zakeyo wati sakugwirizana ndi zomwe achita aphungu a Nyumba ya Malamulo povomereza biluyi, ponena kuti izi zidzabweretsa chisokonezo m’dziko muno.

Zakeyo adati akadakonda boma likadalingaliranso bwino pa biluyi lisanavomereze lamuloli. n

Related Articles

Back to top button