Nkhani

Asing’anga akuti akonza zionetsero

Listen to this article

Asing’anga m’dziko muno akonza zionetsero zokhumudwa ndi chigamulo cha bwalo lalikulu la Mzuzu chopereka chiletso kuti asiye kugwira ntchito yawo powaganizira kuti ndiwo akukolezera mchitidwe wosowetsa ndi kupha anthu achialubino.

Mkulu wa bungwe la asing’anga mu Afrika la Traditional Medicine Council of Africa (TMCA), Steve Chester Katsonga, watsimikiza kuti zionetserozi zichitika sabata ikudzayi mumzinda wa Lilongwe.

Katsonga: Sitibwerera mmbuyo
Katsonga: Sitibwerera mmbuyo

Polankhula ndi Tamvani Lachitatu, Katsonga adati akonza zionetserozi pofuna  kukapereka madandaulo awo kwa mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti apitirize kugwira ntchito yawo mopanda mantha.

Iye wati akonza kuti boma lililonse litumize asing’anga 15 ndipo onse akakumana ku Lilongwe komwe akapereke madandaulo awo kuofesi ya Pulezidenti ndi Kabineti.

Bwalo lalikulu la milandu sabata yatha lidapereka chiletso choletsa asing’anga m’dziko muno koma lidati anthu amene adatenga chiletsocho akuyenera kulengezetsa uthenga woletsa asing’angawo kwa masiku 7 m’nyuzipepala ziwiri zodziwika ndi nyumba ziwirinso zoulutsa mawu zomwe zili ndi omvera ochuluka.

Mpaka pano uthengawo sudayambebe kulengezedwa monga bwalo lidanenera ndipo loya wa anthu amene adatenga chiletsocho, George Kadzipatike, wati ndalama ndi zomwe zawavuta.

“Anthu amene ndikuwaimirira alibe ndalama. Pakufunika pafupifupi K10 miliyoni kuti tilengezere uthengawo, koma tili ndi chikhulupiriro kuti ndalamazi zipezeka ndipo tilengeza momwe khoti lagamulira mpaka asing’angawa ataletsedwa ntchito yawo,” adatero Kadzipatike.

Komabe Katsonga wati pamene akuluakuluwa akuyang’anga ndalama, iwo agwirizana kuti achite zionetsero zamtendere pofuna kuti asaletsedwe kugwira ntchito yawo.

“Mutaonetsetsa, ndondomeko yonseyi sidayende mwadongosolo lake. Angotiganizira kuti tikukhudzidwa ndi kuphedwa kwa maalubino koma palibe umboni kuti zili choncho.

“Komanso mutha kuona kuti, pakakhala madandaulo pa zomwe mwana wachita, umayenera upeze kholo kuti likambirane ndi mwanayo. Asing’anga m’dziko muno ali ndi mabungwe, koma tikudabwa kuti ife sanatidandaulire koma adangopita kukhoti kukatenga chiletso,” adatero Katsonga.

Adapitiriza kunena kuti: “Anthu akupezeka ndi ziwalo, kodi amenewo ndi asing’anga? Komanso kodi anthuwo adawafunsa amene wawatuma? Ngati aulula munthu amene wawatuma, bwanji osamumanga munthuyo?

“Pali zambiri zoyenera kutsatidwa ngati dziko tisanabwere ndi ganizo loletsa asing’anga. Nafenso tikufuna kuthandiza dziko kuti mchitidwe wopha maalubino utheretu.”

Pokambapo nkhani za zionetsero, Katsonga adati akukhulupirira kuti Mutharika ndiye angathandize pa madandaulo awo chifukwa zikalata zomwe ali nazo kuti azigwira ntchito m’dziko muno, zidasaniyidwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino.

Adati iye: “Bungwe lathu kuti likhazikitsidwe udali mgwirizano wa dziko ndi ifeyo asing’anga. Kamuzu Banda ndiye adasayinira. Izi zikutanthauza kuti mtsogoleri wa dziko lino ndiye angatithandize.

“Ngati mtsogoleri wa dziko angavomereze asing’anga, ndiye muganiza kuti n’zolondola wina kukangotenga chiletso kuwaletsa? Nanga mabungwe ovomerezeka a asingawa azitani?”

Kuphedwa mwachisawawa kwa malubino m’dziko muno, kwachititsa kuti anthu ayambe kuperekera maganizo kuti opha anthuwa nawonso aziphedwa.

Mwa iwo ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Mulanje South, Bon Kalindo, amene wati ngati izi sizichitika, iye ayenda chibadwire kusonyeza kukwiya kwake.

Winanso ndi mtsogoleri wa chipani cha Petra Kamuzu Chibambo, yemwe Lachitatu adauza wayilesi ya Zodiak kuti lamulo loti opha anzawo nawo aziphedwa lilipobe m’dziko muno ndipo n’kofunika kuti ligwire ntchito pofuna kuteteza miyoyo ya maalubino.

Koma lipoti lomwe latulutsa bungwe loteteza maufulu a anthu padziko lapansi la Amnesty International (AI) lati silingakhale yankho kuti wopha alubino aziphedwanso.

“Monga Amnesty International, tikutsutsa kwathunthu ganizo lomapha anthu amene akhudzidwa ndi kuphedwa kapena kuzembetsedwa kwa maalubino. Izi ndi nkhanza chifukwa palibe umboni weniweni kuti chilangochi chingathetse nkhanazi,” adatero Deprose Muchena, mkulu wa bungweli kudera la kummwera kwa Afrika (Southern Africa) atabwera kudzacheza m’dziko muno masiku apitawa.

Related Articles

Back to top button