Kwawo sindidziwako Agogo, Ndinapeza mwamuna kudzera patsamba lino ndipo ndikuyamika chifukwa chondithandiza. Komano vuto langa ndi loti amakana kuti ndikadziwe kwawo, koma kwathu anapitako. Kumuuza kuti abwere ndi akwawo amati amakhala kutali. Ine ndimakhala ku Blantyre ndipo mwamunayo amakhala ku Lilongwe. Kodi ndiziti ndili pabanja? Ndine NF, Balaka Zikomo NF, Ndasangalala kuti munatha kupeza…

Mayi anga amandilodza Anatche, Zikomo gogo chifukwa cha malangizo amene mumapereka kwa ife awerengi anu. Anga ndi mantha pa zomwe amandichita mayi anga. Anzawo kwambiri adandiuzapo kuti mayiwo adandiikira mankhwala m’chakudya kuti ndisiyane ndi mkazi wanga. Malinga ndi zochitika pakhomo pathu, sindikudabwa nazo izi. Ndimapezeka kuti ndikumuchitira nkhanza zosadziwika bwino mkazi wanga ngakhalenso ana athu.…

  Akunyengana ndi mnzanga Zikomo Anatchereza, Ndakhala pabanja zaka 7 ndipo tilinso ndi mwana wa zaka 7. Tsiku lina mwanayo adathyoka mkono ndipo adatigoneka kuchipatala sabata ziwiri ndi masiku 4. Ndili konko, ndidamva kuti mwamuna wanga akuyenda ndi mnzanga, yemwenso ndi woyandikana naye nyumba. Titatuluka adabwera kudzandiuza kuti mwamuna wanga adamufunsira koma adawakana. Nditawafunsa amuna…

Akumandiipitsa Zikomo agogo, Ndili ndi chibwenzi ndipo makolo akudziwa ngakhale kuti ndi mwamphekesera chabe. Nthawi ina bambo ake (osati omubereka) amafuna kumugwiririra ndiye akumandiipitsa dzina kwa mayi ake, koma iwo sakutekeseka ndi izi. Ndili ndi mantha, nditani pamenepa agogo? FK, Mchinji   FK, Wati uli ndi mantha, mantha ake otani? Sindikuonapo chifukwa choti uzikhala ndi…

Ndimamukonda Agogo, Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine n’kumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani? Ine Amfumu, Zingwangwa Amfumu, Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu…

Sabata zingapo zapitazi, takhala tikulengeza kuti patsamba lino tizikupatsirani Anatchereza ndi malangizo pamavuto amene mumakumana nawo. Mavutowa akhoza kukhala a m’banja, maphunziro, chipembedzo komanso momwe mumakhalira ndi ena. Anzanu ayamba kale kutitumizira madandaulo awo ndi awa ali mmunsimu. Anatchereza Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona m’numba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja…

Sakundikwatira Agogo, Ndithandizeni. Ndili paubwenzi ndi mwamuna yemwe adakwatirapo koma banja lake lidatha ndi mkaziyo ndipo kuli mwana mmodzi. Inenso ndili ndi mwana mmodzi. Titatha chaka tili pachibwenzi adandiuza kuti andikwatira koma mpaka lero padutsa zaka 4 palibe chimene chkuchitika. Foninso adasiya kundiimbira, komanso pan chikondi chachepa. Nditani? BH   Zikomo BH, Mwamunayo si wachilungamo…

Akundikaikira Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili Fomu 4. Ndili ndi chibwenzi chomwe ndakhala nacho miyezi 6 ndipo timakondana kwambiri ngakhale anthu amayesetsa kuti tidane poimba foni ndi kutumiza mauthenga a pafoni zam’manja (SMS) pamene sindili naye limodzi. Mnzangayu adayamba wanenapo zogonana kamodzi koma ndinakana ndiye kuyambira pamenepo amati ndiye kuti ndili ndi…

