Phalombe yakonzeka kuthana ndi ngozi

Pafupifupi chaka chilichonse boma la Phalombe limakumana ndi ngozi zachilengedwe, kuthana ndi mavutowa lakhala vuto kwa zaka. Mwachitsanzo, chaka chatha kuderali kudali ng’amba komanso mvula itayamba kugwa idagwa mowirikiza zomwe zidaononga katundu. Mavuto a kusefukira kwa madzi sadula phazi. Malinga ndi zomwe bomali layamba ndi kutheka kuti mavuto onga awa sakhalanso vuto kuthananawo kwake. Kuyambira…

Ndale zosadula chitukuko zikhumudwitsa aMalawi

Kudula ntchito zimene adayambitsa atsogoleri akale a dziko lino kukuchititsa kuti Amalawi azingosaukirabe chifukwa ndalama zambiri zimangolowa m’madzi ntchitozo osamalizidwa. Mkulu wa bungwe loonetsetsa kuti chilungamo chikutsatidwa la Justice Link Justine Dzonzi adanena izi Lachinayi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda komanso yemwe adzaimire chipani cha MCP atanena kuti n’kofunika kuti mtsogoleri wina amene watenga…

Woman, 80, sexually abused

She was hoping to spend three hours in her maize field and return home by 10am to help her 10-year-old granddaughter pound some maize. Return home she did, but she had neither the time nor the energy to pound the maize. She had excruciating physical and emotional pain to contend with, after two men took…

Escom isayerekeze kukweza magetsi—Banda

Kutsatira zomwe mkulu wa zachuma kukampani ya magetsi m’dziko muno ya Escom Delano Ulanje adauza wailesi ya MBC kuti bungweli likweza magetsi posakhalitsa, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Malawi Watch Billy Banda wati kampaniyi losayesere zokweza magetsi. Lachinayi Ulanje adakanira The Nation kuti sangabwerezenso mawu amene adalankhula pa MBC kotero tilankhule…

Kanduku achotsa mfumu

Kwathina ku Mwanza pamene T/A Kanduku wachotsa gulupu Thambala komanso kulamula ena awiri kuti alipe mbuzi. Bwanamkubwa wa bomalo Gift Rapozo watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati anakumana ndi mbali ziwirizi Lachitatu m’sabatayi ndipo agwirizana kuti akumanenso zofufuza zina zikatheka. Rapozo wati wayitanitsa kuti amve zokambirana zomwe zimachitika kufikira kuti mpaka Thambala agumulidwe pa mpando. “Padali…

Kuli nkhondo ku Calabar lero. Flames ikhala ikuphana ndi Nigeria masewero amenenso aunikire ntchito ya mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet. Kupambana kwa lero kuthandiza Uncle Tom kuti mwina apate ntchito yophunzitsa Flames. Aganyu lero tili pambuyo pa Flames monga tichitira ngakhale kupambana kwalero kufunika Mulungu akhale mbali yathu. Pemphero lathu tigwirana manja ndi mneneri wa…

Lundu, Kaomba apita ku mwambo wa Kulamba?

Mafumu aakulu a Achewa muno m’Malawi Paramount Chief Lundu ndi Senior Chief Kaomba, akana kunena ngati apite kumwambo wa Kulamba omwe ufike pachimake lero kulikulu la mfumu yaikulu ya Achewa m’maiko a Malawi Mozambique ndi Zambia. Mafumu awiriwa adasiya kupita kumwambowo, umene mafumu a Achewa m’maiko atatuwa amapereka ulemu kwa mfumu yawo yaikulu Kalonga Gawa…

Adzudzula JB zomanga mfumu

Mphunzitsi wa za malamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College Mwiza Nkhata wati ndi zodabwitsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda walamula apolisi kuti anjate T/A Chimombo ya ku Nsanje. Nkhata wati ngakhale pulezidenti ndi komanda wa asilikali ndi apolisi, sakuyenera kutero chifukwa kunjata munthu kumafunika kufufuzidwa kaye kunjatako kusadachitike. Banda Lachiwiri adalamula apolisi kuti…

Sabatayi yakhala yomvetsa mutu ndi nkhani ya Gabadihno Mhango. Zachitika m’sabatayi aganyu zatiwawa ndipo tikufuna bungwe la FAM komanso timu ya Big Bullets afotokoze bwino za zaka za Gaba. Sitikumvetsa zomwe lero FAM ikunena. Kuyambira chaka chatha mpaka lero zakhala zikumveka kuti matimu akunja agwa m’chikondi ndi Gaba. Aliyense amadziwa kuti zikapsa Gaba anyamuka m’dziko…

Chalaka bakha nkhuku singatole. Linda madzi apite ndiye udziti wadala. Miyambiyi ndiyo idatsanuka m’sabatayi kaamba ka jombo yomwe idathudzula Nyerere komanso kudiriza Maule mwachipongwe. Oyambirira kudandaula ndi jombo adali neba winayu ku Zomba kumene amati zikamuyendera. Iye adanyang’wa kuti adadya kale mkango wa umuna ndipo udatsala ndi waukazi koma awo adali maloto amasana chifukwa pakutha…

