Nkhani

Atuma anthu kupha

Apolisi m’boma la Chitipa atsekera m’chitokosi bambo wina pomuganizira kuti adatuma achiwembu kupha mkazi wake wakale.

Facksoni Simbeye adatuma Filisoni Mbendera wa zaka 38 ndi bambo wina yemwe akungodziwika kuti Mshani kupha Lyness Mtawa, awiriwa atasemphana maganizo pankhani zina zam’banja.ARREST

Malinga ndi mneneri wapolisi m’chigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, izi sizidamukomere Simbeye ndipo adakonza chiwembuchi pa 6 mwezi uno.

“Maiyu adapezeka ataphedwa m’munda wa chimanga, koma atakhapidwa kwambiri m’mutu,” adatero Chapola.

Chapola adati anthu a m’mudzi mwa Fyson Nyondo, T/A Mwabulambia m’bomalo adatsatira mapazi kuchokera pomwe maiyu adaphedwera.

Mneneriyu adati apa mapaziwa adalunjika mnyumba mwa Mbendera, yemwe ataona khamu la anthuli adalikumba liwiro la mtondo wadooka.

“Komabe adamugwira pomwe adaulula kuti Simbeye ndiye adawatuma kupha maiyu. Apatu anthu sadaugwire mtima koma adamtibula mpaka kumupha,” adatero Chapola.

Ndipo mmodzi mwa anthu omwe amachokera mudzi umodzi ndi Mtawa koma adakana kutipatsa dzina lake  adatsimikizira Msangulutso kuti Simbeye ndiye adakonza chiwembuchi kaamba ka ndalama za banki m’khonde.

Bamboyo adati ngakhale Simbeye adavomera atagwidwa ndi anthu a m’mudzimo kuti ndiye adakonza upowo

“Banja lawo lidatha mwezi wa Novembala atakhala zaka zoposa zisanu, koma nkhani idagona pa K200 000 ya banki nkhonde yomwe mayiyo adatenga,” adatero bamboyu.

Related Articles

Back to top button