Mkazi wanga asabwere? Anatchereza, Ndili ndi zaka 25 ndipo ndili pantchito yokhalira pomwepo. Ndine wokwatira ndipo ndili mwana mmodzi. Abwana anga aakazi ndi achikulire kwambiri ndithu koma ndikati ndiwapemphe kuti ndiitanitse mkazi wanga kuti tizidzakhala limodzi amakana. Ndichite bwanji pamenepa? Chonde, thandizeni maganizo. I.J. Mzuzu Zikomo IJ, Ndathokoza chifukwa cha kundilembera kuti ndikuthandizeni maganizo pankhani…

Amandikakamiza Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili ndi bwenzi langa la zaka 19. Iyeyu amandikakamiza kugonana naye. Ine zimenezo sindimafuna koma ndimalola kupanga naye zimenezo chifukwa ndimamukonda kwambiri ndipo kukana ndimaopa kumukhumudwitsa. Ndiyeno ndipange chiyani kuti mchitidwewu uthe? Zikomo.   Wandikhumudwitsa kwambiri, mwana iwe. Pamsinkhu wakowo wayamba kale zogonana ndi anyamata? Zoona? Ndithu,…

Akuti tibwererane Anatchereza, Ndinali pambanja ndi mwamuna wa ku Nsanje ndipo ndili naye mwana mmodzi. Koma ndikati tiyeni tikaone kwanu amangoti tidzapitabe chikhalireni palibe ndi tsiku ndi limodzi lomwe abale ake anabwerapo pakhomo pathu ndiponso banja lathu ndi losagwirizira chinkhoswe. Kumudzi kwathu mwanuna wangayu amakananso kukaonako. Panopa tinasiyana chifukwa samagona m’nyumba. Mowa samwa komanso fodya…

Banja lavuta Zikomo Anatchereza, Ndine mayi wa zaka 30 ndipo ndili ndi ana atatu. Kumbuyo kunseku timakhala bwinobwino ngakhale ndimamva kuti amuna anga akuyenda ndi akazi ena. Zimandiwawa koma ndinalibe nazo ntchito. Mu 2014 anzanga omwe ndimayenda nawo onse adali ndi zibwenzi ngakhale adali pabanja ndipo ankandiuza kuti nane ndipeze chibwenzi chamseri koma ndimakana. Kenaka…

Amandimenya Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi bwenzi la zaka 21 yemwe ndili naye mwana mmodzi. Dandaulo langa ndi loti akandipeza ndikucheza ndi anyamata amandimenya ngakhale kuti sitinakwatirane. Koma iyeyo amachezanso ndi atsikana ena koma ine sindiyankhulapo kanthu. Nthawi ina adandimenya mpaka kukomoka. Nditani agogo anga? LWT, Chilobwe, Blantyre   LWT, Ndamva…

Wamboni, ine Msilamu Zikomo Anatchereza, Ndinagwa m’chikondi ndi mtsikana wa Mboni za Yehova mpaka ndinamuchimwitsa moti ndikunena pano kuli mwana wamphongo. Makolo ake atamufunsa ananditchula ineyo ndipo atandiitana ndi akwathu ndidavomera mlanduwo. Makolo a mtsikanayu adati ngati ndikufuna kuti zithe bwino ndilowe mpingo wawo kuti asakandisumire kukhoti komanso kuti ndizisamalira mwana wangayo. Ine sindikufuna kulowa…

Sitinakumanepo Anatchereza, Ine dangwa m’chikondi ndi munthu woti sindinakumanepo naye. Ndili ndi zaka 23 koma iye ndikamufunsa zaka zake samandiuza. Ati anandiona pa Facebook. Iyeyu kwawo akuti ndi ku Karonga ndipo akuti akundifuna banja. Nditani pamenepa, gogo wanga? Foni amandiimbira tsiku ndi tsiku ndipo nkhani yake imakhala yoti “ubwera liti kuno, ndakusowa”. E MP Blantyre…