Nkhani

Aziputa dala

Amuna ambiri amakonda zongotenga asungwana osawadziwa n’kukagona nawo ku maresitihausi.

Zikatha bwino, amaoneka wochenjera. Komatu amaiwala kuti nthawi zina akhoza kugwa nazo m’mavuto oopsa.

Tsikulo, Katakwe adali paulendo wobwerera ku Lilongwe kuchokera ku Blantyre pomwe adamuona msungwanayo. Pagulu la anthu omwe adali pasiteji ya basiyo, mwana wamkazi adawala ngati duwa pakati pa zinyatsi.

Phazi la Katakwe lidagwa pa buleki mosaliuza. Adaima chapatsogolo nakodola msungwanayo. Msungwanayo sadanyamuke nthawi yomweyo.

Adatulutsa kagalasi m’chikwama chake cha m’manja ndikupaka kaye lipisitiki milomo yake. Kenaka adaponya magalasi akuda m’maso mwake.

Adayenda modzithyola ngati ali pa catwalk. Wamtalipo, msungwanayo adali m’diresi lothina, lalitali lomwe lidaumba bwino thupi lake.

Atalowa m’galimoto mpomwe Katakwe adaona kuti diresi la namwaliyo lidali ndi siliti yofika mpaka muntchafu.

Katakwe adazunguzika mutu. M’moyo mwake adali asadaonepo msungwana wokongola ngati namwaliyo.

Mumtima adadzitsimikizira kuti ayenera kutulutsa mawu a kukhosi asadafike ku Lilongwe.

Galimoto lidadya mtunda, uku awiriwo akucheza. Msungwanayo adati dzina lake lidali Jo.

Katakwe adapeza kuti msungwanayo amachitako kachakumwa koledzeretsa ndipo iwo ankaima m’malo osiyanasiyana n’kumakonkhako ka mowa. Mmene ankayandikira ku Lilongwe n’kuti atathodwa ndithu.

Katakwe sadatulutse mawu a kukhosi komabe n’kucheza kwawo kudapezeka kuti awiriwo adagwirizana zokagonera limodzi ku resitihausi.

Atafika mu Lilongwe adapita kumalo angapo achisangalalo ndipo mmene nthawi imafika pakati pa usiku adapita kukagonera limodzi ku resitihausi.

Adayamba kudzuka adali Katakwe. Adakasamba kubafa. Pobwera anadabwa kuona msungwana uja asadadzukebe. Adamugwedeza. Mwana wamkazi adangoti thapsa.

Adamugwedezanso msungwanayo. Ulendo uno mwa mphamvu. Msungwana adangoti lobodo!

Apa mpomwe Katakwe adazindikira kuti kena kake kavuta. Ndi mtima wozama adaona kuti msungwana adali atamwalira.

Mtima wa Katakwe udadumpha. Atani?

Kodi msungwanayo dzina lake adali ndani, nanga siadangoti Jo… Joanna? Josophine? Joyce? Jolinda?

Kupolisi akanenanji?

Related Articles

Back to top button