Kodi nditani? Gogo Natchereza Ndine mtsikana wa zaka 25 ndipo ndakhala pa chibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka zinayi. Mnyamatayu ali ndi nyumba yake ndipo akugwira ntchito yabwino pa kampani ina yopanga mafuta wophikira mu mzinda wa Lilongwe. Tidagwirizana kuti tidzakwatirana, koma mnzanga ndikamufunsa za banja amangozengereza. Kumuuza kuti apite kwathu akaonekere amangoti ndidzapitabe mpaka…

Akundidabwitsa Anatchereza, Ndili pa chibwenzi ndi mwamuna wina. Chomwe chimandidabwitsa n’choti nthawi zonse ndikamuimbira foni usiku samayankha. Ndikamufunsa amati idali kotchajitsa. Gogo ndikuona ngati mwamunayu akundiyenda njomba ali ndi mkazi wina ndipo akuopa kuti akayankha amudziwa kuti ali ndi chibwenzi. Ndithandizeni, PK, Ndirande, Blantyre. PK, Ndikadakuthandizani mokwanira ndikadziwa kuti chibwenzi chanu chidayamba bwanji. Nanga mwakhala…

Ndikufuna kuchoka Zikomo Anatchereza, Ndidabwera kutauni kudzafuna ntchito ndipo ndidasiya mkazi wanga kumudzi. Ntchito ndidaipeza koma abale amene ndimakhala m’nyumba yawo akuti ndisachoke kukafuna nyumba ya lendi ati sakufuna mkazi wangayo abwere. Kodi nditani kuti ndituluke m’nyumba yawoyo? Thandizeni. Ine F. Zikomo a F, ndinu mwamuna kotero pena sibwino kumvera zilizonse. Apapa zikuonetseratu kuti abale…

Ukuchita njomba Gogo Natcheteza, Ndine mtsikana wa zaka 25 ndipo ndakhala pa chibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka zinayi. Mnyamatayu ali ndi nyumba yake ndipo akugwira ntchito yabwino pa kampani ina yopanga mafuta wophikira mu mzinda wa Lilongwe. Tidagwirizana kuti tidzakwatirana, koma mnzanga ndikamufunsa za banja amangozengereza. Kumuuza kuti abwere kwathu azaonekere amangoti ndidzabwerabe mpaka…

Akundifunanso Anatchereza, Telemu yotsiriza ya Fomu 3 ndidapalana ubwenzi ndi mtsikana wina pasukulu yathu ku Mulanje. Koma tikuyandikira kulemba mayeso a Fomu 4, bwenzi langalo lidanditumizira uthenga palamya kundiuza kuti chibwenzi chatha chifukwa sindine ‘mwamuna’. Iye adaonjezera kuti pomwe ankandilola n’kuti ali ndi chibwenzi china. Izitu zidandiwawa kwambiri chifukwa tinkalonjezana kuti tidzakwatirana. Chondivuta n’choti atangomva…

Adandichotsa ntchito Zikomo Gogo Ndakhala ndikugwira ntchito kwa bwana wina mumzinda wa Blantyre kwa zaka 4. Masiku apitawa ndidaapempha holide ya masiku 10 ndipo bwanawo adavomera. Koma ndili kopuma, bwanawo adandiimbira foni kuti andichotsa ntchito ndipo palibe ndalama zimene angandipatse. Ndichitenji chifukwa ku ofesi yolemba anthu ntchito ngakhalenso kukhoti ya makampani koma sindinathandizidwe? Mutu waima.…

Mkazi wanga koma mkonono Agogo, Langa ndi dandaulo pa mkazi wanga wokondeka. Iyetu mwano alibe ndiponso ntchito amagwira molimbika. Abale anga amawalemekeza ndipo ana athu akuloledwa bwino. Koma chimodzi, mkazi wanga mkonono. Ndichite chiyani? YH, Zomba.   YH, Zoonadi mkonono nthawi zina umasokoneza anthu ena. Komatu ichi si chifukwa choti n’kudana nawo. Muziwalimbikitsa akazi anuwo…

Akunyengana ndi mnzanga Zikomo Anatchereza, Ndakhala pabanja zaka 7 ndipo tilinso ndi mwana wa zaka 7. Tsiku lina mwanayo adathyoka mkono ndipo adatigoneka kuchipatala sabata ziwiri ndi masiku 4. Ndili konko, ndidamva kuti mwamuna wanga akuyenda ndi mnzanga, yemwenso ndi woyandikana naye nyumba. Titatuluka adabwera kudzandiuza kuti mwamuna wanga adamufunsira koma adawakana. Nditawafunsa amuna anga…

ANATCHEREZA Akundikakamira Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana mmodzi. Vuto lake ndi limodzi: amakhalira kunyoza makolo ndi abale anga. Amati banja sakulifuna koma ndikati amange zake, amakakamira. Ndichitenji? H, Blantyre.   Zikomo H, Kodi banja lanu mudamangitsa kuti? Kodi mudangogwiriziza kwa ankhoswe? Ngati ndi choncho bwanji osakatula nkhawazo kumeneko? Ngati mudamangitsa kumpingo, mukhonzanso kupita…

