Religion News

Bambo wa mitala apumira pambuzi

Listen to this article

Mbuzi zadya malo. Patangotha miyezi iwiri mkulu wina ku Nkhotakota atachita chisembwere ndi mbuzi, bambo winanso wamitala ndipo ali ndi ana 9 akuti adatopera pambuzi ku Dedza masiku apitawa.

Koma bamboyu, Majaika Salimba, 46, akuti akukhulupirira kuti ‘adalodzedwa’ kuti mpaka umunthu umuchokere posiya akazi ake awiri ndi kukathera chilakolako pambuzi yomwe ati ndi mkota wa ana ake.

“Ndidachitadi, amwene, ndidangolodzedwa kuti mpaka ndigone ndi mbuziyo. Aka nkoyamba kugona ndi mbuzi ndipo sindikumvetsabe chomwe chidandichitikira. Ndikukhulupirira ndi mphamvu ya Satana,” adatero polankhula ndi Msangulutso kupolisi ya Namoni Katengeza m’bomalo.

Akuti akazi awiriwo wabereka nawo ana 9, banja lalikulu kuli ana 7 pomwe laling’ono kuli ana awiri, koma ati akukhalitsa kubanja laling’onoko.

Salimba, yemwe amayembekezeka kukaonekera kubwalo la milandu Lachiwir lapitali, akuti ‘minyamayi’ idamuchitikira pamene ankapita kudimba pa 9 April.

“Ndikupita kudimbako mpomwe ndidaona mbuziyi ikudya chimanga m’munda wa mayi wina [Dolofina Chatata]. Adaimangirira ndiye ndidaimasula kuti ndiitaye kutchire, kumenekokotu basi….[ndi komwe ndidachita nayo zadama],” adafotokoza Salimba.

Mneneri wa polisi ya Dedza, Edward Kabango, wati zomwe apolisi apeza zikusonyeza kuti mayi Chatata ndiye adapulumutsa mbuziyo kwa Salimba.

“Mayiyu adathamangira kumundako atamva mfuu wa mbuziyo, yomwe akuti imamveka ngati ikuswa koma dzidzidzi kupeza Salimba ali [kumbuyo] kwa pambuzi,” adatero Kabango.

Iye adati mkuluyu pocheuka adaphana maso ndi mayiyu. Akuti Salimba adasiya mbuziyo n’kuyamba kuthotha mayiyu moti anthu amene adamva mfuu wa mayiyu ndiwo adamulanditsa.

Koma Salimba akutsutsa zomwe mayiyu wauza apolisi ponena kuti: “Palibe munthu adandipezerera, nditamaliza ndidayisiya popanda munthu kufikapo. Zoti ndidamuthamangitsa n’zabodza.”

Mwini mbuziyo, Teziya Jekapu, wa m’mudzi mwa Nyangu kwa T/A Kaphuka, atamva kuti chiweto chakweredwa, adakanena kupolisi ya Namoni Katengeza omwe adanjata Salimba pa 10 April.

Pamene mwini mbuziyo amakadziwitsa apolisi ati n’kuti mbuziyo ikuonetsa zizindikiro zakuti yakweredwa ndi munthu. Komanso akuti imataya magazi.

Salimba adamutengera kubwalo Lolemba m’sabatayi koma mlanduwo sudamvedwe chifukwa majisitiliti sadabwere.

Titamufunsa mkuluyu momwe machezawo adalili ndi mbuziyo, iye adati: “[Mbuziyo] idali yaikulu, zidatheka bwinobwino monga zimakhalira ndi munthu.

“Nditamaliza ndidaisiya bwinobwino, ena akunena kuti imatuluka magazi koma ndi zabodza. Sidatuluke magazi….Nanenso sindidavulale, koma lidangokhala tsoka, Satana, amwene,” adatero mkuluyo.

Kabango wati mkuluyu amutsegulira mlandu wogona ndi chiweto womwe ndi wotsutsana ndi gawo 153 la malamulo a dziko la Malawi ndi zilango zake ndipo kupezeka wolakwa akaseweza zaka 14 kundende.

Related Articles

Back to top button