Sakuthandiza Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse admwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji? JS Mulanje  …

Wamkulu ndine Zikomo agogo, Ndili ndi chibwenzi koma timasiyana ndi chaka chimodzi, wamkulu ndineyo. Kodi tingathe kukwatirana? Iyeyu akufunitsitsa atandikwatira chifukwa amandikonda kwambiri ndipo inenso ndimamukoinda zedi. CM Lilongwe   Wokondeka CM, Zikomo pondilembera. Kusiyana zaka chisakhale chopinga kuti mukwatirane, bola chikondi ndi kulemekezana. Si chifukwa mkazi kukhala wamkulu pakubadwa bola chikondi. Chimene chimavuta nthawi…

Sakufuna kukayezetsa Anatchereza, Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe m’banja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati “ine zimenezo ndiye ayi”. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati…

Ndisathandize mwana wanga? Anatchereza Ine ndi mkazi wanga tidalekana titakhala pabanja zaka ziwiri. Mkaziyu ndidakukwatira titachimwitsana pasukulu ine ndili Fomu 4 pamene iye adali Fomu 2. Ndidali kuchikamwini. Koma zinthu m’banja zidasintha mosadziwika bwino. Mkazi wanga adayamba makani ndipo ndikamabwera kuchokera kuntchito ndimapeza nsima yosaphika, madzi osamba palibe ndipo izi zitachitika kwa sabata mpamene ndidakawatulira…

Sagona m’nyumba Anatchereza, Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona m’nyumba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja langa litha. Ukwati tapanga chaka chatha. Ndine A Blantyre   Zikomo A, Mwamuna wakoyo ngwachibwana zedi! Mwangokwatirana kumene ndipo ukuti sagona m’nyumba, ndiye amakagona kuti? Ukapanda kusamala naye ameneyo akugwetsa m’mavuto aakulu-ndikunenatu matenda oopsa, kuphatikizapo HIV/Edzi.…

Nditani Anatchereza? Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili ku koleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire m’banja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine…

Ndimamukonda Agogo, Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine n’kumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani? Ine Amfumu, Zingwangwa Amfumu, Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu…

Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mtsikana wa zaka 22 ndipo timakondana kwambiri koma vuto ndi loti akukana kunditsata kuchipembedzo changa. Ndiye ndithetse chibwenzichi kapena ndipitirize? RM   Zikomo RM, Choyamba ndikanakonda nditadziwa kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi chiyani, komabe poti ukufuna maganizo anga ndikuuza. Ndikhulupirira kuti cholinga cha chibwenzi…

Amandimenya Zikomo gogo, Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mwamuna wa zaka 25. Tili ndi mwana mmodzi koma vuto ndi loti ndikati ndachoka kupita kwa chemwali anga osamutsanzika amati ndinali kwa amuna ena ndipo amandimenya. Nthawi ina adandimenya mpaka adandigoneka kuchipatala kwa sabata imodzi. Nditafotokozera akuluakulu za nkhaniyi sanandithandize. Kodi chibwenzichi ndithetse…

Ndazunguzika Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa…

Sakuyankhanso foni Zikomo, Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndidapeza bwenzi langa mu 2012. Poyamba ankalimbikira kuti andikwatire chaka chomwecho koma ndidakana. Kuyambira mu 2014 mpaka 2015 nkhani yake idali yomweyo kuti andikwatire koma ndidamuuza kuti andidikire ndingomaliza kaye sukulu. Koma kuchoka nthawi yomweyo adasiya kundiimbira foni ndipo ineyo ndikati ndimuimbire sayankhanso. Sindikudziwanso ngati ubwenzi…

Amandikakamirabe Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pang’ono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi iatatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima…

  Akumandiipitsa Zikomo agogo, Ndili ndi chibwenzi ndipo makolo akudziwa ngakhale kuti ndi mwamphekesera chabe. Nthawi ina bambo ake (osati omubereka) amafuna kumugwiririra ndiye akumandiipitsa dzina kwa mayi ake, koma iwo sakutekeseka ndi izi. Ndili ndi mantha, nditani pamenepa agogo? Ine GK, Lilongwe.   GK, Wati uli ndi mantha, mantha ake otani? Sindikuonapo chifukwa choti…

Sapereka chithandizo Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse adamwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji? Pepa mtsikana,…

Sakundilipira Zikomo gogo, Ndakhala ndikugwira ntchito kukampani ya alonda ina kwa miyezi 11 popanda masiku opuma. Mwezi ulionse amatidula K500 ati ya yunifolomu. Ndidasiya ntchito mwezi wa December chifukwa amachedwa kulipira. Pakatha miyezi iwiri amatipatsa za mwezi umodzi. Ndalama za mwezi wa December mpaka lero sanandipatse. HP, Zomba. HP, Kampani imeneyo ndithu mukhoza kuitengera kukhoti…

Sakuthandiza mwana Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndidali pabanja koma litatha bambowo samatumiza chithandizo olo sopo. Ndiye nditani poti mwanayu ndimavutika naye ndekha? Pepa mtsikana, Ndi zimene ndakhala ndikulangiza atsikana nthawi zonse kuti limbikirani sukulu mudakali anthete, osati kuthamangira kukwatiwa! Tikamanena kuti si bwino kuthamangira banja timadziwa kuti nthawi…

Sitinakumanepo Anatchereza, Ndili ndi mkazi amene ndidamufunsira pafoni koma sitinaonanepo. Timangoimbirana foni basi koma amandiuza kuti amandikonda kwambiri. Ndimukhululupirire?   Zikomo, Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunanene kuti zidayamba bwanji kuti mumufunsire mkaziyo pafoni. Kodi nambala yake mudaitenga kuti? Adakupatsani ndi mbale wanu kapena mbale wamkaziyo? Mnzanu? Mnzake? Mwa njira iliyonse, nanunso mukuonetsa kuti mukhoza kukhala ndi…

Nditenge uti? Anatchereza, Munthune ndili ndi zibwenzi ziwiri. Zonsezi zidayamba chaka chimodzi panopa zatha zaka zitatu ndipo onsewa ndimawakonda chimodzimodzi inenso onsewa amandikondanso. Ndiye panopa ndapanga chiganizo chokhala ndi mmodzi. Ndipanga bwanji pamenapa? Ine Zochenana A Zochenana, Akamati ichi chakoma ichi chakoma pusi anagwa chagada kapena kuti mapanga awiri avumbwitsa mumati akutanthauzanji? Ndi zimenezitu. Mwagwiratu…

Anatchezera

Anatchereza Ndikumanyozedwa Anatchereza, Zikomo chifukwa cha malangizo amene mukumapereka. Ine ndili pabanja ndipo pano tikutha miyezi 7 ndipo timakondana kwambiri. Koma panopa ndikunyozedwa ndi mkazi yemwe mwamuna wangayu adamukwatira poyamba ineyo kulibe. Kodi pamenepa nditani? Edna, Blantyre Zikomo mayi Edna, Choyamba ndikumbutseni kuti chikondi ndi anthu awiri, wachitatu ndi kapasule. Ndikhulupirira mudayamba mwamvapo mawu amenewa.…

Ndimukhulupirirebe? Agogo, Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina wake ndipo ndakhala naye mwezi umodzi. Vuto ndi loti iye ali ndi mimba ya miyezi iwiri. Kwathu sakudziwa. Ndiye nditani, agogo? Malizani, Blantyre A Malizani, Funso lako ndi lovuta kukuyankha chifukwa sukufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti bwenzi lako wakhala nalo mwezi umodzi koma akupezeka kuti ali ndi pathupi…