Ndikufuna sukulu Zikomo Anatchereza, Ndine msungwana wa zaka 19. Sindidakwatiwepo, ngakhale sukulu ndidaisiyira Fomu 1 zaka zutatu zapitazo. Sukuluyo ndidasiya chifukwa chosowa ndalama chifukwa makolo anga adasiyana ndipo sangathe kundithandiza. Padakali pano ndikugwira ntchito m’nyumba ya munthu. Izi ndidapanga chifukwa anthu amandiuza kuti ndikwatiwe koma ine sindimafuna zimenezo. Ndimafuna kudzakwatiwa ntakonza tsogolo lowala. Chikundivuta ndi…

Za chikondi ndi chibwenzi Agogo, Kodi chibwenzi ndi chikondi ndi zosiyana bwanji? Mwina funso limeneli likhoza kuoneka ngati lopanda nzeru koma kwa ine ndi lofunika kwambiri. Funso lina ndi loti kodi ngati mwamuna amakonda kulonjeza chibwenzi kapena wachikondi kuti adzakwatirana chonsecho mkazi samamulonjeza mwamuna wake, ndiye pamenepa mwamuna angathe kupitiriza chibwenzi kapena angomusiya? LF,  …

Wokondedwa Anatchereza, Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Thandizeni. Ndili ndi mkazi yemwe ndakhala naye kwa nthawi ndithu. Iye adapezeka wodwala ndipo mthunzi wake utatsala miyezi iwiri kuti akhale ndi mwana, makolo ake adamuitanitsa. Pozindikira kuti izi zimachitika, ndidaloleza kuti apite. Ndipo sindidafowoke kumuthandiza nthawi yonseyo mpaka kuchira. Koma atachira, achibalewo adati ndichoke kumene ndikukhala…

Ndimufunsirebe? Ndine mnyamata wa mu Lilongwe ndipo ndidagwa m’chikondi ndi msungwana wina. Ndakhala ndikuponya mawu kwa iye koma iyeyo amayankha moti savomera kapena kundikana. Kodi ndipitirizebe kumufunsira? Ndithndizeni ndazunzika maganizo. B, Lilongwe. Zikomo B, Ndikuyankha molingana ndi kuti siunandiuze kuti wakhala nthawi yaitali bwanji ukuyesa mwayi wako. Zikuoneka kuti msungwanayo sanapange chiganizo chokulola kapena kukukana.…

Za Chikondi ndi chibwenzi Agogo, Kodi chibwenzi ndi chikondi ndi zosiyana bwanji? Mwina funso limeneli likhoza kuoneka ngati lopanda nzeru koma kwa ine ndi lofunika kwambiri. Funso lina ndi loti kodi ngati mwamuna amakonda kulonjeza chibwenzi kapena wachikondi kuti adzakwatirana chonsecho mkazi samamulonjeza mwamuna wake, ndiye pamenepa mwamuna angathe kupitiriza chibwenzi kapena angomusiya? LF, Area…

Zidatheka! Zikomo Anatchereza, Ndafuna ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha malangizo anu. Pano tidamanga banja ndi mtsikana wa ku Machinga uja ndipo pano tikukhala ku Phalombe bwinobwino. Ndathokoza pondithandiza maganizo. Chifundo Makisi, Phalombe Zikomo a Makisi, Nkhani yosangalatsa! Inenso ndathokoza kwambiri kuti mutatsatira malangizo anga mwalongosola zonse za banja ndipo pano zonse zatheka bwinobwino. Zonyandiritsa kwambiri. Izi…

Chikondi amatero? Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili kukoleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire m’banja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti…

Akundimana Anatchereza, Ndakhala pabanja ndi mkazi wanga kuyambira mu 2011. Poyamba zonse zimayenda koma masiku ano ndikamufuna masiku ambiri amanena kuti watopa kapena akudwala. Ndithu mpaka kumaliza mkonono wabodza. Ndikuganiza kuti ali ndi chibwenzi. Nditani? PB, Phalombe.   PB, Malembo Oyera amaneneratu kuipa kokanizana. Malangizo ambiri a mipingo ina komanso a chikhalidwe amakhala a kuipa…

Ndazunguzika Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ine ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa…

Akufuna mwana Zikomo Gogo, Banja ndi mwamuna wanga lidatha mu 2011. Ndidapeza mwamuna wina yemwe timamvana ndipo tidakayezetsa komwe adatipeza kuti tilibe kachilombo koyambitsa Edzi.Vuto ndi lakuti bwenzi langalo limakonda zogonana komanso limandiletsa kuchita za kulera. Wina adandiuza kuti bwenzi langalo lili ndi mkazi koma nditamufunsa adakana. Tsiku lina ndidaimba foni 5 koloko mbandakucha ndipo…

Anzanga sakundifunsira Ndine mtsikana wa zaka 20, vuto ndili nalo ndi loti sindikufunsiridwa ndi anyamata amsinkhu wanga koma okwatira okhaokha. Kodi agogo nditani pamenepa? Kapena ndingosiya kulola anthuwa ndi kumangokhala ‘single’? EDS, Lilongwe   Zikomo EDS, Kuti uzifunsiridwa ndi anthu amene ali kale pabanja vuto lako ndi chiyani? Funsoli udzifunse wekha ndipo yankho ulipeza. Kodi…