Amalawi apindulanji ndi kutsogolera Sadc

Akuluakulu pa zachuma komanso mafumu m’dziko muno ati mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda afunika masomphenya kuti dziko lino lipindule pamene ali wapampando wa mgwirizano wa maiko a kumwera kwa Africa wa Southern Africa Development Community (Sadc). Banda wangosankhidwa sabata yathayi pamsonkhano wa Sadc omwe umachitikira ku Lilongwe komwe atsogoleri a maiko 14 adasonkhana. Aka…

Chikho cha Carlsberg chafika pachimake

Thambo lagwa, chikho cha Carlsberg chaka chino chabwera ndi zake pamene anyamata ovala jombo atenga malo kugwedula matimu omwe amakula mtima. Chikhochi tsopano chafika m’ndime ya semifayinolo pamene dzulo Evirom imakumana ndi Red Lions pa Kamuzu mumzinda wa Blantyre. Lachitatu Big Bullets idatulutsidwa ndi Kamuzu Barracks ku Dedza 1-0 Bullets itapha Silver Strikers ku Kamuzu.…

Marvellous Deeds 3rd album launch Sunday

All is set. The much-awaited time has come for Blantyre fans as the Lilongwe-based Marvellous Deeds will be launching their third album Sanathane Nane at Robins Park this Sunday, August 25. The CD was launched in Lilongwe on July 7at the Sheaffer Marquee. “This is the time for our Blantyre fans and surrounding areas to…

Aika mwala wa maziko kawiri pachipatala

Lolemba m’sabatayi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adatsogolera anthu a m’boma la Ntcheu pomwe amayala mwala wa maziko pa chipatala cha amayi apakati. Kuyala kwa mwalaku kumadza mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Callista Mutharika atayalanso mwala wamaziko pamalopo m’mbuyomu. Mutharika adalonjeza ndalama pafupifupi K18 miliyoni zomwe amati zimangire chipatalacho pomwe Banda adalandira…

La 40 lakwana. Zochitika ku Zambia komwe Flames imakapikisana nawo mumpikisano wa Cosafa zadziwika. Kumeneko Flames idataya bomwetamweta koma ati idatenga mapointi onse kwa mahule. Asungwana a pa Zed tidatenga malo kumeneko ati mpaka kukwera nawo basi ya Flames uko akuyamikira anyamatawa ndi makochi kuti amasewera bwino. Timaganiza kuti poti akwera nawo basiyo ndiye kuti…

Apereka ambulansi ku Bangwe

Kwa kanthawi anthu makamaka amayi oyembekezera akhala akuvutika mayendedwe popita ku chipatala cha Bangwe Clinic mumzinda wa Blantyre. Anthu omwe amavutikawa ndi omwe akukhala ku Mpingwe ndi Mvula chifukwa kumaloko sikufika ma minibasi kaamba koipa kwa msewu. Pano mavutowa tsono angakhale mbiri yakale pomwe anthuwa alandira minibasi komanso ambulance yomwe idziyenda kumeneko. Zinthuzi zaperekedwa ndi…

Kati deru kadazizwitsa mlenje. Ife aganyu tadzidzimuka ndi ganizo la mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet yemwe tsopano wanena kuti sakufunanso K3.3 miliyoni akakapuntha Nigeria pa 7 September. Ife tidayamba kutolera za m’mageti kuti pofika pa 7 zikhale zitakwana koma lero kudzidzimuka akuti ndalama ayi. Ah ah ah! Zataninso wawa? Pamene Uncle Tom amabwera adagwirizana ndi…

Chalaka bakha nkhuku siyingatole. Nkhani ya Gabadinho Mhango ndi Lucky Malata ndiyo yatinenetsa mwambiwu. M’sabatayi nkhani idawawasa ndi ya anyamatawa omwenso amasewera Flames. Akamunawa akadatola chikwama pang’onong’ono ku Joni koma ena alepheretsa. Aganyu sitinadandaule koma pena sitikumvetsa njomba yomwe yaseweredwa apa. Ife sitidamvepo wosewera chigawo cha pakati atalowera kummwera kukayesa mwayi ndi Blantyre United koma…

Chisankho chanunkhira, koma ku MCP kuli chuuu!

Pamene anthu m’madera ena ayambe kulembetsa maina awo m’kalembera wa chisankho cha magawo atatu cha chaka chamawa Lolemba likudzali, sizidadziwikebe tsiku lomwe chipani chachikulu chotsutsa cha MCP chichititse msonkhano wake waukulu pokonzekera chisankho. Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa za msonkhano waukulu (konivenshoni) wa chipanichi, Joseph Njobvuyalema, wati akomiti akudikira pulezidenti wa chipanichi, John Tembo, kuti…